Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Mbiri 26:1-32

26  Tsopano awa ndiwo magulu a alonda a pazipata:+ Pa mbadwa za Kora+ panali Meselemiya,+ mwana wa Kore wochokera mwa ana a Asafu.  Ndipo ana a Meselemiya anali awa: Woyamba anali Zekariya, wachiwiri Yediyaeli, wachitatu Zebadiya, wachinayi Yatiniyeli,  wachisanu Elamu, wa 6 Yehohanani, ndipo wa 7 anali Eliho-enai.  Obedi-edomu+ anali ndi ana awa: Woyamba anali Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinayi Sakari, wachisanu Netaneli,  wa 6 Amiyeli, wa 7 Isakara, ndipo wa 8 anali Peuletai, pakuti Mulungu anamudalitsa.+  Semaya mwana wa Obedi-edomu anabereka ana omwe anali olamulira nyumba ya bambo wawo, popeza anawo anali amuna odalirika ndi amphamvu.  Ana a Semaya anali Otini, Refaeli, Obedi, ndi Elizabadi. Elizabadi anali ndi abale ake odalirika, Elihu ndi Semakiya.  Onsewa anali mbadwa za Obedi-edomu. Iwowa, ana awo ndi abale awo anali odalirika ndi amphamvu potumikira. Onsewa, ochokera mwa Obedi-edomu, analipo 62.  Meselemiya+ anali ndi ana komanso abale ake, amuna odalirika okwanira 18. 10  Hosa, wochokera mwa ana a Merari anali ndi ana. Simuri anali mtsogoleri wa anawo ngakhale kuti sanali woyamba kubadwa,+ koma bambo akewo ndiwo anamusankha kukhala mtsogoleri.+ 11  Wachiwiri anali Hilikiya, wachitatu Tebaliya, ndipo wachinayi anali Zekariya. Ana onse a Hosa kuphatikizapo abale ake, analipo 13. 12  Pa magulu a alonda a pazipatawa, ntchito ya atsogoleri awo inali yofanana ndi ya abale awo,+ ndipo inali yotumikira panyumba ya Yehova. 13  Choncho anachita maere+ ofanana kwa wamng’ono ndi wamkulu potsata nyumba za makolo awo,+ kuti apeze ogwira ntchito pachipata chilichonse. 14  Maere a kum’mawa anagwera Selemiya.+ Anachitanso maere a Zekariya+ mwana wake, yemwe anali phungu+ wanzeru, ndipo maere ake anali oti akhale kumpoto.+ 15  Maere a Obedi-edomu anagwera kum’mwera, ndipo ana ake+ anaikidwa kuti azilondera nyumba zosungiramo zinthu.+ 16  Maere a Supimu ndi a Hosa+ anagwera kumadzulo pafupi ndi Chipata cha Saleketi, pamsewu wopita kumtunda. Gulu limodzi la alonda+ linakhala moyandikana ndi gulu lina la alonda.+ 17  Kum’mawa kunali Alevi 6, kumpoto anayi pa tsiku, kum’mwera anayi pa tsiku,+ ndipo kunyumba zosungiramo katundu+ awiriawiri. 18  Kukhonde la kumadzulo kumsewu, kunali anayi+ ndipo pakhonde panali awiri. 19  Amenewa anali magulu a alonda a pazipata a ana a mbadwa za Kora+ ndi mbadwa za Merari.+ 20  Kumbali ya Alevi, Ahiya anali kuyang’anira chuma+ cha m’nyumba ya Mulungu woona, ndi chuma cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika.+ 21  Pa ana a Ladani,+ panali Yehieli.+ Ana amenewo anali mbadwa za Agerisoni kudzera mwa Ladani, ndipo anali atsogoleri a nyumba za makolo za Ladani Mgerisoni. 22  Ana a Yehieli anali Zetamu ndi Yoweli+ m’bale wake. Amenewa anali kuyang’anira chuma+ cha m’nyumba ya Yehova. 23  Panalinso mbadwa za Amuramu, za Izara, za Heburoni, ndi za Uziyeli,+ 24  ndipo Sebueli+ mwana wa Gerisomu mwana wa Mose, anali mtsogoleri panyumba zosungiramo katundu. 25  Abale ake obadwa mwa Eliezere,+ anali Rehabiya+ mwana wa Eliezere, Yesaiya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake, ndi Selomoti mwana wake. 26  Selomoti ameneyu pamodzi ndi abale ake anali kuyang’anira chuma chonse cha zinthu zimene anaziyeretsa kukhala zopatulika. Amene anayeretsa zinthu zimenezi kukhala zopatulika+ anali Davide+ mfumu, atsogoleri a nyumba za makolo,+ atsogoleri a magulu a anthu 1,000, a magulu a anthu 100, ndi atsogoleri a asilikali. 27  Anayeretsa zinthu zimene anazitenga kunkhondo+ ndiponso zofunkha+ kuti azizigwiritsa ntchito panyumba ya Yehova. 28  Panalinso zinthu zonse zimene Samueli wamasomphenya,+ Sauli mwana wa Kisi, Abineri+ mwana wa Nera, ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ anaziyeretsa kukhala zopatulika. Chilichonse chimene munthu anachiyeretsa chinali kuyang’aniridwa ndi Selomiti ndi abale ake. 29  Kumbali ya mbadwa za Izara,+ panali Kenaniya ndi ana ake omwe anali akapitawo ndi oweruza+ Isiraeli, koma ntchito yawoyi sinali ya pakachisi.+ 30  Kumbali ya Aheburoni,+ panali Hasabiya ndi abale ake, amuna odalirika+ okwanira 1,700. Iwowa anali ndi ntchito yoyang’anira Aisiraeli m’chigawo cha Yorodano kumadzulo, pa ntchito zonse za Yehova ndiponso pa ntchito zotumikira mfumu. 31  Kumbali ya Aheburoni kunalinso Yereya+ mtsogoleri wa Aheburoniwo malinga ndi mibadwo ya makolo awo. M’chaka cha 40+ cha ufumu wa Davide, iwo anafunafuna anthu ndipo anapeza amuna amphamvu ndi olimba mtima pakati pawo ku Yazeri+ ku Giliyadi.+ 32  Ndipo abale a Yereya, amuna odalirika+ komanso atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ analipo 2,700. Choncho mfumu Davide inawaika kuti aziyang’anira Arubeni, Agadi ndi hafu ya fuko la Manase+ pa nkhani iliyonse+ yokhudza Mulungu woona ndiponso yokhudza mfumu.

Mawu a M'munsi