Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mafumu 9:1-37

9  Mneneri Elisa anaitana mmodzi wa ana+ a aneneri n’kumuuza kuti: “Konzeka,*+ nyamula botolo ladothi+ la mafutali m’manja mwako, upite ku Ramoti-giliyadi.+  Ukakalowa mumzindawo, ukafufuze Yehu+ mwana wa Yehosafati mwana wa Nimusi. Ukakam’peza, ukamutenge pakati pa abale ake ndipo ukalowe naye m’chipinda chamkati.+  Ndiyeno ukatenge botolo ladothi la mafutali n’kumuthira pamutu,+ ndipo ukanene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukudzoza+ iwe kukhala mfumu+ ya Isiraeli.”’ Ukakatero, ukatsegule chitseko ndi kuthawa, usakachedwe.”  Ndiyeno mtumiki wa mneneriyo ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.  Atalowa mumzindawo, anapeza akuluakulu a asilikali atakhalakhala. Kenako iye anati: “Ndili nanu mawu inu+ mkulu wa asilikali.” Ndiyeno Yehu anati: “Ndani kwenikweni pakati pa tonsefe?” Iye anayankha kuti: “Inuyo mkulu wa asilikali.”  Choncho Yehu ananyamuka n’kulowa m’nyumba. Mmenemo mtumiki wa mneneri uja anatenga mafuta aja n’kumuthira pamutu. Kenako anamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikukudzoza iwe kukhala mfumu+ ya anthu a Yehova,+ kutanthauza Aisiraeli.  Ukaphe anthu a m’nyumba ya mbuye wako Ahabu, kuti ine ndibwezere+ magazi a atumiki anga aneneri ndiponso magazi a atumiki onse a Yehova amene Yezebeli anapha.+  Nyumba yonse ya Ahabu+ ifafanizidwe. Ine ndidzapha munthu aliyense wokodzera khoma*+ wa m’banja la Ahabu, ngakhale aliyense wonyozeka ndi wopanda pake+ mu Isiraeli.  Ndidzachititsa nyumba ya Ahabu kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati, ndiponso ngati nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya. 10  Yezebeli adzadyedwa ndi agalu+ m’munda wa ku Yezereeli, ndipo palibe amene adzamuike m’manda.’” Mtumikiyo atamaliza kunena zimenezi, anatsegula chitseko n’kuthawa.+ 11  Ndiyeno Yehu anatuluka n’kupita kwa atumiki a mbuye wake. Atumikiwo anayamba kum’funsa kuti: “Zili bwino kodi?+ Nanga munthu wamisalayu+ amadzatani kwa iwe?” Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo mukum’dziwa bwino munthuyu ndiponso zonena zake.” 12  Koma iwo anati: “Ayi ukunama! Tiuze zoona.” Pamenepo Yehu anati: “Munthu uja anandiuza zakutizakuti, ndipo anati, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukudzoza iwe kukhala mfumu ya Isiraeli.”’”+ 13  Anthuwo atamva zimenezi, msangamsanga aliyense anavula malaya ake+ n’kumuyalira pamasitepe popanda kanthu. Kenako anayamba kuliza malipenga,+ ndipo anali kunena kuti: “Yehu wakhala mfumu!”+ 14  Tsopano Yehu+ mwana wa Yehosafati mwana wa Nimusi,+ anayamba kukonzera Yehoramu chiwembu.+ Pa nthawiyi n’kuti Yehoramu akulondera Ramoti-giliyadi+ pamodzi ndi Aisiraeli onse, chifukwa cha Hazaeli+ mfumu ya Siriya. 15  Pambuyo pake, mfumu Yehoramu+ inabwerera ku Yezereeli+ kukachira zilonda zake zimene Asiriya anaivulaza pamene inali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+ Kenako Yehu anati: “Ngati mukugwirizana nazo,+ musalole aliyense kuthawa kutuluka mumzinda uno kuti akanene ku Yezereeli.” 16  Tsopano Yehu anakwera galeta ulendo wa ku Yezereeli popeza Yehoramu anali chigonere kumeneko. Ahaziya+ mfumu ya Yuda anali atapita ku Yezereeli komweko kukaona Yehoramu. 17  Ku Yezereeliko,+ mlonda+ amene anaimirira pansanja+ anaona gulu lankhondo la Yehu likubwera mwaliwiro. Nthawi yomweyo mlondayo anati: “Ndikuona gulu la amuna likubwera mwaliwiro.” Pamenepo Yehoramu anati: “Uza munthu wokwera hatchi kuti apite kukakumana nawo. Akawafunse kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’”+ 18  Chotero munthu wokwera pahatchiyo anapitadi kukakumana ndi Yehu, n’kunena kuti, “Mfumu yanena kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’”+ Koma Yehu anati: “Ukudziwa chiyani zokhudza ‘mtendere’ iweyo? Tiye zinditsatira!” Ndiyeno mlonda+ wa pansanja uja anati: “Munthu wauthenga tinam’tuma uja wakumana nawo koma sakubwerera.” 