Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Mbiri 27:1-34

27  Tsopano nawa magulu a Aisiraeli amene anali m’gulu la asilikali a mfumu. M’magulu amenewa munali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ atsogoleri+ a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100,+ ndi atsogoleri amene anali kusamalira magulu amenewa. Maguluwa anali kusinthanasinthana mwezi uliwonse pa chaka kutumikira+ mfumu, ndipo gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa gulu loyamba, la mwezi woyamba, anali Yasobeamu+ mwana wa Zabidiyeli. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Ana ena a Perezi+ anali akuluakulu a anthu amene anali kutumikira monga atsogoleri a asilikali. Nawonso ankatumikira mwezi woyamba.  Woyang’anira wa gulu la mwezi wachiwiri anali Dodai+ Muahohi,+ ndipo Mikiloti anali mtsogoleri wawo. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa gulu lachitatu, lotumikira mwezi wachitatu, anali Benaya+ mwana wa Yehoyada+ wansembe wamkulu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Benaya+ ameneyu anali mwamuna wamphamvu pa amuna 30+ komanso anali mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Pagulu lakelo, mwana wake Amizabadi ndiye anali mtsogoleri.  Mtsogoleri wachinayi, wa mwezi wachinayi, anali Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu,+ ndipo mwana wake Zebadiya anabwera pambuyo pake. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wachisanu, wa mwezi wachisanu, anali Samuti+ Mwizirahiya. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa 6, wa mwezi wa 6, anali Ira+ mwana wa Ikesi+ Mtekowa.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 10  Mtsogoleri wa 7, wa mwezi wa 7, anali Helezi+ Mpeloni,+ wochokera mwa ana a Efuraimu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 11  Mtsogoleri wa 8, wa mwezi wa 8, anali Sibekai+ Mhusati, wochokera mwa Azera.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 12  Mtsogoleri wa 9, wa mwezi wa 9, anali Abi-ezeri+ Muanatoti,+ wochokera mwa Abenjamini. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 13  Mtsogoleri wa 10, wa mwezi wa 10, anali Maharai+ Mnetofa, wochokera mwa Azera.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 14  Mtsogoleri wa 11, wa mwezi wa 11, anali Benaya+ Mpiratoni, wochokera mwa ana a Efuraimu.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 15  Mtsogoleri wa 12, wa mwezi wa 12, anali Heledai+ Mnetofa wa kubanja la Otiniyeli. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 16  Tsopano nawa atsogoleri a mafuko a ana a Isiraeli:+ Mtsogoleri wa Arubeni anali Eliezere mwana wa Zikiri, wa Asimiyoni anali Sefatiya mwana wa Maaka, 17  wa Alevi anali Hasabiya mwana wa Kemueli, wa ana a Aroni anali Zadoki,+ 18  wa Ayuda anali Elihu+ mmodzi wa abale ake a Davide,+ wa Aisakara anali Omuri mwana wa Mikayeli, 19  wa Azebuloni anali Isimaya mwana wa Obadiya, wa Anafitali anali Yerimoti mwana wa Azirieli, 20  wa ana a Efuraimu anali Hoshiya mwana wa Azaziya, wa hafu ya fuko la Manase anali Yoweli mwana wa Pedaya, 21  wa hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi anali Ido mwana wa Zekariya, wa Abenjamini anali Yaasiyeli mwana wa Abineri,+ 22  ndipo mtsogoleri wa fuko la Dani anali Azareli mwana wa Yerohamu. Amenewa anali akalonga+ a mafuko a Isiraeli. 23  Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka 20 kutsika m’munsi, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisiraeli ngati nyenyezi zakumwamba.+ 24  Yowabu+ mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga anthu koma sanamalize.+ Kenako mkwiyo+ wa Mulungu unagwera Isiraeli chifukwa chowerenga anthuwo, ndipo chiwerengerocho sichinalembedwe pa zochitika za m’masiku a Mfumu Davide. 25  Azimaveti mwana wa Adieli anali kuyang’anira chuma cha mfumu.+ Yonatani mwana wa Uziya anali kuyang’anira chuma chosungidwa m’madera apafupi,+ m’mizinda,+ m’midzi ndi m’nyumba zosanja. 26  Eziri mwana wa Kelubu anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yolima minda.+ 27  Simeyi wa ku Rama anali woyang’anira minda ya mpesa,+ koma Zabidi wa ku Sifimi anali woyang’anira zinthu zonse zokhudza vinyo za m’minda ya mpesayo. 28  Baala-hanani Mgederi anali woyang’anira mitengo ya maolivi ndi ya mkuyu+ imene inali ku Sefela,+ ndipo Yowasi anali kuyang’anira mafuta.+ 29  Sitirai wa ku Sharoni+ anali kuyang’anira zoweta zimene anali kudyetsera ku Sharoni. Safati mwana wa Adilai anali kuyang’anira zoweta zimene zinali kuzigwa. 30  Obili Mwisimaeli+ anali kuyang’anira ngamila.+ Yedeya Mmeronoti anali kuyang’anira abulu aakazi. 31  Ndipo Yazizi Mhagara anali woyang’anira nkhosa. Anthu onsewa anali oyang’anira katundu wa Mfumu Davide. 32  Yonatani,+ mwana wa m’bale wake wa Davide, anali phungu wanzeru+ komanso mlembi. Yehiela mwana wa Hakimoni+ ndiye anali kuyang’anira ana a mfumu.+ 33  Ahitofeli+ anali phungu+ wa mfumu ndipo Husai+ Mwareki+ anali mnzake wa mfumu.+ 34  Kuwonjezera pa Ahitofeli panalinso Yehoyada mwana wa Benaya+ ndi Abiyatara,+ ndipo Yowabu+ anali mkulu wa asilikali a mfumu.

Mawu a M'munsi