Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Akorinto 5:1-21

5  Tikudziwa kuti nyumba yathu ya padziko lapansi pano,+ msasa uno,+ ikadzaphwasuka,+ tidzalandira nyumba yochokera kwa Mulungu. Imeneyo idzakhala nyumba yosamangidwa ndi manja,+ koma yamuyaya,+ ndipo idzakhala kumwamba.  Pakuti tikubuula m’nyumba imene tikukhalamoyi+ pofunitsitsa kuvala yathu yakumwamba,+  kuti tikadzaivala, tisadzapezeke amaliseche.+  Ndipotu, ife amene tili mumsasa uno tikubuula chifukwa cholemedwa. Kwenikweni si chifukwa chofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo,+ kuti chokhoza kufachi chilowedwe m’malo ndi moyo.+  Tsopano amene anatikonzekeretsa kuti tilandire zimenezi ndi Mulungu.+ Iye ndiye anatipatsa chikole+ cha zinthu zam’tsogolo, chomwe ndi mzimu.+  Chotero nthawi zonse timakhala olimba mtima ndipo tikudziwa kuti pamene tikukhala m’thupi, tili kutali ndi Ambuye,+  pakuti tikuyenda mwa chikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.+  Koma tikulimba mtima ndipo ndife okondwa kukakhala ndi Ambuye, m’malo mokhala m’thupi linoli.+  Choncho n’cholinga chathunso kuti, kaya tikhale ndi iye kapena tikhale kutali naye,+ tikhale ovomerezeka kwa iye.+ 10  Pakuti mtima wa aliyense wa ife udzaonekera pamaso pa mpando woweruzira milandu wa Khristu,+ kuti aliyense alandire mphoto yake pa zinthu zimene anachita ali m’thupi, mogwirizana ndi zimene anali kuchita, zabwino kapena zoipa.+ 11  Choncho popeza timaopa+ Ambuye, tikupitiriza kukopa+ anthu. Mulungu akudziwa bwino zolinga zathu. Koma ndili ndi chikhulupiriro kuti inunso, mwachikumbumtima chanu, mukudziwa bwino zolinga zathu.+ 12  Sikuti tayambanso kudzichitira umboni+ tokha kwa inu ayi, koma tikukupatsani chifukwa chodzitamandira, ndipo chifukwacho ndifeyo,+ kuti muwayankhe amene amadzitama chifukwa cha maonekedwe akunja,+ osati chifukwa cha mtima.+ 13  Pakuti ngati tinachita misala,+ tinachitira Mulungu. Ngati tili olongosoka,+ cholinga ndi kupindulitsa inuyo. 14  Pakuti chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse,+ chifukwatu onsewo anali atafa kale. 15  Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha,+ koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera+ n’kuukitsidwa.+ 16  Ndiye chifukwa chake kuyambira tsopano sitiona munthu mwakuthupi.+ Ngakhale kuti Khristu tinamuona mwakuthupi,+ tsopano sitikumuonanso motero.+ 17  Choncho ngati aliyense ali wogwirizana ndi Khristu, iye ndi cholengedwa chatsopano.+ Zinthu zakale zinatha,+ ndipo pali zatsopano.+ 18  Koma zinthu zonse n’zochokera kwa Mulungu, amene anatigwirizanitsa+ ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, ndipo anatipatsa utumiki+ wokhazikitsanso mtendere. 19  Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu anali kugwirizanitsa dziko+ ndi iyeyo+ kudzera mwa Khristu,+ moti sanawawerengere anthuwo machimo awo,+ ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolengeza uthenga+ umenewu wokhazikitsanso mtendere.+ 20  Chotero ndife+ akazembe+ m’malo mwa Khristu,+ ngati kuti Mulungu akuchonderera anthu kudzera mwa ife.+ Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti:+ “Gwirizananinso ndi Mulungu.” 21  Amene analibe uchimoyo,+ Mulungu anamupanga kukhala uchimo+ chifukwa cha ife, kuti tikhale olungama pamaso pa Mulungu+ kudzera mwa iye.

Mawu a M'munsi