19  Tsopano anatumiza munthu wina wachiwiri wokwera pahatchi. Iyenso atafika anati: “Mfumu yanena kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’”+ Koma Yehu anati: “Ukudziwa chiyani zokhudza ‘mtendere’ iweyo? Tiye zinditsatira!” 20  Mlonda wa pansanja uja ananenanso kuti: “Munthu tamutuma ujanso wakumana nawo, koma sakubwerera. Ndipo mmene anthuwo akuthamangira, akuthamanga ngati Yehu+ mdzukulu wa Nimusi,+ pakuti iye amathamangitsa galeta ngati wamisala.”+ 21  Yehoramu atamva zimenezi, anati: “Mangirirani mahatchi kugaleta!”+ Chotero anamangiriradi mahatchi kugaleta lake lankhondo. Ndiyeno Yehoramu mfumu ya Isiraeli ndi Ahaziya+ mfumu ya Yuda, ananyamuka aliyense pagaleta lake lankhondo, kupita kukakumana ndi Yehu, ndipo anakumana naye pamunda wa Naboti+ Myezereeli. 22  Yehoramu atangoona Yehu, nthawi yomweyo anam’funsa kuti: “Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?” Koma Yehu anayankha kuti: “Mtendere ungakhalepo bwanji+ pali dama la Yezebeli+ mayi ako ndi amatsenga ake ambirimbiri?”+ 23  Ndiyeno Yehoramu anatembenuza galeta lake kuti azithawa, ndipo anauza Ahaziya kuti: “Ahaziya, anthuwa atikonzera chiwembu!”+ 24  Pamenepo Yehu anakoka uta+ wake n’kulasa Yehoramu kumsana pakati pamapewa, mpaka muviwo unatulukira pamtima pake, moti Yehoramu anagwa m’galeta lake lankhondo.+ 25  Kenako Yehu anauza msilikali wake womuthandiza pagaleta+ dzina lake Bidikara, kuti: “Munyamule, umuponye m’munda wa Naboti Myezereeli.+ Kumbukira kuti iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu bambo ake, aliyense atakwera pagaleta lake la mahatchi awiri, pa nthawi imene Yehova anam’temberera+ kuti: 26  ‘“Ndithu magazi+ a Naboti ndi magazi a ana ake+ amene ndawaona dzulo,” watero Yehova, “ndidzawabwezera+ pa iwe ndithu m’munda uwu,” Yehova watero.’ Choncho munyamule, umuponye m’mundamo mogwirizana ndi mawu a Yehova.”+ 27  Ahaziya+ mfumu ya Yuda, anaona zonsezo moti anayamba kuthawa kudzera njira ya kumunda.*+ (Pambuyo pake Yehu anayamba kum’tsatira, ndipo anati: “Ameneyonso m’kantheni!” Choncho anam’kanthadi ali m’galeta lake pamene anali kuthawira ku Guru, kufupi ndi ku Ibuleamu.+ Iye anapitirizabe kuthawa mpaka ku Megido+ kumene anakafera.+ 28  Kenako atumiki ake anamunyamula m’galeta ndi kupita naye ku Yerusalemu kumene anakamuika m’manda ake pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ 29  Ahaziya+ anakhala mfumu ya Yuda m’chaka cha 11 cha Yehoramu+ mwana wa Ahabu.) 30  Kenako Yehu anafika ku Yezereeli,+ ndipo Yezebeli+ anamva zimenezo. Yezebeliyo anadzikongoletsa podzipaka utoto+ wakuda m’maso mwake n’kukongoletsanso tsitsi lake mochititsa kaso.+ Atatero anakaima pawindo n’kumayang’ana kunja.+ 31  Ndiyeno Yehu anafika pachipata, ndipo Yezebeli anati: “Kodi Zimiri+ amene anapha mbuye wake, zinthu zinamuyendera bwino?” 32  Yehu atamva mawu amenewa, anakweza maso kuyang’ana pawindopo, n’kufunsa kuti: “Ndani ali kumbali yanga? Ndani?”+ Nthawi yomweyo nduna ziwiri kapena zitatu za panyumba ya mfumu+ zinasuzumira pansi kuyang’ana Yehu. 33  Ndiyeno Yehu anati: “M’ponyeni+ pansi Yezebeliyo!” Iwo anam’ponyadi pansi, ndipo magazi ake ena anamwazika n’kuwaza khoma ndi mahatchi. Kenako Yehu anam’pondaponda+ ndi mahatchi ake. 34  Atatero, analowa m’nyumba ndipo anayamba kudya ndi kumwa, kenako anati: “Amuna inu, m’samaleni munthu wotembereredwayu.+ M’tengeni mukamuike m’manda, popeza ndi mwana wa mfumu.”+ 35  Atapita kuti akam’tenge kukamuika m’manda, sanapezepo chilichonse. Iwo anangopezapo mutu, mapazi, ndi zikhatho zake. + 36  Anthuwo atabwerera kwa Yehu kukamuuza, iye anati: “Amenewo ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera+ mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, kuti, ‘M’munda wa ku Yezereeli, agalu adzadya mnofu wa Yezebeli.+ 37  Ndipo mtembo wa Yezebeli, ndithu udzasanduka manyowa+ m’munda wa ku Yezereeli kuti anthu asadzanene kuti: “Uyu ndi Yezebeli.”’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Kokera chovala chako m’chiuno n’kuchimanga.”
Mawuwa ndi mkuluwiko wachiheberi wotanthauza mwamuna.
Mawu ake enieni, “Kudzera kunyumba ya kumunda.”