Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

2 Mbiri 3:1-17

3  Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu paphiri la Moriya,+ pamalo amene Yehova anaonekera kwa Davide bambo ake.+ Anamanga nyumbayo pamalo amene Davide anali atakonza. Amenewa anali malo opunthira mbewu a Orinani+ Myebusi.  Iye anayamba kumanga nyumbayi m’mwezi wachiwiri pa tsiku lachiwiri, m’chaka chachinayi cha ufumu wake.+  Tsopano awa ndiwo maziko amene Solomo anayala omangira nyumba ya Mulungu woona. M’litali mwa mazikowo, malinga ndi muyezo wakale, munali mikono* 60 ndipo m’lifupi mwake munali mikono 20.+  Kutsata m’litali mwa nyumbayo, kumaso kwake kunali khonde+ la mikono 20 m’litali, mofanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Kuchoka pansi kufika pamwamba, khondelo linali lalitali mikono 120, ndipo mkati mwake anakutamo ndi golide woyenga bwino.  Nyumba yaikuluyo anaikuta+ ndi matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza, kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi zithunzi za mitengo yakanjedza+ zojambula mochita kugoba ndiponso matcheni.+  Kuwonjezera apo, anakongoletsa nyumbayo+ poikuta ndi miyala yamtengo wapatali. Golide+ wakeyo anali wochokera kudziko la golide.  Ndipo mitanda yake ya denga,* makomo, makoma,* ndi zitseko za nyumbayo anazikuta ndi golide.+ Pamakoma ake anajambulapo akerubi mochita kugoba.+  Kenako anapanga chipinda cha Malo Oyera Koposa.+ M’litali mwake chinali mikono 20+ mofanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Choncho m’lifupi mwake, chipindacho chinali mikono 20, ndipo anachikuta ndi golide wabwino wokwanira matalente* 600.  Misomali yake inali yolemera+ masekeli* 50 agolide, ndipo zipinda zake zapadenga anazikuta ndi golide. 10  M’chipinda cha Malo Oyera Koposa anapangamo zifaniziro za akerubi+ ziwiri n’kuzikuta ndi golide.+ 11  Mapiko a akerubiwo+ kutalika kwake anali mikono 20. Phiko limodzi linali lalitali mikono isanu kufika kukhoma la chipindacho. Phiko linalo linali lalitali mikono isanu kufika paphiko la kerubi mnzake.+ 12  Phiko limodzi la kerubi wina linali lalitali mikono isanu kufika kukhoma la chipindacho, ndipo phiko linalo, lalitali mikono isanu, linali kukhudzana ndi phiko la kerubi mnzake.+ 13  Mapiko a akerubiwo anali otambasuka mikono 20. Akerubiwo anali choimirira ndipo nkhope zawo zinali zitayang’ana mkati. 14  Anapanganso nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu,+ ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira ndi nsalu yofiira komanso yabwino kwambiri. Kenako nsaluyo anaikongoletsa ndi akerubi.+ 15  Ndiyeno kumaso kwa nyumbayo anamangako zipilala ziwiri+ zazitali mikono 35. Mutu+ wa chipilala chilichonse umene unali pamwamba pake unali wautali mikono isanu. 16  Atatero anapanganso matcheni+ okhala ngati ovala m’khosi ndi kuwaika kumutu kwa zipilala zija, ndipo anapanga makangaza*+ 100 n’kuwaika kumatcheniwo. 17  Zipilalazo anaziika kumaso kwa kachisi, china mbali ya kudzanja lamanja china mbali ya kumanzere. Chipilala cha mbali ya kudzanja lamanja anachitcha dzina lakuti Yakini, ndipo cha mbali ya kumanzere anachitcha dzina lakuti Boazi.+

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Kapena kuti “ya tsindwi.”
Ena amati, “chipupa” kapena “chikupa.”
Onani Zakumapeto 12.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
“Makangaza,” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.