Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mbiri 16:1-43

16  Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+  Davide atamaliza kupereka nsembe yopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano,+ anadalitsa+ anthu m’dzina la Yehova.+  Kuwonjezera apo, Aisiraeli onse, mwamuna komanso mkazi, aliyense wa iwo anapatsidwa+ keke yozungulira, zipatso za kanjedza zouma zoumba pamodzi ndi mphesa zouma zoumba pamodzi.  Ndiyeno Davide anaika Alevi+ ena kukhala otumikira+ pa likasa la Yehova kuti azikumbutsa+ anthu, kuyamika,+ ndi kutamanda+ Yehova Mulungu wa Isiraeli.  Mtsogoleri wawo anali Asafu,+ wachiwiri wake anali Zekariya. Panalinso Yeyeli, Semiramoti, Yehiela, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obedi-edomu, ndi Yeyeli.+ Onsewa anali ndi zoimbira za zingwe ndi azeze,+ ndipo Asafu+ anali kuimba zinganga mokweza.+  Benaya ndi Yahazieli, omwe anali ansembe, ankaimba malipenga+ nthawi zonse patsogolo pa likasa la pangano la Mulungu woona.  Pa tsiku limeneli m’pamene Davide anathandiza+ nawo kuyamika+ Yehova kudzera mwa Asafu+ ndi abale ake kwanthawi yoyamba, ndi nyimbo yakuti:   “Yamikani Yehova,+ anthu inu. Itanani pa dzina lake.+ Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake!+   Muimbireni,+ muimbireni nyimbo zomutamanda!+ Sinkhasinkhani ntchito zake zonse zodabwitsa.+ 10  Nyadirani dzina+ lake loyera.+ Mtima wa anthu ofunafuna Yehova usangalale.+ 11  Funafunani Yehova ndiponso mphamvu zake,+ Funafunani nkhope yake+ nthawi zonse. 12  Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+ Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,+ 13  Inu mbadwa za Isiraeli mtumiki wake,+ Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.+ 14  Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+ Zigamulo zake zili padziko lonse lapansi.+ 15  Kumbukirani pangano lake mpaka kalekale,+ Kumbukirani lonjezo limene anapereka, ku mibadwo 1,000,+ 16  Kumbukirani pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+ Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki.+ 17  Pangano limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,+ Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,+ 18  Pamene anati: ‘Ndidzakupatsa dziko la Kanani,+ Kuti likhale gawo la cholowa chako.’+ 19  Pamene ananena zimenezi n’kuti inu muli ochepa,+ N’kuti muli ochepa kwambiri, komanso muli alendo m’dzikolo.+ 20  Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,+ Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina.+ 21  Mulungu sanalole aliyense kuwachitira zachinyengo,+ Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+ 22  Iye anati: ‘Anthu inu musakhudze odzozedwa anga, Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’+ 23  Imbirani Yehova, inu nonse okhala padziko lapansi!+ Tsiku ndi tsiku lengezani chipulumutso chimene amapereka!+ 24  Fotokozani za ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina, Ndiponso za ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu. 25  Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+ Ndipo ndi woyenera kuopedwa kuposa milungu ina yonse.+ 26  Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake.+ Koma Yehova, ndiye anapanga kumwamba.+ 27  Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake,+ Pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.+ 28  Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu, M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+ 29  M’patseni Yehova ulemerero wa dzina lake,+ Tengani mphatso n’kubwera nayo pamaso pake.+ Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+ 30  Njenjemerani ndi mantha* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi! Ndiponso dziko lapansi ndi lokhazikika, Silidzagwedezeka ku nthawi zonse.+ 31  Kumwamba kukondwere, ndipo dziko lapansi lisangalale,+ Ndipo anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’+ 32  Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,+ Mtunda ukondwere ndi zonse zimene zili kumeneko.+ 33  Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera chifukwa cha Yehova,+ Pakuti iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+ 34  Yamikani Yehova anthu inu, chifukwa iye ndi wabwino,+ Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+ 35  Nenani kuti: ‘Tipulumutseni, inu Mulungu wachipulumutso chathu,+ Tisonkhanitseni pamodzi ndi kutilanditsa kwa anthu a mitundu ina,+ Kuti titamande dzina lanu loyera,+ ndiponso kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+ 36  Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli kuyambira kalekale mpaka kalekale.’”+ Ndiyeno anthu onse ananena kuti, “Ame!”* n’kutamanda Yehova.+ 37  Kenako Davide anasiya Asafu+ ndi abale ake kumeneko pamaso pa likasa la Yehova, kuti azitumikira+ pamaso pa Likasalo nthawi zonse, malinga ndi zofunikira pa tsiku lililonse.+ 38  Anasiyanso Obedi-edomu ndi abale ake okwanira 68, ndiponso Obedi-edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa kukhala alonda a pachipata. 39  Anasiyanso Zadoki+ wansembe ndi abale ake ansembe kuchihema cha Yehova chimene chinali pamalo okwezeka a ku Gibeoni,+ 40  kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova nthawi zonse paguwa lansembe zopsereza, m’mawa ndi madzulo, malinga ndi zonse zolembedwa m’chilamulo cha Yehova chimene analamula Aisiraeli.+ 41  Iwowa anali limodzi ndi Hemani+ ndi Yedutuni ndiponso amuna onse amene anasankhidwa+ mwa kutchulidwa mayina kuti aziyamika Yehova,+ chifukwa “kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+ 42  Anasiya Hemani+ ndi Yedutuni+ limodzi ndi amuna aja kuti aziimba malipenga,+ zinganga ndi zipangizo zina zoimbira nyimbo ya Mulungu woona, ndipo ana+ a Yedutuni anali alonda a pachipata. 43  Pambuyo pake anthu onse ananyamuka, ndipo aliyense anapita kunyumba kwake.+ Nayenso Davide anapita kunyumba kwake n’kukadalitsa banja lake.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “imvani kupweteka kwambiri.”
Mawuwa amatanthauza kuti, “zikhale momwemo.”