Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Mafumu 2:1-25

2  Yehova atatsala pang’ono kutenga Eliya+ mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,+ Eliya ndi Elisa+ ananyamuka ku Giligala.+  Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo+ ndiponso pali moyo wanu,+ sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapita ku Beteli.+  Ndiyeno ana a aneneri+ amene anali ku Beteli anabwera kwa Elisa n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?”+ Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa bwino zimenezo.+ Khalani chete.”  Tsopano Eliya anauza Elisa kuti: “Khala apa Elisa, pakuti ine Yehova wandituma ku Yeriko.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.” Choncho iwo anafika ku Yeriko.  Kenako ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa n’kumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?” Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa bwino zimenezo. Khalani chete.”+  Tsopano Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo khala apa, pakuti ine Yehova wandituma ku Yorodano.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.”+ Choncho iwo anapitiriza ulendo wawo.  Ndiyeno panali ana a aneneri 50 omwe anakaima chapatali poonekera.+ Koma Eliya ndi Elisa anakaima pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.  Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika uku ndi uku, chotero iwo anawoloka pouma.+  Iwo atangowoloka, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanakuchokere.”+ Elisa anati: “Chonde, magawo awiri+ a mzimu+ wanu abwere kwa ine.”+ 10  Eliya anati: “Wapempha+ chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.” 11  Pamene anali kuyenda n’kumalankhulana, anangoona galeta*+ lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto. Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo n’kuwalekanitsa, ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba.+ 12  Nthawi yonseyi Elisa anali kuona zimene zinali kuchitikazo, ndipo anali kufuula kuti: “Bambo anga, bambo anga!+ Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Zitatero, Elisa sanamuonenso Eliya. Kenako Elisa anagwira zovala zake n’kuzing’amba pakati.+ 13  Atatero anatola chovala chauneneri+ cha Eliya chimene chinagwa pansi, ndipo anabwerera kukaima m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano. 14  Ali pamenepo, anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija n’kumenya nacho madzi a mtsinjewo,+ n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?”+ Atamenya madziwo, pang’onopang’ono madziwo anagawanika uku ndi uku, ndipo Elisa anawoloka. 15  Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu+ wa Eliya uli pa Elisa.” Chotero anapita kukakumana naye n’kugwada+ pamaso pake mpaka nkhope zawo pansi. 16  Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu, bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu+ wa Yehova wamunyamula ndipo wam’ponya paphiri linalake kapena m’chigwa.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatumize.” 17  Koma iwo anam’kakamiza mpaka iye anachita manyazi, choncho anati: “Atumizeni.” Chotero anatumiza amuna 50 kukafunafuna Eliya. Iwo anam’funafuna kwa masiku atatu koma sanam’peze. 18  Ndiyeno anabwerera kwa Elisa ku Yeriko.+ Anthuwo atafika, Elisa ananena kuti: “Kodi ine sindinakuuzeni kuti, ‘Musapite’?” 19  Patapita nthawi, anthu a mumzindawo anauza Elisa kuti: “Mzindawu uli pamalo abwino+ monga mmene inu mbuyathu mukuonera, koma madzi+ ake ndi oipa, ndipo nthaka ikuchititsa akazi kupita padera.”+ 20  Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni mbale yaing’ono yatsopano yolowa, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anam’bweretseradi mbaleyo. 21  Ndiyeno Elisa anapita pamene panayambira madziwo n’kuponyapo mchere uja,+ n’kunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndakonza madziwa kuti akhale abwino.+ Sadzachititsanso imfa kapena kuchititsa akazi kupita padera.’” 22  Madziwo ndi abwino kufikira lero+ mogwirizana ndi mawu amene Elisa ananena. 23  Kenako Elisa ananyamuka kupita ku Beteli.+ Akuyenda kukwezeka chitunda, anyamata ena+ amene anachokera mumzinda anayamba kumunyoza mokuwa+ kuti: “Choka kuno wadazi iwe!+ Choka kuno wadazi iwe!” 24  Pomalizira pake Elisa anatembenuka ndipo anawaona. Atatero anawaitanira tsoka+ m’dzina la Yehova. Kenako zimbalangondo ziwiri zazikazi+ zinatuluka m’thengo n’kukhadzulapo anyamata 42.+ 25  Elisa anapitiriza ulendo wake mpaka kuphiri la Karimeli.+ Atachoka kumeneko anabwerera n’kupita ku Samariya.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”