Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Mbiri 19:1-19

19  Kenako, Nahasi+ mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndipo mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwa bambo akewo.+  Zitachitika zimenezi, Davide anati: “Ndidzasonyeza Hanuni mwana wa Nahasi kukoma mtima kosatha,+ chifukwa bambo ake anandisonyeza kukoma mtima kosatha.”+ Chotero Davide anatumiza amithenga kuti akatonthoze Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo ake, ndipo atumiki a Davidewo anafika m’dziko la ana a Amoni+ kwa Hanuni kuti amutonthoze.  Koma akalonga a ana a Amoni anauza Hanuni kuti: “Kodi mukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthozani kuti alemekeze bambo anu pamaso panu? Kodi atumiki akewa sanabwere kwa inu kuti adzaonetsetse mzindawu ndi kuchita ukazitape,+ kuti adzaulande?”+  Pamenepo Hanuni anatenga atumiki a Davide+ aja ndi kuwameta ndevu.+ Kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza m’matako,+ n’kuwauza kuti azipita.+  Pambuyo pake anthu anauza Davide zimene zinachitikira atumiki ake aja, ndipo iye nthawi yomweyo anatumiza mthenga kuti akakumane nawo chifukwa atumikiwo anachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ kufikira ndevu zanu zitakula ndithu, kenako mudzabwere.”  Patapita nthawi, ana a Amoni anaona kuti akhala chinthu chonunkha+ kwa Davide. Choncho Hanuni+ ndi ana a Amoni anatumiza matalente* asiliva 1,000+ kuti akabwereke magaleta+ ndi kulemba ganyu asilikali okwera pamahatchi a ku Mesopotamiya, a ku Aramu-maaka+ ndi a ku Zoba.+  Chotero anakabwereka magaleta 32,000,+ ndi kulemba ganyu mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake.+ Zitatero, iwowa anafika ndi kumanga misasa yawo pafupi ndi Medeba.+ Ndipo ana a Amoni anatuluka m’mizinda yawo ndi kusonkhana kuti akamenye nkhondo.  Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza Yowabu+ ndi gulu lonse lankhondo pamodzi ndi amuna amphamvu.+  Ndiyeno ana a Amoni anapita kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuchipata cha mzinda. Ndipo mafumu+ amene anabwera aja anali okhaokha kutchire. 10  Yowabu ataona kuti asilikali a adani ake akubwera mofulumira kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo kudzamenyana naye, nthawi yomweyo anatenga amuna ochita kusankhidwa mwapadera a mu Isiraeli ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti akumane ndi Asiriya.+ 11  Anthu ena onse anawapereka m’manja mwa Abisai+ m’bale wake, kuti afole mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi kukumana ndi ana a Amoni.+ 12  Ndiyeno anamuuza kuti: “Asiriya+ akandiposa mphamvu, iweyo undipulumutse.+ Koma ana a Amoni akakukulira mphamvu, ineyo ndifika kudzakupulumutsa.+ 13  Uchite zinthu mwamphamvu,+ ndipo tisonyeze kulimba mtima chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu.+ Yehova adzachita zimene zili zabwino m’maso mwake.”+ 14  Choncho Yowabu ndi amuna amene anali naye anapita kukamenyana ndi Asiriya,+ ndipo Asiriyawo anathawa+ pamaso pake. 15  Ana a Amoni ataona kuti Asiriya athawa, nawonso anathawa+ pamaso pa Abisai m’bale wake ndi kubwerera kumzinda.+ Kenako Yowabu anabwerera ku Yerusalemu. 16  Asiriya ataona kuti agonjetsedwa+ ndi Aisiraeli, anatumiza amithenga kukaitana Asiriya amene anali m’dera la ku Mtsinje,*+ pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa gulu lankhondo la Hadadezeri. 17  Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse pamodzi ndi kuwoloka Yorodano kupita kukakumana nawo n’kukafola kuti amenyane nawo.+ Atafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi Asiriya, Asiriyawo anayamba kumenyana naye. 18  Koma Asiriyawo anathawa+ pamaso pa Isiraeli, ndipo Davide anapha Asiriya 7,000 okwera magaleta, ndi asilikali 40,000 oyenda pansi. Komanso anapha Sofaki, mtsogoleri wa gulu lankhondo.+ 19  Atumiki a Hadadezeri ataona kuti agonja pamaso pa Isiraeli,+ nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Davide n’kuyamba kumutumikira.+ Asiriya sanayesenso kupulumutsa ana a Amoni.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.