Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Yohane 3:1-24

3  Taganizirani za chikondi chachikulu+ chimene Atate watisonyeza. Watitchula kuti ndife ana a Mulungu,+ ndipo ndifedi ana ake. N’chifukwa chake dziko+ silitidziwa, pakuti silimudziwa iyeyo.+  Okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu,+ koma padakali pano sizinaonekerebe kuti tidzakhala otani.+ Tikudziwa kuti akadzaonekera,+ tidzakhala ngati iyeyo,+ chifukwa tidzamuona mmene alili.+  Ndipo aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi mwa iye, amadziyeretsa+ pakuti iye ndi woyera.+  Aliyense amene amachita tchimo+ samvera malamulo,+ choncho tchimo+ ndilo kusamvera malamulo.  Inu mukudziwanso kuti iye anaonekera kuti achotse machimo athu,+ ndipo mwa iye mulibe tchimo.+  Aliyense amene ali wogwirizana+ ndi Yesu sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo.+ Aliyense amene amachita tchimo ndiye kuti sanamuone kapena kumudziwa.+  Ana inu, wina asakusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama ngati mmene Yesu alili wolungama.+  Amene amachitabe tchimo anachokera kwa Mdyerekezi, chifukwa Mdyerekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi.+ Choncho, Mwana wa Mulungu anaonekera+ kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.+  Aliyense amene ali mwana wa Mulungu sapitiriza kuchita tchimo,+ chifukwa mbewu ya Mulungu yopatsa moyo imakhalabe mwa munthu ameneyo, ndipo sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.+ 10  Ana a Mulungu ndiponso ana a Mdyerekezi amaonekera bwino ndi mfundo iyi: Aliyense amene sachita zolungama+ sanachokere kwa Mulungu, chimodzimodzinso amene sakonda m’bale wake.+ 11  Pakuti uwu ndi uthenga umene munamva kuyambira pa chiyambi,+ kuti tizikondana,+ 12  osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha+ m’bale wake. N’chifukwa chiyani iye anapha m’bale wake? Chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa,+ koma za m’bale wake zinali zolungama.+ 13  Abale, musadabwe kuti dziko limakudani.+ 14  Tikudziwa kuti tinali akufa koma tsopano ndife amoyo+ chifukwa timakonda abale athu.+ Amene sakonda m’bale wake ndiye kuti adakali mu imfa.+ 15  Aliyense amene amadana+ ndi m’bale wake ndi wopha munthu,+ ndipo mukudziwa kuti aliyense wopha munthu+ sadzalandira moyo wosatha.+ 16  Tadziwa chikondi+ chifukwa chakuti iye anapereka moyo wake chifukwa cha ife,+ ndipo ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.+ 17  Koma aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo,+ n’kuona m’bale wake zikumusowa,+ koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu,+ kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?+ 18  Ana anga okondedwa,+ tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha,+ koma tizisonyezana chikondi chenicheni+ m’zochita zathu.+ 19  Mwa njira imeneyi tidzadziwa kuti ndife ochokera m’choonadi,+ ndipo tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu 20  pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse,+ chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.+ 21  Okondedwa, ngati mitima yathu sititsutsa, tikhoza kulankhula momasuka ndi Mulungu,+ 22  ndipo chilichonse chimene tingapemphe, iye adzatipatsa,+ chifukwa tikusunga malamulo ake ndi kuchita zinthu zomukondweretsa.+ 23  Lamulo lake ndi lakuti, tikhale ndi chikhulupiriro m’dzina la Mwana wake Yesu Khristu+ ndiponso tizikondana,+ monga mmene iye anatilamulira. 24  Komanso, munthu wosunga malamulo ake amakhalabe wogwirizana naye.+ Iyenso amakhala wogwirizana ndi munthuyo, ndipo chifukwa cha mzimu+ umene anatipatsa, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+

Mawu a M'munsi