Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 30:1-27

30  Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembanso makalata ku Efuraimu+ ndi ku Manase,+ kuti abwere kunyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu kudzachita pasika+ kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.  Koma mfumuyo, akalonga ake+ ndi mpingo wonse+ ku Yerusalemu anagwirizana zoti achite pasikayo m’mwezi wachiwiri.+  Iwo sanathe kuchita pasikayo m’mwezi woyamba+ popeza ansembe amene anadziyeretsa sanali okwanira+ komanso anthuwo sanasonkhane ku Yerusalemu.  Nkhaniyi inakomera mfumu ndi mpingo wonsewo.+  Choncho anagwirizana kuti alengeze+ zimenezi mu Isiraeli yense kuyambira ku Beere-seba+ mpaka ku Dani,+ ndipo auze anthuwo kuti abwere ku Yerusalemu adzachite pasika kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa m’mbuyomo, iwo sanali kusonkhana onse pamodzi+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+  Ndiyeno asilikali othamanga+ amene anatenga makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akalonga ake,+ anapita mu Isiraeli ndi Yuda yense mogwirizana ndi lamulo la mfumu, lakuti: “Inu ana a Isiraeli, bwererani+ kwa Yehova Mulungu+ wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli, kuti iye abwerere kwa anthu anu otsala+ amene anapulumuka m’manja mwa mafumu a Asuri.+  Musakhale ngati makolo anu+ ndi abale anu amene anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo, mwakuti anawachititsa kukhala chinthu chodabwitsa+ monga mmene mukuoneramu.  Tsopano musaumitse khosi lanu+ ngati mmene anachitira makolo anu. Gonjerani Yehova,+ pitani kunyumba yake yopatulika+ imene waiyeretsa+ mpaka kalekale. Tumikirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake umene wakuyakirani+ ukuchokereni.  Mukabwerera+ kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo+ ndi anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina. Chotero iwo adzaloledwa kubwerera kudziko lino+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo+ ndiponso wachifundo,+ ndipo sadzayang’ana kumbali mukabwerera kwa iye.”+ 10  Asilikali othamangawo+ anapitiriza ulendo wawo ndipo anapita kumzinda ndi mzinda m’dziko lonse la Efuraimu+ ndi Manase mpaka ku Zebuloni. Koma anthuwo ankangokhalira kuwatonza ndi kuwaseka.+ 11  Anthu+ ochokera ku Aseri, ku Manase, ndi ku Zebuloni okha ndi amene anadzichepetsa+ n’kubwera ku Yerusalemu. 12  Dzanja la Mulungu woona linakhalanso ndi anthu a ku Yuda, moti anawapatsa mtima umodzi+ kuti amvere lamulo+ la mfumu ndi la akalonga pa nkhani zokhudza kutumikira Yehova.+ 13  Tsopano chikhamu cha anthu chinasonkhana ku Yerusalemu+ kuti achite chikondwerero+ cha mkate wopanda chofufumitsa m’mwezi wachiwiri,+ ndipo unali mpingo waukulu kwambiri. 14  Kenako iwo ananyamuka n’kuchotsa maguwa ansembe+ amene anali mu Yerusalemu. Anachotsanso maguwa ansembe onse ofukizirapo+ n’kukawataya kuchigwa cha Kidironi.+ 15  Atatero anapha nyama ya pasika+ pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anali atachititsidwa manyazi moti anadziyeretsa+ n’kubweretsa nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova. 16  Iwo anaimirira+ m’malo mwawo mogwirizana ndi zimene analamulidwa, malinga ndi lamulo la Mose munthu wa Mulungu woona. Ansembe+ anali kuwaza paguwa lansembe magazi amene anali kulandira kwa Alevi. 17  Koma panali anthu ambiri mumpingowo amene sanadziyeretse. Choncho Alevi+ ndi amene anali kugwira ntchito yophera nyama za pasika+ anthu onse amene sanali oyera, kuti awayeretse kwa Yehova. 18  Panali anthu ambiri ochokera ku Efuraimu,+ ku Manase,+ ku Isakara ndi ku Zebuloni+ amene sanadziyeretse+ ndipo anadya pasikayo mosatsatira zimene zinalembedwa.+ Koma Hezekiya anawapempherera+ kuti: “Yehova wabwino+ asakwiyire 19  aliyense amene wakonza mtima wake+ kuti afunefune Mulungu woona Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti sanadziyeretse mogwirizana ndi zinthu zopatulika.”+ 20  Choncho Yehova anamvera Hezekiya ndipo anakhululukira anthuwo.+ 21  Chotero ana a Isiraeli amene anali ku Yerusalemu anachita chikondwerero+ cha mkate wopanda chofufumitsa masiku 7 mosangalala kwambiri.+ Alevi+ ndi ansembe+ anali kutamanda Yehova tsiku ndi tsiku ndi zipangizo zoimbira za mawu okwera zotamandira Yehova.+ 22  Kuwonjezera apo, Hezekiya analankhula mokoma mtima+ kwa Alevi onse amene anali kutumikira Yehova mwanzeru.+ Anthuwo anachita phwando loikidwiratu kwa masiku 7.+ Anali kupereka nsembe zachiyanjano+ ndi kulapa+ kwa Yehova Mulungu wa makolo awo. 23  Ndiyeno mpingo wonsewo unagwirizana+ kuti uchitenso phwandolo masiku ena 7.+ Choncho analichitanso masiku 7 mosangalala. 24  Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka+ ku mpingowo ng’ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 7,000. Akalonganso+ anapereka ku mpingowo ng’ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 10,000, ndipo ansembe+ ambiri anali kudziyeretsa. 25  Mpingo wonse wa Ayuda,+ ansembe, Alevi+ ndiponso mpingo wonse wa anthu amene anachokera ku Isiraeli,+ alendo+ amene anachokera m’dziko la Isiraeli+ ndi amene anali kukhala m’dziko la Yuda, anapitiriza kusangalala.+ 26  Chotero munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira m’masiku a Solomo+ mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanachitike chikondwerero ngati chimenechi ku Yerusalemu.+ 27  Pomalizira pake ansembe achilevi anaimirira n’kudalitsa+ anthuwo, ndipo mawu awo anamvedwa moti pemphero lawo linafika kumwamba, kumalo oyera okhala Mulungu.+

Mawu a M'munsi