Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 19:1-11

19  Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera mu mtendere+ kunyumba kwake ku Yerusalemu.  Tsopano Yehu+ mwana wa Haneni+ wamasomphenya,+ anapita kukaonekera kwa Mfumu Yehosafati ndipo anaifunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa+ kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana+ ndi Yehova?+ Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.+  Komabe, pali zinthu zabwino+ zimene zapezeka mwa inu, chifukwa mwachotsa mizati yopatulika m’dzikoli,+ ndipo mwakonza mtima wanu kuti mufunefune Mulungu woona.”+  Yehosafati anapitiriza kukhala ku Yerusalemu. Iye anayambanso kupita pakati pa anthu, kuyambira ku Beere-seba+ mpaka kudera lamapiri la Efuraimu,+ kuti awabwezere kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.+  Anaika oweruza m’dziko lonselo, mumzinda ndi mzinda, m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+  Ndiyeno anauza oweruzawo kuti: “Samalani zochita zanu+ chifukwa simukuweruzira munthu koma mukuweruzira Yehova,+ ndipo iye ali nanu pa ntchito yoweruzayi.+  Tsopano mantha+ a Yehova akugwireni.+ Samalani mmene mukuchitira+ chifukwa Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo+ kapena watsankho,+ ndipo salandira chiphuphu.”+  Ku Yerusalemu nakonso Yehosafati anaikako Alevi ena,+ ansembe,+ ndi ena mwa atsogoleri a nyumba za makolo+ a Isiraeli, kuti azionetsetsa kuti anthu akutsatira chilamulo+ cha Yehova ndi kuti aziweruza milandu+ ya anthu a ku Yerusalemu.  Kuwonjezera apo, anawalamula kuti: “Muzichita zimenezi moopa+ Yehova ndi mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu. 10  Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene akukhala m’mizinda yawo, wokhudza kukhetsa magazi,+ chilamulo,+ ndi zigamulo,+ muziwachenjeza kuti asalakwire Yehova kuopera kuti mkwiyo wa Mulungu+ ungakuyakireni inuyo ndi abale anu. Muzichita zimenezi n’cholinga choti musapalamule mlandu. 11  Ndakupatsani wansembe wamkulu Amariya kuti azisamalira nkhani iliyonse yokhudza Yehova.+ Zebadiya mwana wa Isimaeli mtsogoleri wa nyumba ya Yuda aziyang’anira nkhani iliyonse yokhudza mfumu. Ndakupatsaninso Alevi kuti akhale oyang’anira anu. Khalani olimba mtima+ ndipo gwirani ntchitoyi. Yehova+ adalitse zabwino zimene muzichita.”+

Mawu a M'munsi