Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 14:1-15

14  Pomalizira pake, Abiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Asa+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. M’masiku ake, m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse+ kwa zaka 10.  Asa anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.  Choncho iye anachotsa maguwa ansembe achilendo,+ anagwetsa malo okwezeka,+ anaphwanya zipilala zopatulika+ ndi kudula mizati yopatulika.+  Kuwonjezera apo, anauza Ayuda kuti afunefune+ Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira chilamulo.+  Iye anachotsa malo okwezeka ndi maguwa ofukizirapo zonunkhira+ m’mizinda yonse ya Yuda, ndipo ufumuwo unapitiriza kukhala wopanda chosokoneza chilichonse+ mu ulamuliro wake.  Kenako anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri m’dziko la Yuda,+ chifukwa m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse, komanso palibe anachita naye nkhondo pa zaka zimenezi, chifukwa Yehova anam’patsa mpumulo.+  Choncho iye anauza Ayuda kuti: “Tiyeni timange mizindayi ndi mipanda+ yoizungulira. Timangenso nsanja+ ndipo tipange makomo a zitseko ziwiriziwiri ndi mipiringidzo.+ Malo m’dzikoli akadalipo chifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu.+ Tam’funafuna ndipo watipatsa mpumulo pakati pa adani athu onse otizungulira.”+ Chotero iwo anamangadi ndipo zinthu zinawayendera bwino.+  Asa anakhala ndi gulu lankhondo lonyamula zishango zazikulu+ ndi mikondo ing’onoing’ono,+ la asilikali 300,000 a fuko la Yuda.+ Analinso ndi asilikali onyamula zishango zazing’ono+ ndi odziwa kupinda uta okwanira 280,000+ a fuko la Benjamini. Onsewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima.  Pambuyo pake Zera Mwitiyopiya+ anabwera kudzamenyana nawo ali ndi gulu lankhondo la asilikali 1,000,000+ ndi magaleta 300, ndipo anafika ku Maresha.+ 10  Asa anapita kukamenyana naye ndipo iwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo m’chigwa cha Sefata ku Maresha. 11  Tsopano Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake,+ kuti: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera m’dzina lanu+ kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+ 12  Atatero, Yehova anagonjetsa+ Aitiyopiyawo pamaso pa Asa ndi Ayuda, ndipo Aitiyopiyawo anayamba kuthawa. 13  Asa ndi anthu amene anali naye anawathamangitsa mpaka kukafika ku Gerari,+ ndipo Aitiyopiyawo anapitiriza kuphedwa mpaka palibe amene anatsala ndi moyo, popeza Yehova+ ndi gulu lake+ anawagonjetseratu. Pambuyo pake, anthuwo anatenga zofunkha zochuluka zedi.+ 14  Kuwonjezera apo, anawononga mizinda yonse yozungulira Gerari chifukwa mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira anthu a m’mizindayo. Iwo anafunkha mizinda yonseyo, chifukwa munali zambiri zoti afunkhe.+ 15  Anawononganso mahema+ a anthu okhala ndi ziweto n’kutengamo+ ziweto zambiri ndi ngamila.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu.

Mawu a M'munsi