Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Mbiri 4:1-43

4  Ana a Yuda anali Perezi,+ Hezironi,+ Karami,+ Hura,+ ndi Sobala.+  Reyaya+ mwana wa Sobala anabereka Yahati. Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Amenewa ndiwo anali mabanja a Azorati.+  Tsopano awa ndiwo ana a bambo wa Etami:+ Yezereeli,+ Isima, Idibasi, (dzina la mlongo wawo linali Hazeleleponi,)  Penueli bambo wa Gedori,+ ndi Ezeri bambo wa Husa. Amenewa ndiwo anali ana a Hura+ mwana woyamba wa Efurata, ndipo Hura anali bambo wa Betelehemu.+  Ashari+ bambo wa Tekowa+ anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.  M’kupita kwa nthawi Naara anam’berekera Ahuzamu, Heferi, Temeni, ndi Hahasitari. Amenewa ndiwo anali ana a Naara.  Ana a Hela anali Zereti, Izara, ndi Etani.  Kozi anabereka Anubu, Zobeba, ndi mabanja a Ahaheli mwana wa Harumu.  Yabezi+ anali wolemekezeka kwambiri+ kuposa abale ake, ndipo mayi ake ndiwo anamutcha Yabezi,* chifukwa anati: “Ndam’bereka ndikumva ululu.”+ 10  Tsopano Yabezi anayamba kuitana Mulungu+ wa Isiraeli, kuti: “Mukandidalitsa+ ndi kukulitsa dziko langa,+ ndipo dzanja lanu+ likakhala nane, komanso mukanditeteza ku tsoka,+ kuti lisandivulaze,+ . . .” Choncho Mulungu anakwaniritsa zimene iye anapempha.+ 11  Kelubu m’bale wake wa Suha anabereka Mehiri, yemwe anali bambo wa Esitoni. 12  Esitoni anabereka Beti-rafa, Paseya, ndi Tehina bambo wa Iri-nahasi. Amenewa anali amuna a ku Reka. 13  Ana a Kenazi+ anali Otiniyeli+ ndi Seraya, ndipo mwana wa Otiniyeli anali Hatati. 14  Meyonatai anabereka Ofira. Seraya anabereka Yowabu bambo wa Ge-harasimu,* chifukwa iwo anakhala amisiri.+ 15  Ana a Kalebe+ mwana wa Yefune+ anali Iru, Ela, ndi Naamu. Mwana wa Ela anali Kenazi. 16  Ana a Yehaleleli anali Zifi, Zifa, Tiriya, ndi Asareli. 17  Ana a Ezira anali Yeteri, Meredi, Eferi, ndi Yaloni. Mkaziyo anabereka Miriamu, Samai, ndi Isiba bambo wa Esitemowa.+ 18  Mkazi wake wachiyuda anabereka Yeredi bambo wa Gedori, Hiberi bambo wa Soko, ndi Yekutieli bambo wa Zanowa. Amenewa anali ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anam’kwatira. 19  Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, anali bambo wa Keila+ Mgarimi, ndi Esitemowa Mmaakati. 20  Ana a Shimoni anali Aminoni, Rina, Beni-hanani, ndi Tiloni. Ana a Isi anali Zoheti ndi Beni-zoheti. 21  Ana a Shela+ mwana wa Yuda anali Ere bambo wa Leka, Laada bambo wa Maresha, ndi mabanja a nyumba ya anthu ogwira ntchito yopanga nsalu zabwino kwambiri,+ a nyumba ya Asibeya, 22  Yokimu, amuna a ku Kozeba, Yowasi, ndi Sarafa, (amenewa anakwatira akazi achimowabu),+ ndi Yasubi-lehemu. Nkhani zimenezi zachokera m’zolembedwa zakale.+ 23  Iwo anali oumba zinthu+ okhala ku Netaimu ndi ku Gedera. Ankakhala kumeneko n’kumagwirira ntchito mfumu.+ 24  Ana a Simiyoni anali Nemueli,+ Yamini,+ Yaribi, Zera, ndi Shauli.+ 25  Shauli anabereka Salumu, Salumu anabereka Mibisamu, Mibisamu anabereka Misima, 26  Misima anabereka Hamueli, Hamueli anabereka Zakuri, Zakuri anabereka Simeyi. 27  Simeyi anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake analibe ana ambiri. Palibe banja lawo lililonse limene linali ndi ana ambiri ngati mabanja a ana a Yuda.+ 28  Iwo anapitiriza kukhala ku Beere-seba,+ ku Molada,+ ku Hazara-suali,+ 29  ku Biliha,+ ku Ezemu,+ ku Toladi,+ 30  ku Betuele,+ ku Horima,+ ku Zikilaga,+ 31  ku Beti-marikaboti, ku Hazara-susimu,+ ku Beti-biri, ndi ku Saaraimu.+ Imeneyi inali mizinda yawo kufikira pamene Davide anayamba kulamulira. 32  Midzi yawo inali Etami, Aini, Rimoni, Tokeni, ndi Asani.+ Mizinda isanu. 33  Midzi yawo yonse yozungulira mizinda imeneyi inakafika mpaka ku Baala.+ Awa anali malo awo okhala ndi mndandanda wa mayina awo wotsatira makolo. 34  Ana ena a Simiyoni anali: Mesobabu, Yameleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35  Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, Yosibiya mwana wa Seraya, Seraya mwana wa Asieli, 36  Elioenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, 37  Ziza mwana wa Sifi, Sifi mwana wa Aloni, Aloni mwana wa Yedaya, Yedaya mwana wa Simuri, ndi Simuri mwana wa Semaya. 38  Amene atchulidwa mayinawa anali atsogoleri pamabanja awo,+ ndipo banja la makolo awo linakula kwambiri. 39  Iwo anapita kuchipata cha mzinda wa Gedori mpaka kukafika kum’mawa kwa chigwa, kukafuna msipu wa ziweto zawo. 40  Pomaliza pake anapeza msipu wabwino kwambiri,+ ndipo dzikolo linali lalikulu. Linali pa mtendere, lopanda chosokoneza chilichonse,+ chifukwa anthu amene ankakhala kumeneko kale anali mbadwa za Hamu.+ 41  Anthu otchulidwa mayinawa anapita kumeneko m’masiku a Hezekiya+ mfumu ya Yuda n’kukagwetsa+ mahema a Ahamu, n’kupha Ameyuni amene anali kumeneko. Anawawononga+ anthuwo, ndipo iwo kulibe mpaka lero. Kenako iwo anayamba kukhala kumeneko m’malo mwawo, chifukwa kunali msipu+ wa ziweto zawo. 42  Pakati pawo panali ana ena a Simiyoni, amuna okwana 500, amene anapita kuphiri la Seiri.+ Atsogoleri awo anali Pelatiya, Neariya, Refaya, ndi Uziyeli ana a Isi. 43  Iwo anapha Aamaleki+ otsala omwe anathawa, ndipo akukhala kumeneko mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Dzina limeneli likuchokera ku mawu amene m’Chiheberi amatanthauza “ululu.”
Dzinali limatanthauza, “Chigwa cha Amisiri.”