Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

2 Mbiri 18:1-34

18  Yehosafati anakhala ndi chuma chambiri ndi ulemerero waukulu,+ koma anachita mgwirizano wa ukwati+ ndi Ahabu.+  Chotero patapita zaka, iye anapita kwa Ahabu ku Samariya.+ Ahabu anapha nkhosa ndi ng’ombe zambiri n’kuzipereka nsembe+ m’malo mwa Yehosafati ndi anthu amene anali naye. Kenako Ahabu anayamba kunyengerera+ Yehosafati kuti apite kukamenyana ndi mzinda wa Ramoti-giliyadi.+  Ahabu mfumu ya Isiraeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti: “Kodi upita nane ku Ramoti-giliyadi?”+ Yehosafati anamuyankha kuti: “Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu ako ndi amodzi, ndipo ali nawe limodzi pankhondoyi.”+  Komabe Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, umve+ kaye mawu a Yehova.”  Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri+ pamodzi. Analipo amuna 400, ndipo inawafunsa kuti: “Kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?”+ Iwo anayankha kuti: “Pitani, ndipo Mulungu woona akapereka mzindawo m’manja mwanu mfumu.”  Koma Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene watsala?+ Ngati alipo, tiyeni tifunse kudzera mwa ameneyo.”+  Poyankha, mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati+ kuti: “Pali munthu mmodzi+ amene tingathe kufunsira kwa Yehova kudzera mwa iye, koma ineyo ndimadana naye+ kwambiri, chifukwa masiku ake onse salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Munthuyo dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.”+ Koma Yehosafati anati: “Musalankhule choncho mfumu.”+  Chotero mfumu ya Isiraeli inaitana nduna ya panyumba ya mfumu,+ n’kuiuza kuti: “Kaitane Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye msangamsanga.”+  Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anali atakhala pabwalo* la pachipata cha Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu, atavala zovala zachifumu.+ Aneneri onse anali pamaso pawo ndipo anali kulosera.+ 10  Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga+ zachitsulo n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Ndi nyanga izi mudzakankha Asiriya mpaka kuwatha.’”+ 11  Aneneri ena onse analinso kulosera zofanana ndi zomwezo, ndipo anali kunena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana.+ Yehova akaperekadi mzindawo m’manja mwanu mfumu.”+ 12  Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Tamvera, mawu amene aneneri onse alankhula kwa mfumu ndi abwino. Nawenso mawu ako akakhale ngati mawu awo,+ ndipo ukalankhule zabwino.”+ 13  Koma Mikaya anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ zimene Mulungu wanga anene n’zimene ndikalankhule.”+ 14  Kenako anafika kwa mfumu, ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana. Iwo akaperekedwa m’manja mwanu.”+ 15  Ndiyeno mfumuyo inamuuza kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati+ kuti uzilankhula kwa ine zoona zokhazokha m’dzina la Yehova?”+ 16  Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika m’mapiri ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe atsogoleri.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake mu mtendere.’”+ 17  Mfumu ya Isiraeli itamva zimenezi inauza Yehosafati kuti: “Pajatu ndinakuuza kuti, ‘Adzalosera zoipa zokhudza ine, osati zabwino.’”+ 18  Mikaya anapitiriza kunena kuti: “Choncho imvani mawu a Yehova:+ Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu,+ makamu onse+ akumwamba ataimirira kudzanja lake lamanja ndi kumanzere kwake.+ 19  Kenako Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu mfumu ya Isiraeli, kuti apite ku Ramoti-giliyadi n’kukafa?’ Choncho panali kukambirana. Uyu anali kunena zakutizakuti, uyunso n’kumanena zakutizakuti.+ 20  Pomalizira pake, mzimu+ wina unabwera kudzaima pamaso pa Yehova n’kunena kuti, ‘Ine ndikam’pusitsa.’ Ndipo Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukam’pusitsa motani?’+ 21  Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukam’pusitsadi ndipo zikakuyendera bwino.+ Pita kachite momwemo.’+ 22  Choncho Yehova waika mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anuwa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+ 23  Tsopano Zedekiya+ mwana wa Kenaana+ anayandikira Mikaya+ ndipo anam’menya mbama.+ Kenako anati: “Kodi mzimu wa Yehova wachoka bwanji kwa ine n’kukalankhula ndi iwe?”+ 24  Pamenepo Mikaya anati: “Udzadziwa zimenezo tsiku+ limene udzalowe m’chipinda chamkati kukabisala.”+ 25  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Tengani Mikaya mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu.+ 26  Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti: “Kam’tsekereni munthu uyu.+ Muzim’patsa chakudya chochepa+ ndi madzinso ochepa, kufikira ine nditabwerera mu mtendere.”’”+ 27  Pamenepo Mikaya ananena kuti: “Mukakabwereradi mu mtendere, ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Anatinso: “Imvani anthu nonsenu.”+ 28  Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 29  Tsopano mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha+ kuti ndisadziwike, ndipo ndimenya nawo nkhondo. Koma iweyo uvale zovala zako zachifumu.”+ Chotero mfumu ya Isiraeli inadzisintha, kenako iwo anayamba kumenya nawo nkhondo.+ 30  Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu ake oyang’anira asilikali okwera magaleta, kuti: “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamng’ono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.”+ 31  Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Iyi ndiyo mfumu ya Isiraeli.”+ Choncho anatembenuka kuti amenyane naye, koma Yehosafati anayamba kukuwa popempha thandizo,+ ndipo Yehova anamuthandiza.+ Nthawi yomweyo Mulungu anawachititsa kuchoka kwa iye.+ 32  Akuluakulu oyang’anira asilikali okwera magaleta aja atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, nthawi yomweyo anasiya kumuthamangitsa ndipo anabwerera.+ 33  Ndiyeno munthu wina anakoka uta n’kuponya muvi wake chiponyeponye, koma analasa+ mfumu ya Isiraeli pampata umene unali pakati pa chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo, ndi zovala zake zina zodzitetezera. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti:+ “Tembenuza galetali ndipo unditulutse m’bwalo lankhondoli, chifukwa ndavulala kwambiri.”+ 34  Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo, ndipo mfumu ya Isiraeliyo anaiimiritsa m’galeta moyang’anizana ndi Asiriya mpaka madzulo. Potsirizira pake mfumuyo inafa pamene dzuwa linali kulowa.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “popunthira mbewu.”