Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Timoteyo 5:1-25

5  Usadzudzule mwamuna wachikulire mokalipa,+ koma umudandaulire ngati bambo ako. Amuna achinyamata uwadandaulire ngati abale ako,  ndipo akazi achikulire+ ngati amayi ako. Akazi achitsikana uwadandaulire ngati alongo ako,+ ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse oipa.  Lemekeza akazi amasiye amene alidi amasiye.+  Koma ngati mkazi wamasiye aliyense ali ndi ana kapena adzukulu, amenewo aphunzire kukhala odzipereka kwa Mulungu m’banja mwawo choyamba,+ mwa kubwezera kwa makolo+ ndi agogo awo zowayenerera, pakuti zimenezi zimakondweretsa Mulungu.+  Mkazi amene alidi wamasiye, amene akusowa womusamala,+ amadalira Mulungu+ ndipo amalimbikira mapembedzero ndi mapemphero usiku ndi usana.+  Koma amene amatsatira zilakolako zake kuti azikhutiritse,+ ndi wakufa+ ngakhale kuti ali ndi moyo.  Choncho, uziwapatsa malamulo amenewa+ nthawi zonse kuti asakhale ndi chifukwa chowanenezera.+  Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira,+ makamaka a m’banja lake,+ wakana+ chikhulupiriro+ ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.  Mkazi wamasiye wolembedwa pamndandanda wa akazi amasiye, akhale wazaka zoposa 60. Akhale amene anali wokhulupirika kwa mwamuna wake,*+ 10  wodziwika kuti anachita ntchito zabwino,+ analera bwino ana,+ anali kuchereza alendo,+ anasambitsa mapazi a oyera,+ anathandiza ena m’masautso,+ ndiponso anali kugwira mwakhama ntchito iliyonse yabwino.+ 11  Koma usalole kuika akazi amasiye achitsikana pamndandanda umenewu, pakuti chilakolako chawo chofuna mwamuna chikaima pakati pa iwo ndi Khristu,+ amafuna kukwatiwa. 12  Zikatero, amapezeka olakwa chifukwa sanasunge chikhulupiriro chimene anasonyeza poyamba.+ 13  Komanso pa nthawi yomweyo, amayamba chizolowezi chomangokhala osachita kanthu, n’kumangoyendayenda m’makomo mwa anzawo. Kuwonjezera pa kumangokhala osachita kanthu, amakhalanso amiseche ndi olowerera nkhani za eni,+ n’kumalankhula zimene sayenera kulankhula. 14  Choncho ndimafuna kuti akazi amasiye achitsikana azikwatiwa,+ azibereka ana,+ ndi kusamalira banja, kuti wotsutsa asapeze chifukwa chonenera zachipongwe.+ 15  Ndipotu ena apatutsidwa kale moti ayamba kutsatira Satana. 16  Ngati mkazi aliyense wokhulupirira ali ndi achibale amene ndi akazi amasiye, aziwathandiza,+ kuti akazi amasiyewo asakhale cholemetsa ku mpingo. Zikatero, mpingowo ungathe kuthandiza amene alidi akazi amasiye.+ 17  Akulu otsogolera+ bwino apatsidwe ulemu waukulu,+ makamaka amene amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.+ 18  Pakuti lemba limati: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+ Komanso limati: “Wantchito ayenera kulandira malipiro ake.”+ 19  Usavomereze mlandu woneneza mkulu, kupatulapo ngati pali umboni wa mboni ziwiri kapena zitatu.+ 20  Anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo,+ uwadzudzule+ pamaso pa onse kuti ena onse akhale ndi mantha.+ 21  Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu+ ndiponso angelo ochita kusankhidwa, kuti uzitsatira malangizo amenewa popanda kuweruziratu. Usachite kanthu ndi maganizo okondera.+ 22  Usafulumire kuika munthu aliyense pa udindo,*+ kapena kugawana ndi anthu ena machimo awo.+ Pitiriza kukhala ndi khalidwe loyera.+ 23  Usamangomwa madzi okha, koma uzimwanso vinyo pang’ono,+ chifukwa cha vuto lako la m’mimba ndi kudwaladwala kwako kuja. 24  Machimo a anthu ena amaonekera poyera,+ ndipo zimenezi zimachititsa kuti aweruzidwe. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pambuyo pake.+ 25  Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera,+ ndipo ngakhale kuti zisaonekere sizingabisike mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mkazi wa mwamuna mmodzi.”
Kapena kuti, “kuika manja ako pamunthu.”