Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mbiri 24:1-31

24  Tsopano anagawa ana a Aroni m’magulu awo. Ana a Aroni anali Nadabu,+ Abihu,+ Eleazara,+ ndi Itamara.+  Nadabu ndi Abihu+ anamwalira opanda ana aamuna bambo awo akali ndi moyo,+ koma Eleazara+ ndi Itamara anapitiriza kukhala ansembe.  Davide ndi Zadoki,+ yemwe anali wochokera mwa ana a Eleazara, ndiponso Ahimeleki,+ wochokera mwa ana a Itamara, anagawa ana a Aroniwo m’magulu a udindo pa utumiki wawo.+  Koma ana a Eleazara anapezeka kuti anali ndi atsogoleri ambiri kuposa ana a Itamara. Choncho ana a Eleazara, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anawagawa m’magulu 16. Ndiponso ana a Itamara, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, anawagawa m’magulu 8.  Pogawapo, anachita maere+ panyumba ya Eleazara pamodzi ndi panyumba ya Itamara. Anachita zimenezi chifukwa chakuti panafunika atsogoleri a pamalo oyera,+ ndi atsogoleri otumikira Mulungu woona, ochokera mwa ana a Eleazara ndiponso ochokera mwa ana a Itamara.  Kenako Semaya mwana wa Netaneli mlembi+ wa Alevi, anawalemba mayina pamaso pa mfumu, akalonga, wansembe Zadoki,+ Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara,+ ndiponso pamaso pa atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi.+ Anali kutenga nyumba imodzi ya makolo ya Eleazara+ ndi nyumba imodzi ya makolo ya Itamara.+  Atachita maere, zotsatira zake zinali motere: Woyamba anali Yehoyaribu,+ wachiwiri Yedaya,  wachitatu Harimu, wachinayi Seorimu,  wachisanu Malikiya, wa 6 Miyamini, 10  wa 7 Hakozi, wa 8 Abiya,+ 11  wa 9 Yesuwa, wa 10 Sekaniya, 12  wa 11 Eliyasibu, wa 12 Yakimu, 13  wa 13 Hupa, wa 14 Yesebeabu, 14  wa 15 Biliga, wa 16 Imeri, 15  wa 17 Heziri, wa 18 Hapizezi, 16  wa 19 Petahiya, wa 20 Yehezikeli, 17  wa 21 Yakini, wa 22 Gamuli, 18  wa 23 Delaya, ndipo wa 24 anali Maaziya. 19  Limeneli ndilo linali dongosolo+ la utumiki wawo,+ kuti azilowa m’nyumba ya Yehova malinga ndi mphamvu imene anapatsidwa+ kudzera m’dzanja la Aroni kholo lawo, monga mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli anamulamulira. 20  Ana a Levi amene anatsala anali motere: Pa ana a Amuramu+ panali Subaeli.+ Pa ana a Subaeli panali Yedeya. 21  Panalinso Rehabiya:+ Pa ana a Rehabiya panali Isiya mtsogoleri wawo. 22  Mwa mbadwa za Izara,+ panali Selomoti.+ Pa ana a Selomoti panali Yahati. 23  Ana a Heburoni+ anali Yeriya+ mtsogoleri wawo, Amariya wachiwiri, Yahazieli wachitatu, ndi Yekameamu wachinayi. 24  Pa ana a Uziyeli panali Mika. Pa ana a Mika+ panali Samiri. 25  M’bale wake wa Mika anali Isiya, ndipo pa ana a Isiya panali Zekariya. 26  Ana a Merari+ anali Mali+ ndi Musi.+ Pa ana a Yaaziya panali Beno. 27  Pa ana a Merari panali Yaaziya. Ana a Yaaziya anali Beno, Sohamu, Zakuri, ndi Ibiri. 28  Pa ana a Mali panali Eleazara amene analibe mwana.+ 29  Panalinso Kisi: Pa ana a Kisi panali Yerameeli. 30  Ana a Musi anali Mali,+ Ederi, ndi Yerimoti.+ Amenewa anali ana a Alevi potsata nyumba za makolo awo.+ 31  Iwonso anachita maere+ mofanana ndi mmene abale awo, ana a Aroni, anachitira pamaso pa Davide mfumu, Zadoki, Ahimeleki, ndiponso pamaso pa atsogoleri a nyumba za makolo za ansembe ndi za Alevi. Nyumba ya makolo+ ya wamkulu inali chimodzimodzi ndi nyumba ya makolo ya wamng’ono.

Mawu a M'munsi