Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Samueli 8:1-22

8  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Samueli atakalamba anaika+ ana ake aamuna kukhala oweruza mu Isiraeli.  Mwana wake woyamba dzina lake anali Yoweli,+ ndipo mwana wake wachiwiri anali Abiya.+ Amenewa anali oweruza ku Beere-seba.  Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake,+ koma anali okonda kupeza phindu mwachinyengo,+ ndipo anali kulandira ziphuphu+ ndi kupotoza chiweruzo.+  Patapita nthawi, akulu onse a mu Isiraeli+ anasonkhana pamodzi n’kupita kwa Samueli ku Rama.  Atafika kumeneko anamuuza kuti: “Iweyo wakalamba, koma ana ako sakutsatira chitsanzo chako. Ndiye tikufuna kuti utiikire mfumu+ yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.”  Koma zimenezi zinamuipira Samueli, chifukwa iwo anati: “Utipatse mfumu yoti izitiweruza.” Pamenepo Samueli anayamba kupemphera kwa Yehova.+  Poyankha, Yehova anauza Samueli+ kuti: “Mvera zonse zimene anthuwo akunena kwa iwe,+ pakuti sanakane iweyo koma akana ine kuti ndisakhale mfumu yawo.+  Zinthu zonse zimene akhala akuchita kuyambira pa tsiku limene ndinawatulutsa mu Iguputo+ mpaka lero, kundisiya+ n’kumakatumikira milungu ina,+ n’zimenenso akuchitira iwe.  Choncho mvera mawu awo. Koma uwachenjeze mwamphamvu, ndipo uwauze zimene mfumu imene iziwalamulirayo izidzafuna kwa iwo.”+ 10  Samueli anafotokozera anthu amene anali kum’pempha kuti awaikire mfumuwo mawu onse a Yehova. 11  Iye anawauza kuti: “Izi ndi zimene mfumu yokulamuliraniyo izidzafuna kwa inu:+ Idzatenga ana anu+ kuti azikayenda m’magaleta*+ ake ndi kukwera pamahatchi*+ ake, ndipo ena mwa ana anuwo azidzathamanga patsogolo pa magaleta ake.+ 12  Idzaika anthu ena kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake+ ndi kukolola mbewu zake,+ ndiponso ena azidzapanga zida zake zankhondo+ ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+ 13  Ana anu aakazi idzawatenga kuti akakhale opanga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi opanga mkate.+ 14  Mfumuyo idzakulandani minda yanu yabwino kwambiri, minda ya mbewu, ya mpesa+ ndi ya maolivi+ n’kupatsa antchito ake. 15  Idzatenganso gawo limodzi mwa magawo 10+ a zokolola za m’minda yanu ya mbewu ndi ya mpesa, n’kuzipereka kwa nduna za panyumba ya mfumu+ ndi kwa antchito ake. 16  Antchito anu aamuna, antchito anu aakazi, abusa anu aluso kwambiri ndi abulu anu idzawatenganso kuti ikawagwiritse ntchito.+ 17  Pa zoweta zanu+ idzatengapo gawo limodzi mwa magawo 10, ndipo inuyo mudzakhala antchito ake. 18  Ndipo mudzalira pa tsiku limenelo chifukwa cha mfumu yanu+ imene mwadzisankhira nokha, koma Yehova sadzakuyankhani.”+ 19  Koma anthuwo anakana kumvera mawu a Samueli+ ndipo anati: “Ife tikufuna kuti mfumu izitilamulira. 20  Ifenso tikufuna kukhala ngati mitundu ina yonse,+ ndipo mfumu yathuyo ndi imene izitiweruza ndi kutitsogolera kukamenya nkhondo zathu.” 21  Samueli anamvera mawu onse amene anthuwo ananena, kenako anafotokozera Yehova mawuwo.+ 22  Zitatero Yehova anauza Samueli kuti: “Mvera mawu awo ndipo uwaikire mfumu yoti iziwalamulira.”+ Chotero Samueli anauza amuna a Isiraeli kuti: “Aliyense wa inu apite kumzinda wakwawo.”

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”