Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mbiri 23:1-32

23  Davide anali atakalamba+ ndiponso atakhutira ndi masiku a moyo wake. Chotero analonga mwana wake Solomo+ kukhala mfumu ya Isiraeli.  Kenako anasonkhanitsa akalonga onse+ a Isiraeli komanso ansembe+ ndi Alevi.+  Atatero, Alevi anawerengedwa kuyambira azaka 30 kupita m’tsogolo.+ Anawerenga mwamuna aliyense wamphamvu, mmodzi ndi mmodzi,* ndipo onse anakwana 38,000.  Pakati pawo panali oyang’anira ntchito ya panyumba ya Yehova okwana 24,000. Akapitawo+ ndi oweruza+ analipo 6,000.  Panalinso alonda 4,000 a pachipata+ ndi anthu 4,000 oimbira Yehova zitamando+ ndi zoimbira+ zimene Davide anati, “Zimenezi ndazipanga kuti tizitamandira Mulungu.”  Ndiyeno Davide anawagawa m’magulu+ ndi kuwapereka kwa ana a Levi.+ Anawapereka kwa Gerisoni, Kohati, ndi Merari.  M’banja la Gerisoni munali Ladani ndi Simeyi.  Ana a Ladani anali atatu. Panali Yehiela+ mtsogoleri wawo, Zetamu ndi Yoweli.+  Ana a Simeyi anali atatu. Panali Selomoti, Hazieli ndi Harana. Amenewa anali atsogoleri a nyumba ya makolo ya Ladani. 10  Ana a Simeyi anali Yahati, Zina,* Yeusi, ndi Beriya. Ana anayiwa anali a Simeyi. 11  Yahati anali mtsogoleri wawo, ndipo wachiwiri wake anali Ziza. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri aamuna, choncho anakhala nyumba imodzi ya makolo+ ndiponso gulu limodzi lokhala ndi udindo wofanana. 12  Ana a Kohati+ analipo anayi. Panali Amuramu, Izara,+ Heburoni+ ndi Uziyeli.+ 13  Ana aamuna a Amuramu anali Aroni+ ndi Mose.+ Koma Aroni anapatulidwa+ kuti iye ndi ana ake aziyeretsa Malo Oyera Koposa,+ mpaka kalekale. Komanso kuti azifukiza nsembe+ yautsi pamaso pa Yehova, kumutumikira,+ ndi kupereka madalitso+ m’dzina lake mpaka kalekale. 14  Ponena za Mose munthu wa Mulungu woona,+ ana ake anapitiriza kuwawerenga pamodzi ndi fuko la Levi.+ 15  Ana a Mose anali Gerisomu+ ndi Eliezere.+ 16  Ana a Gerisomu, mtsogoleri wawo anali Sebueli.+ 17  Ana a Eliezere, mtsogoleri wawo anali Rehabiya.+ Eliezere sanakhalenso ndi ana ena aamuna, koma Rehabiya anali ndi ana ochuluka kwambiri. 18  Ana a Izara,+ mtsogoleri wawo anali Selomiti.+ 19  Ana a Heburoni anali Yeriya amene anali mtsogoleri wawo, wachiwiri wake anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli, ndipo wachinayi anali Yekameamu.+ 20  Ana a Uziyeli+ anali Mika amene anali mtsogoleri wawo, ndipo Isiya anali wachiwiri wake. 21  Ana a Merari+ anali Mali ndi Musi.+ Ana a Mali anali Eleazara+ ndi Kisi. 22  Koma Eleazara anamwalira. Iye analibe ana aamuna koma aakazi. Choncho abale awo, ana a Kisi, anawatenga kukhala akazi awo.+ 23  Ana a Musi analipo atatu. Panali Mali, Ederi, ndi Yeremoti.+ 24  Amenewa ndiwo anali ana a Levi potsata nyumba ya makolo awo.+ Iwowa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, ndipo mmodzi ndi mmodzi anapatsidwa udindo potsata mndandanda wa mayina awo. Amenewa anali oti azigwira ntchito yotumikira+ panyumba ya Yehova kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo.+ 25  Davide anachita zimenezi popeza anati: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wapereka mpumulo kwa anthu ake,+ ndipo iye adzakhala mu Yerusalemu mpaka kalekale.+ 26  Ndipo Alevi sazinyamulanso chihema chopatulika kapena ziwiya zake zilizonse zogwiritsa ntchito potumikira kumeneko.”+ 27  Malinga ndi mawu omaliza+ a Davide, amenewa ndiwo ana a Levi amene anawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo. 28  Ntchito yawo inali yotumidwa ndi ana a Aroni+ pa utumiki wa panyumba ya Yehova m’mabwalo a nyumbayo,+ m’zipinda zodyeramo,+ pa ntchito yoyeretsa chinthu chilichonse chopatulika,+ ndiponso pa ntchito yotumikira panyumba ya Mulungu woona. 29  Anali kutumidwanso pa ntchito zokhudza mkate wosanjikiza,+ ufa wosalala+ wa nsembe yambewu, mikate yopyapyala+ yopanda chofufumitsa,+ makeke ophika m’chiwaya,+ ufa wokanya wosakaniza ndi mafuta,+ ndiponso miyezo yosiyanasiyana.+ 30  Analinso kutumikira m’mawa ulionse+ pa nthawi yoimirira+ kuti athokoze+ ndi kutamanda+ Yehova. Analinso kuchita zimenezi madzulo. 31  Anali kutumikiranso nthawi iliyonse yopereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo za chikondwerero.+ Nthawi zonse anali kutumikira popereka nsembezo kwa Yehova, malinga ndi ziwerengero zake, komanso potsata lamulo lake. 32  Ana a Leviwa analinso ndi ntchito yolondera+ chihema chokumanako, malo oyera,+ ndiponso yolondera abale awo, ana a Aroni, pa utumiki wa panyumba ya Yehova.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mutu ndi mutu.”
Ameneyu ndi Ziza wotchulidwa m’vesi 11.