Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Yohane 2:1-29

2  Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo.+ Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi+ wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.+  Iye ndi nsembe+ yophimba+ machimo athu.+ Osati athu+ okha, komanso a dziko lonse lapansi.+  Tikapitiriza kusunga malamulo ake ndiye kuti tikumudziwa.+  Munthu amene amanena kuti: “Ine ndikumudziwa,”+ koma sasunga malamulo ake,+ ameneyo ndi wabodza, ndipo mwa munthu ameneyo mulibe choonadi.+  Koma aliyense wosunga mawu ake,+ amasonyeza kuti amakondadi Mulungu.+ Chifukwa cha zimenezi, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+  Amene amanena kuti ndi wogwirizana+ naye, ayenera kupitiriza kuyenda mmene iyeyo anayendera.+  Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lamulo lakale+ limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi.+ Lamulo lakale limeneli ndiwo mawu amene munamva.  Komabe, ndikukulemberani lamulo latsopano limene Yesu analitsatira, limenenso inuyo mukulitsatira, chifukwa chakuti mdima+ ukupita ndipo kuwala kwenikweni+ kwayamba kale kuunika.  Amene amanena kuti ali m’kuunika koma amadana+ ndi m’bale wake, ndiye kuti ali mu mdima mpaka pano.+ 10  Amene amakonda m’bale wake ndiye kuti ali m’kuunika,+ ndipo palibe chimene chingamukhumudwitse.+ 11  Koma amene amadana ndi m’bale wake ndiye kuti ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdimawo,+ ndiponso sakudziwa kumene akupita+ chifukwa maso ake achita khungu chifukwa cha mdimawo. 12  Ndikukulemberani inu ana anga okondedwa, pakuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina lake.+ 13  Ndikulembera abambo inu, chifukwa mukumudziwa amene wakhala alipo kuyambira pa chiyambi.+ Ndikulemberanso inu anyamata+ chifukwa mwagonjetsa woipayo.+ Ndikulembera inu ana+ chifukwa mukuwadziwa Atate.+ 14  Ndikulembera inu abambo+ chifukwa mukumudziwa iye amene wakhalapo kuyambira pa chiyambi.+ Ndikulembera inu anyamata chifukwa ndinu olimba+ ndipo mawu a Mulungu akhaladi mwa inu+ ndiponso mwagonjetsa woipayo.+ 15  Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko.+ Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.+ 16  Pakuti chilichonse cha m’dziko,+ monga chilakolako cha thupi,+ chilakolako cha maso+ ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake,+ sizichokera kwa Atate, koma kudziko.+ 17  Ndiponso, dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake,+ koma wochita chifuniro+ cha Mulungu adzakhala kosatha.+ 18  Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto,+ ndipo monga mmene munamvera kuti wokana Khristu akubwera,+ ngakhale panopa alipo okana Khristu ambiri.+ Chifukwa cha zimenezi timadziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto. 19  Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu,+ chifukwa akanakhala a m’gulu lathu, akanakhalabe ndi ife.+ Sikuti onse ali m’gulu lathu ayi, ndipo iwo achoka m’gulu lathu, kuti zimenezi zidziwike.+ 20  Inu munadzozedwa ndi woyerayo,+ ndipo nonsenu ndinu odziwa choonadi.+ 21  Ndikukulemberani izi, osati chifukwa chakuti simudziwa choonadi,+ koma chifukwa chakuti mukuchidziwa,+ ndiponso chifukwa chakuti palibe bodza lililonse limene limachokera m’choonadi.+ 22  Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?+ Ameneyu ndiye wokana Khristu,+ amene amakana Atate ndi Mwana.+ 23  Aliyense amene amakana Mwana sangakhale pa ubwenzi ndi Atate.+ Amene wavomereza+ Mwana amakhalanso pa ubwenzi ndi Atate.+ 24  Koma zimene inu munamva pa chiyambi zikhalebe mumtima mwanu.+ Zimene munamva pa chiyambi zikakhalabe mumtima mwanu, mudzakhalanso ogwirizana+ ndi Mwana ndi Atate.+ 25  Ndipotu, lonjezo limene iye watipatsa ndi la moyo wosatha.+ 26  Ndikukulemberani za anthu amene akufuna kukusocheretsani.+ 27  Inuyo, Mulungu anakudzozani ndi mzimu+ ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu. Chotero simukufunikira wina aliyense kuti azikuphunzitsani,+ koma popeza kuti munadzozedwadi moona+ osati monama, chifukwa cha kudzozedwako, mukuphunzitsidwa zinthu zonse.+ Monga mmene mwaphunzitsidwira, pitirizani kukhala ogwirizana+ naye. 28  Tsopano inu ana anga okondedwa,+ khalanibe ogwirizana+ naye, kuti akadzaonetsedwa,+ tidzakhale ndi ufulu wa kulankhula.+ Kutinso tisadzachititsidwe manyazi ndi kuchotsedwa kwa iye pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake. 29  Ngati mwadziwa kuti iye ndi wolungama,+ mwadziwa kuti aliyense wochita zolungama anabadwa kuchokera kwa iye.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 8.