Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mafumu 24:1-20

24  M’masiku ake, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera kudzachita nkhondo ndi Yerusalemu. Choncho Yehoyakimu anakhala mtumiki wake+ kwa zaka zitatu, koma kenako anam’pandukira.  Tsopano Yehova anayamba kum’tumizira Yehoyakimu magulu a achifwamba a Akasidi,+ a Asiriya, a Amowabu,+ ndi a ana a Amoni. Ankawatumiza ku Yuda kuti awononge dzikolo mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene analankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri.  Zimenezi zinachitikira Yuda molamulidwa ndi Yehova, kuti achotse+ dzikolo pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase,+ malinga ndi zonse zimene anachita,  komanso chifukwa cha magazi osalakwa+ amene iye anakhetsa, moti anadzaza Yerusalemu ndi magazi osalakwa, ndipo Yehova sanalole kukhululuka.+  Nkhani zina zokhudza Yehoyakimu+ ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.  Pomalizira pake Yehoyakimu anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Yehoyakini mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.  Mfumu ya Iguputo sinatulukenso+ m’dziko lake,+ chifukwa mfumu ya Babulo inali itatenga zinthu zonse zomwe zinali za mfumu ya Iguputo,+ kuyambira kuchigwa*+ cha Iguputo kukafika kumtsinje wa Firate.+  Yehoyakini+ anali ndi zaka 18 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Nehusita mwana wa Elinatani.  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene bambo ake anachita.+ 10  Pa nthawi imeneyo, atumiki a Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu n’kuzungulira mzindawo.+ 11  Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo atumiki ake atauzungulira.+ 12  Patapita nthawi, Yehoyakini mfumu ya Yuda anatuluka n’kupita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake,+ atumiki ake, akalonga ake, ndi nduna za panyumba yake, ndipo mfumu ya Babuloyo inam’tengera Yehoyakini ku ukapolo m’chaka cha 8+ cha ufumu wake. 13  Mfumu ya Babulo inatenga chuma chonse cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Inaphwanyaphwanyanso ziwiya zonse+ zagolide zimene Solomo mfumu ya Isiraeli anapangira kachisi wa Yehova, monga momwe Yehova ananenera. 14  Mfumuyo inatenga+ anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ mmisiri aliyense+ ndi munthu aliyense womanga makoma achitetezo, n’kupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu onyozeka+ okha a m’dzikolo. 15  Chotero iye anatengera Yehoyakini+ ku Babulo.+ Anatenga ku Yerusalemu mayi a mfumuyo,+ akazi ake, nduna za panyumba yake,+ ndi akuluakulu a m’dzikolo, n’kuwapititsa ku Babulo. 16  Mfumu ya Babulo inatengera ku Babulo amuna onse olimba mtima okwana 7,000, amisiri ndi anthu omanga makoma achitetezo okwana 1,000, ndi amuna onse amphamvu omenya nkhondo.+ 17  Komanso mfumu ya Babulo+ inatenga Mataniya, bambo ake aang’ono+ a Yehoyakini, n’kuwaika kukhala mfumu m’malo mwake. Kenako inam’sintha dzina Mataniya kuti akhale Zedekiya.+ 18  Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina, ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 19  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+ 20  Zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda zinakwiyitsa+ kwambiri Yehova ndipo anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.