Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Akorinto 6:1-18

6  Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukudandauliraninso kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu n’kuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+  Pakuti iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo m’tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa.+ Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.+  Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa,+ kuti utumiki wathu usapezedwe chifukwa.+  Koma tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi mwa kupirira zambiri, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, kukumana ndi zovuta,+  kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende,+ kukumana ndi zipolowe, kugwira ntchito mwakhama, kusagona tulo, ndi kukhala osadya.+  Tikusonyezanso zimenezi mwa kukhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ okhala ndi mzimu woyera, osonyeza chikondi chopanda chinyengo,+  olankhula zoona, ndiponso okhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso, tikuchita zimenezi ponyamula zida+ za chilungamo kudzanja lamanja ndi lamanzere,  mwa kupatsidwa ulemerero ndi kutonzedwa, mwa kuneneredwa zoipa komanso zabwino. Mwa kukhala ngati achinyengo+ koma oona mtima,  ngati osadziwika koma odziwika bwino,+ ngati oti tikufa koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa+ koma osakaphedwa,+ 10  ngati ogwidwa ndi chisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri, ngati opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.+ 11  Takhala tikulankhula mosabisa mawu kwa inu Akorinto, tafutukula mtima wathu.+ 12  Malo sakukucheperani mumtima mwathu,+ koma m’chikondi chanu ndi mmene muli malo ochepa.+ 13  Choncho mutibwezere zofanana ndi zimene takuchitirani. Ndikulankhula nanu ngati ana anga,+ inunso futukulani mtima wanu. 14  Musamangidwe m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+ 15  Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Kapena munthu wokhulupirira angagawane+ chiyani ndi wosakhulupirira? 16  Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ 17  “‘Choncho tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+ 18  “‘Ndidzakhala atate wanu,+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova Wamphamvuyonse.”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti, “Wopanda pake,” amene ndi woipayo, Satana.
Onani Zakumapeto 2.