Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Petulo 1:1-25

1  Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu,+ amene muli alendo osakhalitsa,+ amene mwamwazikana+ ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia, ndi ku Bituniya.  Ndikukulemberani inu amene Mulungu Atate+ anakudziwiranitu mwa kukuyeretsani ndi mzimu+ kuti mukhale omvera ndi owazidwa+ magazi a Yesu Khristu, kuti:+ Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere ziwonjezeke kwa inu.+  Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ pakuti mwachifundo chake chachikulu, anatibereka mwatsopano+ kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo+ mwa kuukitsidwa+ kwa Yesu Khristu.  Anatibereka kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka,+ chosadetsedwa ndiponso chosasuluka. Cholowa chimenechi anasungira inuyo kumwamba,+  inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro.+ Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso,+ ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera+ mu nthawi ya mapeto.+  Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti padakali pano n’koyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana amene akukuchititsani chisoni.+  Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu, chimene chayesedwa+ ndipo n’chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa m’moto,+ chidzakuchititseni kutamandidwa ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, zochita za Yesu Khristu zikadzaululika.*+  Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda.+ Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chachikulu ndiponso chosaneneka,  popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.+ 10  Aneneri amene analosera+ za kukoma mtima kwakukulu kumene munali kudzasonyezedwa,+ anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndi mosamala.+ 11  Anali kufufuza nyengo+ yake kapena mtundu wa nyengo imene mzimu+ umene unali mwa iwo unali kuwasonyeza yokhudzana ndi Khristu.+ Mzimuwo unali kuchitira umboni za masautso a Khristu+ ndi za ulemerero+ wobwera pambuyo pake. 12  Zinaululidwa kwa iwo kuti sanali kudzitumikira okha,+ koma anali kutumikira inu mwa zinthu zimene tsopano zalengezedwa+ kwa inu. Zimenezi zalengezedwa kwa inu ndi olengeza uthenga wabwino, mwa mzimu woyera+ wotumizidwa kuchokera kumwamba. M’zinthu zimenezi angelo akulakalaka kusuzumiramo.+ 13  Konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu,+ khalanibe oganiza bwino,+ ndipo ikani chiyembekezo chanu pa kukoma mtima kwakukulu+ kumene kudzafika kwa inu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+ 14  Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira+ zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. 15  Koma khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse,+ 16  chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+ 17  Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+ 18  Pajatu mukudziwa kuti sizinali zinthu zotha kuvunda,+ siliva kapena golide, zimene zinakumasulani+ ku khalidwe lanu lopanda phindu limene munalilandira kuchokera kwa makolo anu mwa chikhalidwe chanu. 19  Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali,+ monga a nkhosa yopanda chilema ndi yopanda mawanga,+ magazi a Khristu.+ 20  Iye anadziwikiratu dziko lisanakhazikitsidwe,+ koma anaonekera pa nthawi ya mapeto chifukwa cha inuyo,+ 21  amene kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu,+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kum’patsa ulemerero,+ kuti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu.+ 22  Tsopano, popeza mwayeretsa+ miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo,+ kondanani kwambiri kuchokera mumtima.+ 23  Pakuti inu mwabadwa mwatsopano,+ osati kuchokera m’mbewu yotha kuwonongeka,+ koma m’mbewu+ yosatha kuwonongeka,+ kudzera m’mawu+ a Mulungu wamoyo ndi wamuyaya.+ 24  Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa la udzu.+ Udzuwo umafota ndipo duwalo limathothoka,+ 25  koma mawu a Yehova amakhala kosatha.”+ “Mawu”+ amenewo ndi amene alengezedwa+ kwa inu monga uthenga wabwino.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Yesu Khristu akadzaululika.”
Mawu ake enieni, “akadzaululika.”