Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Akorinto 4:1-18

4  Popeza tili ndi utumiki umenewu+ malinga ndi chifundo chimene tinasonyezedwa,+ sitikubwerera m’mbuyo.  Koma tasiya zinthu zochititsa manyazi zochitikira mseri,+ ndipo sitikuyenda mwachinyengo komanso sitikupotoza mawu a Mulungu.+ Koma pamaso pa Mulungu, takhala chitsanzo chabwino kwa chikumbumtima cha munthu aliyense.+  Tsopano ngati uthenga wabwino umene tikulengeza uli wophimbika, ndi wophimbika pakati pa anthu amene akupita kukawonongedwa.+  Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi* ino+ wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira,+ kuti asaone+ kuwala+ kwa uthenga wabwino waulemerero+ wonena za Khristu, yemwe ali chifaniziro+ cha Mulungu.  Pakuti sitikulalikira za ifeyo koma za Khristu Yesu, kuti iye ndiye Ambuye+ ndipo ifeyo ndife akapolo+ anu chifukwa cha Yesu.  Pakuti Mulungu ndiye anati: “Kuwala kuunike kuchokera mu mdima,”+ ndipo kudzera mwa nkhope ya Khristu,+ waunika mitima yathu kuti iwale+ ndi ulemerero wokhudzana ndi kudziwa+ Mulungu.  Komabe, tili ndi chuma+ chimenechi m’zonyamulira+ zoumbidwa ndi dothi,+ kuti mphamvu+ yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu,+ osati kwa ife.+  Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse,+ koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.+  Timazunzidwa, koma osati mochita kusowa kolowera.+ Timagwetsedwa pansi,+ koma sitiwonongedwa.+ 10  Kulikonse kumene tikupita, timapirira m’matupi mwathu ndipo timakhala pa ngozi yoti tikhoza kuphedwa, ngati mmene Yesu anachitira,+ kuti moyo wa Yesu uonekerenso m’matupi mwathu.+ 11  Pakuti nthawi zonse amoyofe timakhala pa ngozi yoti tikhoza kuphedwa+ chifukwa cha Yesu, kuti moyo wa Yesu uonekerenso m’thupi lathu lokhoza kufali.+ 12  Choncho ngakhale kuti moyo wathu ukukhala pa ngozi, zimenezi zikubweretsa moyo kwa inuyo.+ 13  Tsopano, popeza tili ndi mtima wachikhulupiriro wofanana ndi umene anaunena kuti: “Ndinali ndi chikhulupiriro, chotero ndinalankhula,”+ ifenso tili ndi chikhulupiriro, chotero tikulankhula, 14  podziwa kuti amene anaukitsa Yesu adzaukitsanso ifeyo pamodzi ndi Yesu, ndipo adzatipititsa pamaso pa Yesuyo pamodzi ndi inuyo.+ 15  Pakuti zonsezi zachitika chifukwa cha ubwino wanu.+ Ndiponso zachitika kuti kukoma mtima kwakukulu kumene kunawonjezeka kuchulukebe chifukwa cha anthu ambiri amene akupereka mapemphero oyamikira, zimene zikuchititsa kuti Mulungu alandire ulemerero.+ 16  Choncho sitikubwerera m’mbuyo. Koma ngakhale munthu wathu wakunja akutha, ndithudi munthu wathu wamkati+ akukhalitsidwanso watsopano tsiku ndi tsiku. 17  Pakuti ngakhale kuti masautso amene tikukumana nawo ndi akanthawi+ ndipo ndi opepuka, masautsowo akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso wamuyaya,+ 18  pamene tikuika maso athu pa zinthu zosaoneka, osati pa zooneka.+ Pakuti zooneka n’zakanthawi,+ koma zosaoneka n’zamuyaya.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.