Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mbiri 21:1-30

21  Tsopano Satana anayamba kulimbana ndi Isiraeli polimbikitsa+ Davide kuti awerenge Aisiraeli.  Chotero Davide anauza Yowabu+ ndi atsogoleri a anthu kuti: “Pitani mukawerenge+ Aisiraeli kuyambira ku Beere-seba+ mpaka ku Dani,+ ndipo mubweretse chiwerengero chawo kwa ine kuti ndidziwe kuchuluka kwawo.”+  Koma Yowabu anati: “Yehova awonjezere anthu ake kuwirikiza nthawi 100 pa chiwerengero chawo.+ Koma kodi mbuyanga mfumu, anthu onsewa si anu komanso si atumiki anu? Nanga n’chifukwa chiyani mbuyanga mukufuna kuchita zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mukufuna kupalamulitsa Isiraeli?”  Koma mawu a mfumu+ anaposa mawu a Yowabu moti Yowabu anachoka pamaso pa mfumu+ n’kuyenda mu Isiraeli yense. Kenako anabwerera ku Yerusalemu.+  Atafika kumeneko, Yowabu anapereka chiwerengero chonse cha anthu kwa Davide. Aisiraeli onse analipo 1,100,000, amuna ogwira lupanga,+ ndipo amuna a Yuda ogwira lupanga analipo 470,000.  Koma Yowabu sanawerenge+ a fuko la Levi+ ndi la Benjamini, chifukwa anali ataipidwa ndi mawu a mfumu.  Zinthu zimenezi zinali zoipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo anapha Aisiraeli.  Davide ataona zimenezo, anauza Mulungu woona kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano, chonde, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu,+ pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+  Pamenepo Yehova analankhula kwa Gadi,+ wamasomphenya wa Davide+ kuti: 10  “Pita, ukauze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndaika zilango zitatu pamaso pako.+ Sankha wekha chimodzi mwa zitatuzi chimene ukufuna kuti ndikuchitire.”’”+ 11  Choncho Gadi anapita kwa Davide+ ndi kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Sankhapo chimodzi: 12  Zaka zitatu za njala+ kapena miyezi itatu yoti adani anu akuseseni+ ndi kukuphani ndi lupanga lawo, kapenanso masiku atatu a lupanga la Yehova,+ lomwe ndi mliri+ umene udzagwe m’dziko lanu mpaka mngelo wa Yehova atasakaza+ madera onse a Isiraeli.’ Ndiye tandiuzani zoti ndikayankhe kwa Amene wanditumayo.” 13  Atamva zimenezo, Davide anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisautsa kwambiri. Chonde, ndilangidwe ndi Yehova,+ pakuti chifundo chake n’chochuluka,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+ 14  Pamenepo Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli, moti mu Isiraeli munafa anthu 70,000.+ 15  Kuwonjezera pamenepo, Mulungu woona anatumiza mngelo ku Yerusalemu kuti akawononge mzindawo.+ Mngeloyo atangoyamba kuwononga, Yehova anaona zimenezo ndi kumva chisoni chifukwa cha tsokalo,+ choncho anauza mngelo amene anali kuwonongayo kuti: “Basi pakwanira!+ Tsitsa dzanja lako tsopano.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehova uja anali ataimirira pafupi ndi malo opunthira mbewu a Orinani+ Myebusi.+ 16  Davide atakweza maso ake, anaona mngelo wa Yehova+ ataima m’malere, pakati padziko lapansi ndi kumwamba. Mngeloyo anali atagwira lupanga+ n’kuloza nalo Yerusalemu. Nthawi yomweyo, Davide ndi akulu amene anali naye, atavala ziguduli,*+ anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 17  Kenako Davide anauza Mulungu woona kuti: “Kodi si ine amene ndinalamula kuti awerenge anthu? Ndipo kodi si ine ndachimwa ndi kuchitadi cholakwa?+ Nanga nkhosazi+ zalakwa chiyani? Chonde Yehova Mulungu wanga, dzanja lanu likhale pa ine ndi panyumba ya bambo anga, koma mliriwu usakhale pa anthu anu.”+ 18  Ndiyeno mngelo wa Yehova anauza Gadi+ kuti auze Davide kuti Davideyo apite kumalo opunthira mbewu a Orinani Myebusi, n’kukamanga guwa lansembe la Yehova.+ 19  Choncho Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi amene anawanena m’dzina la Yehova.+ 20  Pamene zimenezi zinali kuchitika, Orinani+ anali akupuntha tirigu. Atatembenuka anaona mngelo, ndipo ana ake anayi amene anali naye limodzi anakabisala. 21  Davide uja anakafika kwa Orinani. Ndiye Orinani atakweza maso n’kuona Davide,+ nthawi yomweyo anachoka pamalo opunthira mbewu aja n’kukagwada pamaso pa Davide n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. 22  Kenako Davide anauza Orinani kuti: “Ndipatse malo ako opunthira mbewuwa kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwu+ uthe pakati pa anthuwa. Ndikupatsa ndalama+ zake zonse.”+ 23  Koma Orinani anauza Davide kuti: “Ingotengani malowa akhale anu,+ ndipo mbuyanga mfumu chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino. Taonani, ineyo ndipereka ng’ombe+ kuti zikhale nsembe zopsereza ndi chopunthira tirigu+ kuti chikhale nkhuni,+ ndiponso ndipereka tirigu kuti akhale nsembe yambewu. Ndikupereka zonsezi.”+ 24  Koma Mfumu Davide inauza Orinani kuti: “Iyayi, ineyo ndigula ndipo ndipereka ndalama zake zonse,+ chifukwa sindingatenge zinthu zako n’kupita nazo kwa Yehova kukapereka nsembe zopsereza popanda kulipira.” 25  Atatero, Davide anapatsa Orinani ndalama za malowo zolemera masekeli* 600 agolide.+ 26  Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamalopo,+ ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova+ yemwe tsopano anamuyankha ndi moto+ wochokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza. 27  Kenako Yehova analankhula ndi mngelo uja,+ ndipo mngeloyo anabwezera lupanga lake m’chimake. 28  Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pamalo opunthira mbewu a Orinani Myebusi, anapitiriza kuperekera nsembe pamalopo.+ 29  Koma pa nthawiyo, chihema chopatulika cha Yehova chimene Mose anapanga m’chipululu ndi guwa lansembe zopsereza, zinali pamalo okwezeka a ku Gibeoni.+ 30  Davide anali atasiya kupita kumeneko kukafunsira kwa Mulungu, chifukwa anali kuopa+ lupanga la mngelo wa Yehova.

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.