Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

2 Akorinto 1:1-24

1  Ine Paulo, mtumwi+ wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu, ndikulembera mpingo wa Mulungu wa ku Korinto, pamodzi ndi oyera onse+ amene ali mu Akaya+ monse, ndili limodzi ndi Timoteyo+ m’bale wathu, kuti:  Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu.+  Atamandike Mulungu ndi Atate+ wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wachifundo chachikulu+ ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,+  amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse,+ kuti tithe kutonthoza+ amene ali m’masautso amtundu uliwonse, chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.+  Popeza tikukumana ndi masautso ambiri chifukwa cha Khristu,+ tikutonthozedwanso kwambiri kudzera mwa Khristu.+  Tsopano ngati tili m’masautso, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa.+ Ngati tikutonthozedwa, cholinga chake ndi choti inuyo mutonthozedwe kuti mupirire masautso amene ifenso tikukumana nawo.+  Chotero chiyembekezo chathu mwa inu sichikugwedera, podziwa kuti mukukumana ndi masautso ofanana ndi amene ifeyo tikukumana nawo, inunso mudzatonthozedwa ngati ifeyo.+  Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo m’chigawo cha Asia,+ pamene tinali pa vuto lalikulu lotiposa mphamvu, moti tinalibenso chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.+  Ngakhalenso m’mitima mwathu, tinali kumva ngati talandira chiweruzo cha imfa. Zinatero kuti tisakhale ndi chikhulupiriro mwa ife tokha,+ koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa.+ 10  Iye anatipulumutsadi ku chinthu choopsa, ndicho imfa, ndipo adzatipulumutsabe.+ Tikukhulupirira kuti iye apitiriza kutipulumutsa.+ 11  Inunso mungathandizepo mwa kutiperekera mapembedzero anu,+ kuti pakhale anthu ambiri otiperekera mapemphero oyamikira+ zinthu zimene tapatsidwa mokoma mtima, chifukwa cha mapemphero a anthu ambiri.+ 12  Ifeyo tili ndi chifukwa chodzitamandira chakuti m’dzikoli, makamaka pakati pa inuyo, tachita zinthu zoyera ndiponso moona mtima mogwirizana ndi zimene Mulungu amaphunzitsa. Tachita zimenezi osati modalira nzeru+ za m’dzikoli koma modalira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndipo chikumbumtima chathu chikuchitiranso umboni zimenezi.+ 13  Pakuti zimene takulemberanizi si zina ayi, koma zimene mukuzidziwa bwino ndiponso zimene mukuzivomereza. Ndili ndi chikhulupiriro choti mupitiriza kuvomereza zinthu zimenezi mpaka pa mapeto.+ 14  Inuyo mwavomereza kale, ngakhale kuti m’pang’ono pokha, kuti ifeyo ndife chifukwa choti mudzitamandire,+ ngati mmene inuyonso mudzakhalire chifukwa choti ifeyo tidzadzitamandire m’tsiku la Ambuye wathu Yesu.+ 15  Choncho, popeza ndine wotsimikiza za zimenezi, ndinali ndi cholinga chofika kwa inu poyamba,+ kuti mudzakhale ndi mwayi wachiwiri+ wosangalala. 16  Kuti ndikadzacheza nanu pang’ono ndidzapite ku Makedoniya,+ ndipo ndikadzachoka ku Makedoniya ndidzabwerenso kwa inu+ kuti mudzandiperekeze+ popita ku Yudeya. 17  Tsopano pamene ndinali ndi cholinga chimenechi, kodi ndinali kulingalira mwachibwana?+ Kapena kodi zimene ndimaganiza kuti ndichite, ndimaziganiza ndi zolinga zadyera,+ kuti ndikati “Inde, inde” nthawi yomweyo ndisinthe ndinene kuti “Ayi, ayi”?+ 18  Koma Mulungu ndi wodalirika kuti mawu athu kwa inu asakhale Inde kenako Ayi. 19  Pakuti Mwana wa Mulungu,+ Khristu Yesu, amene analalikidwa pakati panu kudzera mwa ineyo, Silivano, ndi Timoteyo,+ sanakhale Inde kenako Ayi, koma mwa iye, Inde wakhalabe Inde.+ 20  Ndiponso malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani,+ akhala Inde kudzera mwa iye.+ Choteronso kudzera mwa iye, “Ame”+ amanenedwa kwa Mulungu kuti Mulungu alandire ulemerero kudzera mwa ife. 21  Koma amene amatitsimikizira kuti inuyo ndi ife tili a Khristu, amenenso anatidzoza,+ ndiye Mulungu. 22  Iye watiikanso chidindo+ chake chotitsimikizira ndipo watipatsa m’mitima mwathu chikole+ cha madalitso am’tsogolo, ndicho mzimu.+ 23  Mulungu akhale mboni+ pa moyo wanga kuti chifukwa chimene sindinabwererebe ku Korintoko n’chakuti sindinafune kuti ndidzawonjezere chisoni chanu.+ 24  Sikuti ndife olamulira+ chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu+ kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika+ chifukwa cha chikhulupiriro chanu.+

Mawu a M'munsi