Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Akorinto 3:1-18

3  Kodi tikuyambanso kudzichitira umboni tokha?+ Kapena kodi n’kofunika kuti ifenso, mofanana ndi anthu ena, tikhale ndi makalata+ otichitira umboni kwa inu kapena ochokera kwa inu?  Inuyo ndiye kalata yathu,+ yolembedwa pamitima yathu, yodziwika ndiponso yowerengedwa ndi anthu onse.+  Pakuti zikuonekeratu kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu yolembedwa ndi ifeyo kudzera mu utumiki wathu.+ Kalatayo siyolembedwa ndi inki koma ndi mzimu+ wa Mulungu wamoyo. Siyolembedwa pazolembapo zamiyala,+ koma zamnofu, pamitima.+  Tsopano kudzera mwa Khristu, tikhoza kunena zimenezi molimba mtima+ pamaso pa Mulungu.  Sitinganene kuti ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha mphamvu zathu,+ koma ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha Mulungu,+  ndipo chifukwa cha iyeyo ndife oyenera kukhala atumiki a pangano latsopano,+ ndipo ndife ogwirizana osati kudzera m’malamulo olembedwa,+ koma mu mzimu.+ Pakuti malamulo olembedwa amaweruza munthu+ kuti afe, koma mzimu umapatsa munthu moyo.+  Ndiponso malamulo amene amapereka imfa,+ amenenso analembedwa pamiyala,+ anabwera ndi ulemerero waukulu kwambiri+ moti ana a Isiraeli sanathe kuyang’anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa inali kuwala ndi ulemerero,+ ulemerero umene unatha patapita nthawi.  Chotero, kodi mzimu+ sukuyenera kuperekedwa ndi ulemerero waukulu koposa pamenepa?+  Pakuti ngati malamulo oweruza anthu kuti alangidwe+ anaperekedwa ndi ulemerero,+ chilungamo chikuyenera kuperekedwa+ ndi ulemerero waukulu kuposa pamenepa.+ 10  Nawonso malamulo olembedwa amene anapatsidwa ulemerero poyamba achotsedwa ulemererowo,+ chifukwa ulemerero umene wabwera pambuyo pawo ndi wokulirapo.+ 11  Pakuti ngati malamulo olembedwa, amene anatha patapita nthawi, anaperekedwa ndi ulemerero,+ ndiye kuti okhalapo nthawi zonse adzakhala ndi ulemerero woposa pamenepo.+ 12  Chotero popeza tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ tikulankhula momasuka kwambiri, 13  osati ngati Mose amene anaphimba nkhope yake ndi nsalu,+ kuti ana a Isiraeli asaone kutha+ kwa ulemerero wosakhalitsawo. 14  Ndipo maganizo awo anachita khungu.+ Pakuti mpaka lero, nsaluyo imakhalabe yophimba powerenga pangano lakale,+ chifukwa imachotsedwa kudzera mwa Khristu basi.+ 15  Moti mpaka lero, pamene zolemba za Mose zikuwerengedwa,+ mitima yawo imakhalabe yophimba.+ 16  Koma munthu akatembenukira kwa Yehova, chophimbacho chimachotsedwa.+ 17  Tsopano Yehova ndiye Mzimu,+ ndipo pamene pali mzimu+ wa Yehova,+ pali ufulu.+ 18  Tonsefe+ tili ndi nkhope zosaphimba ndipo tili ngati magalasi oonera amene amaonetsa ulemerero wa Yehova.+ Pamene tikuonetsa ulemerero umenewu, timasintha+ n’kukhala ngati chifaniziro chake+ ndipo timaonetsa ulemerero wowonjezerekawonjezereka+ mofanana ndendende ndi mmene Yehova, amene ndi Mzimu, watisinthira.+

Mawu a M'munsi