Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 33:1-25

33  Manase+ anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu.+  Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonyansa+ za mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli.+  Choncho iye anamanganso malo okwezeka+ amene Hezekiya bambo ake anagwetsa.+ Anamanga maguwa ansembe+ a Abaala+ n’kumanga mizati yopatulika,+ ndipo anayamba kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+  Anamanga maguwa ansembe+ m’nyumba ya Yehova, imene ponena za iyo Yehova anati: “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka kalekale.”+  Iye anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo+ m’mabwalo+ awiri a nyumba ya Yehova.+  Manase anatentha* ana ake aamuna pamoto+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,+ ankachita zanyanga,+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.+  Komanso iye anaika m’nyumba ya Mulungu woona+ chifaniziro+ chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo, Mulungu anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha+ pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa+ mpaka kalekale.+  Sindidzachotsanso phazi la Isiraeli panthaka imene ndinapatsa+ makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ ndiponso mogwirizana ndi chilamulo+ chonse, malangizo+ onse, ndi zigamulo+ zonse zimene ndinawapatsa kudzera m’manja mwa Mose.”+  Koma Manase+ anapitiriza kunyengerera Yuda+ ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.+ 10  Yehova anapitiriza kulankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanamvere.+ 11  Pomalizira pake Yehova anawabweretsera+ akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri.+ Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje.+ Atatero anam’manga+ ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo. 12  Iye atasautsika mumtima mwake chifukwa cha zimenezi,+ anakhazikitsa pansi mtima wa Yehova Mulungu wake+ ndipo anadzichepetsa+ kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13  Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+ 14  Pambuyo pa zimenezi, Manase anamanga mpanda kunja+ kwa Mzinda wa Davide,+ kumadzulo kwa Gihoni,+ kuyambira m’chigwa kukafika ku Chipata cha Nsomba.+ Mpandawo unazungulira n’kukafika ku Ofeli+ ndipo unali wautali kwambiri kuchokera pansi kufika pamwamba. Kuwonjezera apo, iye anaika akuluakulu a asilikali m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ 15  Anachotsa milungu yachilendo,+ fano+ limene linali m’nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse ansembe+ amene anamanga m’phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu. Kenako, zinthu zimenezi anakazitaya kunja kwa mzinda. 16  Komanso Manase anakonza guwa lansembe la Yehova+ n’kuyamba kuperekerapo nsembe zachiyanjano+ ndi zoyamikira,+ ndipo anauza Ayuda kuti azitumikira Yehova Mulungu wa Isiraeli.+ 17  Komabe anthu anali kuperekabe nsembe m’malo okwezeka,+ kungoti anali kuzipereka kwa Yehova Mulungu wawo. 18  Nkhani zina zokhudza Manase, pemphero+ limene anapereka kwa Mulungu wake, ndi mawu a anthu amasomphenya+ amene anali kulankhula naye m’dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli, zatchulidwa m’nkhani za mafumu a Isiraeli.+ 19  Nkhani zokhudza pemphero lake,+ zokhudza mmene Mulungu anamvera kupembedza kwake,+ machimo ake onse,+ ndi kusakhulupirika kwake+ zinalembedwa m’mawu a amasomphenya ake. M’mawu amenewa munalembedwanso nkhani zokhudza malo amene iye anamangako malo okwezeka+ n’kuikapo mizati yopatulika+ ndi zifaniziro zogoba+ asanadzichepetse.+ 20  Pomalizira pake Manase anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda+ panyumba yake. Kenako Amoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. 21  Amoni+ anali ndi zaka 22 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ 22  Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ monga anachitira Manase bambo ake.+ Amoni anali kupereka nsembe+ kwa zifaniziro zonse zogoba+ zimene bambo ake+ anapanga, ndipo anapitiriza kuzitumikira.+ 23  Iye sanadzichepetse+ pamaso pa Yehova monga anadzichepetsera Manase bambo ake,+ pakuti Amoni ndiye amene anawonjezera kupalamula.+ 24  Pomalizira pake, atumiki ake anam’chitira chiwembu+ n’kumupha m’nyumba mwake momwe.+ 25  Koma anthu a m’dzikolo anapha+ anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni.+ Kenako anthu+ a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anadutsitsa.”