Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mafumu 20:1-21

20  M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.+ Choncho mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anabwera kwa iye n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita,+ chifukwa iweyo ufa ndithu. Sukhala ndi moyo.’”+  Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova+ kuti:  “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+  Pamene Yesaya anali kutuluka, asanafike n’komwe pabwalo lapakati, mawu a Yehova anam’fikira,+ akuti:  “Bwerera, kauze Hezekiya mtsogoleri+ wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu+ wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva+ pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Ndikuchiritsa.+ Pa tsiku lachitatu udzapita kunyumba ya Yehova.+  Ndithu ndiwonjezera zaka 15 pa masiku ako, ndipo ndidzalanditsa+ iweyo ndi mzindawu m’manja mwa mfumu ya Asuri. Ndidzateteza mzinda uno chifukwa cha ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+  Kenako Yesaya anati: “Amuna inu, tengani nkhuyu zouma zoumba pamodzi.”+ Choncho iwo anatenga nkhuyuzo n’kuziika pachithupsa+ chimene anali nacho, ndipo Hezekiya anachira pang’onopang’ono.+  Pa nthawiyi, Hezekiya anafunsa Yesaya kuti: “Kodi chizindikiro chakuti Yehova andichiritsa, ndi kuti ndidzapitadi kunyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu n’chiyani?”+  Yesaya anayankha kuti: “Chizindikiro+ chochokera kwa Yehova, chakuti Yehova adzakwaniritsadi mawu amene walankhula, ndi ichi: Kodi mthunzi uyende masitepe 10 kupita kutsogolo, kapena uyende masitepe 10 kubwerera m’mbuyo pamasitepe olowera m’nyumba?” 10  Hezekiya anayankha kuti: “N’zosavuta kuti mthunzi upite kutsogolo masitepe 10, koma osati kubwerera m’mbuyo masitepe 10.”+ 11  Pamenepo mneneri Yesaya anayamba kufuulira Yehova, ndipo iye anachititsa mthunzi umene unali utapita kale kutsogolo kuti ubwerere m’mbuyo pang’onopang’ono pamasitepe a Ahazi. Mthunziwo unabwerera m’mbuyo masitepe 10.+ 12  Pa nthawi imeneyo, Berodaki-baladani+ mwana wa Baladani mfumu ya Babulo,+ anatumiza makalata+ ndi mphatso kwa Hezekiya chifukwa anamva kuti Hezekiya anali kudwala. 13  Hezekiya anawamvetsera anthuwo ndipo anawaonetsa zonse za m’nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide,+ mafuta a basamu,+ mafuta abwino, nyumba yake yosungiramo zida zankhondo, ndi chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse m’nyumba yake ndi mu ufumu wake wonse.+ 14  Pambuyo pake mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya n’kuifunsa kuti:+ “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, ndipo anachokera kuti?”+ Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.” 15  Ndiyeno Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani m’nyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili m’nyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”+ 16  Tsopano Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imvani mawu a Yehova.+ 17  ‘“Masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili m’nyumba mwako,+ ndi zonse zimene makolo ako akhala akusunga kufikira lero, anthu adzazitenga n’kupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,”+ watero Yehova. 18  “Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna+ za panyumba ya mfumu ya ku Babulo.”’”+ 19  Pamenepo Hezekiya anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwalankhulawa ndi abwino.”+ Anapitiriza kuti: “Ngati mtendere ndi chilungamo+ zipitirire m’masiku anga, ndiye kuti zili bwino, si choncho?”+ 20  Nkhani zina zokhudza Hezekiya ndi zochita zake zonse zamphamvu, ndiponso mmene anakumbira dziwe+ ndi ngalande+ n’kubweretsa madzi mumzindawo, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 21  Pomalizira pake, Hezekiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Manase+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi