Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mbiri 13:1-22

13  M’chaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu, Abiya anayamba kulamulira Yuda.+  Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Mikaya+ mwana wa Uriyeli wa ku Gibeya.+ Kenako pakati pa Abiya ndi Yerobowamu panachitika nkhondo.+  Choncho Abiya anapita kukamenya nkhondoyo ndi gulu la amuna amphamvu ankhondo+ osankhidwa mwapadera okwanira 400,000. Yerobowamu nayenso anapita kukamenyana ndi Abiya ndipo anapita ndi asilikali 800,000. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima osankhidwa mwapadera, ndipo anakafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+  Tsopano Abiya anaimirira paphiri la Zemaraimu limene lili m’dera lamapiri la Efuraimu,+ n’kunena kuti: “Tamvera, iwe Yerobowamu ndi Aisiraeli onsewo.  Kodi simukudziwa kuti Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka ufumu kwa Davide+ kuti azilamulira Isiraeli mpaka kalekale?+ Simukudziwa kodi kuti anaupereka kwa iye ndi ana ake+ pochita naye pangano losatha?*+  Koma Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anali mtumiki+ wa Solomo mwana wa Davide, anapanduka+ n’kuukira mbuye wake.+  Ndipo anthu osowa chochita+ ndi opanda pake+ anasonkhana kumbali yake. Pamapeto pake iwo anakhala amphamvu kuposa Rehobowamu+ mwana wa Solomo pamene Rehobowamuyo anali wamng’ono komanso wamantha,+ ndipo sanathe kulimbana nawo.  “Tsopano anthu inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Yehova umene uli m’manja mwa ana a Davide,+ popeza ndinu khamu lalikulu+ ndipo muli ndi ana a ng’ombe agolide amene Yerobowamu anakupangirani kuti akhale milungu yanu.+  Kodi simunathamangitse ansembe a Yehova,+ omwe ndi ana a Aroni, komanso Alevi? Ndipo kodi simukudziikira ansembe ngati mmene amachitira anthu a mayiko ena?+ Aliyense amene wabwera n’kudziika pa udindo waunsembe mwa kupereka ng’ombe yaing’ono yamphongo ndi nkhosa zamphongo 7, amakhala wansembe wa mafano omwe si milungu.+ 10  Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu+ ndipo sitinamusiye. Ansembe, omwe ndi ana a Aroni, akutumikira Yehova, ndiponso Alevi akugwira ntchito yawo.+ 11  Iwo akufukiza nsembe zopsereza kwa Yehova m’mawa uliwonse ndi madzulo alionse.+ Akufukizanso mafuta onunkhira+ ndipo mikate yosanjikiza ili patebulo la golide woyenga bwino.+ Tilinso ndi choikapo nyale chagolide+ ndi nyale zake zimene amayatsa madzulo alionse.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu+ kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.+ 12  Taonani, ife patsogolo pathu pali Mulungu woona+ ndi ansembe ake,+ ndi malipenga+ otiitanira ku nkhondo yomenyana nanu. Inu ana a Isiraeli, musamenyane ndi Yehova Mulungu wa makolo anu,+ chifukwa simupambana.”+ 13  Pamenepo Yerobowamu anatumiza asilikali kuti akawabisalire kumbuyo, choncho Yerobowamuyo ndi asilikali ake anakhala kutsogolo kwa Ayuda ndipo obisalawo anali kumbuyo kwa Ayudawo.+ 14  Ayudawo atatembenuka, anangoona kuti adani awo ali kumbuyo ndi kutsogolo kwawo.+ Choncho anayamba kufuulira Yehova+ pamene ansembe anali kuliza malipenga mokweza. 15  Kenako amuna a Yuda anayamba kufuula mfuu ya nkhondo.+ Atafuula mfuu ya nkhondoyo, Mulungu woona anagonjetsa+ Yerobowamu ndi Aisiraeli onse pamaso pa Abiya+ ndi Ayuda. 16  Kenako ana a Isiraeli anayamba kuthawa pamaso pa Ayuda, koma Mulungu anawapereka m’manja mwa Ayudawo.+ 17  Abiya ndi anthu ake anapha Aisiraeli ambirimbiri. Aisiraeliwo anapitirira kuphedwa mpaka ophedwawo anakwana amuna 500,000 osankhidwa mwapadera. 18  Choncho ana a Isiraeli anachititsidwa manyazi pa nthawi imeneyo, koma ana a Yuda anapambana chifukwa anadalira+ Yehova Mulungu wa makolo awo. 19  Abiya anapitiriza kuthamangitsa Yerobowamu ndipo anamulanda mizinda yake. Analanda Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, Yesana ndi midzi yake yozungulira, ndiponso Efuraini ndi midzi yake yozungulira.+ 20  Yerobowamu sanakhalenso ndi mphamvu+ m’masiku a Abiya, ndipo Yehova anamukantha+ moti anafa. 21  Abiya anapitiriza kulimbitsa ufumu wake.+ M’kupita kwa nthawi, anakwatira akazi 14+ ndipo anabereka ana aamuna 22+ ndi aakazi 16. 22  Nkhani zina zokhudza Abiya, njira zake ndi mawu ake, zinalembedwa m’buku la ndemanga la mneneri Ido.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “pangano la mchere.”