Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mafumu 3:1-27

3  Yehoramu+ mwana wa Ahabu, anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya m’chaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya Yuda, ndipo analamulira kwa zaka 12.  Iye anali kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ koma osati ngati mmene anachitira bambo ake+ kapenanso mmene anachitira mayi ake. Iye anachotsa chipilala chopatulika+ cha Baala chimene bambo ake anapanga.+  Komabe, anaumirira osasiya kuchita machimo a Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anachimwitsa+ nawo Isiraeli.  Mesa+ mfumu ya Mowabu anali woweta nkhosa. Ankapereka kwa mfumu ya Isiraeli ana a nkhosa 100,000, ndi nkhosa zamphongo zosameta ubweya zokwana 100,000 monga msonkho.  Ahabu atangomwalira,+ mfumu ya Mowabu inapandukira+ mfumu ya Isiraeli.  Pa nthawiyo, Mfumu Yehoramu inatuluka ku Samariya n’kukasonkhanitsa+ Aisiraeli onse.  Kuwonjezera apo, inatumiza uthenga kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, wakuti: “Mfumu ya Mowabu yandipandukira. Kodi upita nane kukamenya nkhondo ku Mowabu?” Yehosafati anayankha kuti: “Inde ndipita.+ Iwe ndi ine ndife amodzi. Anthu ako ndi anthu anga ndi amodzi.+ Mahatchi anga n’chimodzimodzi ndi mahatchi ako.”  Yehosafati anafunsa kuti: “Tidzera njira iti?” Yehoramu anayankha kuti: “Tidzera njira ya m’chipululu cha Edomu.”+  Choncho mfumu ya Isiraeli, mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu+ ananyamuka n’kuyenda mozungulira kwa masiku 7. Koma kuchipululuko kunalibe madzi oti anthuwo amwe pamodzi ndi ziweto zimene anali kuyenda nazo. 10  Kenako mfumu ya Isiraeli inati: “Kalanga ine! Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu!”+ 11  Pamenepo Yehosafati anati:+ “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova?+ Ngati alipo tiyeni tifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye.”+ Ndiyeno mmodzi mwa atumiki a mfumu ya Isiraeli anayankha kuti: “Kuli Elisa+ mwana wa Safati, amene anali kuthirira Eliya madzi osamba m’manja.”+ 12  Atamva zimenezo, Yehosafati anati: “Mawu a Yehova ali mwa iye.” Choncho mfumu ya Isiraeli, Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anapita kwa Elisa. 13  Elisa anafunsa mfumu ya Isiraeli kuti: “Ndili nanu chiyani?+ Pitani kwa aneneri+ a bambo anu ndi kwa aneneri a mayi anu.” Koma mfumu ya Isiraeliyo inati: “Ayi musatero, chifukwa Yehova wasonkhanitsa ife mafumu atatu kuti atipereke m’manja mwa Mowabu.”+ 14  Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova wa makamu Mulungu wamoyo amene ndimam’tumikira,+ pakanakhala kuti palibe Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikanakuyang’anani+ n’komwe kapena kukusamalani.+ 15  Anthu inu, ndiitanireni woimba zeze.”+ Woimba zezeyo atangoyamba kuimba, dzanja+ la Yehova linakhala pa Elisa. 16  Kenako iye anati: “Yehova wanena kuti, ‘Mukumbekumbe ngalande m’chigwa* chonsechi,+ 17  chifukwa Yehova wanena kuti: “Anthu inu simuona mphepo kapena mvula, koma chigwa chonsechi chidzaza madzi.+ Inu pamodzi ndi ziweto zanu, ndithu mumwa madziwo.”’+ 18  Zimenezi ndi zinthu zazing’ono kwambiri pamaso pa Yehova,+ ndipo ndithu apereka Amowabu m’manja mwanu.+ 19  Choncho mukagwetse mzinda uliwonse wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,+ mzinda uliwonse wabwino kwambiri,+ ndi mtengo uliwonse wabwino.+ Mukatseke akasupe onse amadzi, ndipo mukawononge malo alionse abwino mwa kuponyapo miyala.” 20  Ndiyeno zinachitika n’zakuti, pa nthawi yopereka nsembe yambewu+ m’mawa,+ anangoona madzi akuyenda kuchokera cha ku Edomu, ndipo malo onsewo anadzaza madzi. 21  Amowabu onse atamva kuti kwabwera mafumu kudzamenyana nawo, anasonkhanitsa amuna ambiri kuyambira amsinkhu wopita ku nkhondo+ kupita m’tsogolo, ndipo anakaima m’malire. 22  Atadzuka m’mawa, dzuwa linawalira pamadzi aja, moti kwa Amowabu amene anali kutsidya linalo, madziwo anaoneka ofiira ngati magazi. 23  Ataona zimenezi, anayamba kunena kuti: “Amenewa ndi magazi. Ndithu mafumu aja aphedwa ndi lupanga. Ndiye kuti aphana okhaokha. Tsopano Amowabu inu, tiyeni tikafunkhe!”+ 24  Iwo atalowa mumsasa wa Aisiraeli,+ nthawi yomweyo Aisiraeli ananyamuka n’kuyamba kuwapha. Amowabuwo anayamba kuthawa,+ ndipo Aisiraeli anathamangitsa Amowabuwo n’kumawapha mpaka kukalowa ku Mowabu. 25  Ndiyeno Aisiraeliwo anayamba kugwetsa mizinda.+ Pamalo alionse abwino, aliyense anali kuponyapo mwala mpaka kudzaza malo onsewo. Anatseka kasupe aliyense wamadzi+ ndi kugwetsa mtengo uliwonse wabwino.+ Koma miyala ya mzinda wa Kiri-hareseti+ yokha anaisiya. Oponya miyala anazungulira mzindawo n’kuuponya miyala. 26  Mfumu ya Mowabu itaona kuti nkhondo yaikulira, nthawi yomweyo inatenga amuna 700 amalupanga pofuna kudutsa kuti ikapeze mfumu ya Edomu,+ koma iwo analephera. 27  Pomalizira pake, mfumu ya Mowabu inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa amene akanalowa ufumu m’malo mwake, n’kumupereka+ nsembe yopsereza pakhoma. Choncho panabuka mkwiyo waukulu kwambiri wokwiyira Aisiraeli, motero iwo analeka kumenyana ndi mfumu ya Mowabu ndipo anabwerera kwawo.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.