Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Mbiri 15:1-29

15  Davide anapitiriza kumanga nyumba+ zake mu Mzinda wa Davide, ndipo anakonza malo+ oikapo likasa la Mulungu woona, n’kulimangira hema.  Pa nthawi imeneyi m’pamene Davide ananena kuti: “Alevi okha ndiwo ayenera kunyamula likasa la Mulungu woona, chifukwa Yehova anasankha iwowa kuti azinyamula likasa la Yehova+ ndi kum’tumikira+ mpaka kalekale.”*  Ndiyeno Davide anasonkhanitsa Aisiraeli onse ku Yerusalemu+ kuti akanyamule likasa+ la Yehova, kupita nalo kumalo amene iye anakonza kuti akaliike.  Kenako Davide anaitanitsa ana a Aroni+ ndi Alevi.  Pa ana a Kohati panali Uriyeli+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 120.  Pa ana a Merari+ panali Asaya+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 220.  Pa ana a Gerisomu+ panali Yoweli+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 130.  Pa ana a Elizafana+ panali Semaya+ mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 200.  Pa ana a Heburoni panali Elieli mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 80. 10  Pa ana a Uziyeli+ panali Aminadabu mtsogoleri wawo ndi abale ake okwanira 112. 11  Kuwonjezera pa amenewa, Davide anaitanitsa Zadoki+ ndi Abiyatara,+ omwe anali ansembe. Anaitanitsanso Alevi awa: Uriyeli,+ Asaya,+ Yoweli,+ Semaya,+ Elieli,+ ndi Aminadabu. 12  Tsopano Davide anawauza kuti: “Inuyo ndinu atsogoleri+ a nyumba ya makolo a Alevi. Choncho inu ndi abale anu mudziyeretse,+ ndipo mukatenge likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli n’kukaliika kumalo amene ine ndakonza kuti likakhaleko. 13  Chifukwa chakuti ulendo woyamba uja inuyo simunapite kukalitenga,+ mkwiyo wa Yehova Mulungu wathu unatiphulikira,+ pakuti sitinatsatire malangizo ake monga mwa mwambo wathu.”+ 14  Chotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ kuti akatenge likasa la Yehova Mulungu wa Isiraeli. 15  Ndiyeno ana a Alevi anakanyamula+ likasa la Mulungu woona, monga mmene Mose anawalamulira potsatira mawu a Yehova. Iwo analinyamula pamapewa awo pogwiritsa ntchito ndodo zake.+ 16  Tsopano Davide anauza atsogoleri a Alevi kuti aike m’malo awo abale awo oimba+ okhala ndi zipangizo zoimbira.+ Zipangizozo zinali zoimbira za zingwe,+ azeze,+ ndi zinganga.+ Anawauza kuti aimbe mokweza kuti nyimbo zachisangalalo zimveke. 17  Chotero Alevi anatenga Hemani+ mwana wa Yoweli n’kumuika pamalo ake. Kenako, pa abale ake, anatengapo Asafu+ mwana wa Berekiya n’kumuika pamalo ake. Pa abale awo, ana a Merari, anatengapo Etani+ mwana wa Kusaya n’kumuika pamalo ake. 18  Iwowa anawaika pamalo awo pamodzi ndi abale awo a gulu lachiwiri.+ Abale awowo anali Zekariya,+ Beni, Yaazieli, Semiramoti, Yehiela, Uni, Eliyabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, ndiponso Obedi-edomu+ ndi Yeyeli, alonda a pachipata. 19  Panalinso oimba awa: Hemani,+ Asafu,+ ndi Etani, kuti aimbe zinganga zamkuwa mokweza.+ 20  Zekariya, Azieli,+ Semiramoti, Yehiela, Uni, Eliyabu, Maaseya, ndi Benaya, anali ndi zoimbira za zingwe zochunidwa kuti ziziimba Alamoti.*+ 21  Matitiya,+ Elifelehu, Mikineya, Obedi-edomu, Yeyeli, ndi Azaziya, anali ndi azeze+ ochunidwa kuti aziimba Seminiti,*+ kuti akhale otsogolera nyimbo. 22  Kenaniya+ ndiye anali mtsogoleri wa Alevi pa ntchito yonyamula katundu, ndipo anali kupereka malangizo onyamulira katundu, chifukwa anali katswiri pa ntchito imeneyi.+ 23  Berekiya ndi Elikana anali alonda+ a Likasa. 24  Sebaniya, Yosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya, ndi Eliezere, anali ansembe omwe anali kuimba malipenga mokweza+ patsogolo pa likasa la Mulungu woona. Obedi-edomu ndi Yehiya anali alonda a Likasa. 25  Koma Davide+ ndi akulu a Isiraeli+ ndiponso atsogoleri+a anthu 1,000 aliyense, anali kuyenda mosangalala+ kupita kunyumba kwa Obedi-edomu,+ kukatenga likasa la pangano la Yehova. 26  Mulungu woona atathandiza+ Alevi ponyamula likasa la pangano la Yehova, iwo anapereka nsembe ng’ombe zazing’ono zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.+ 27  Davide, Alevi onse onyamula Likasa, oimba, ndi Kenaniya+ mtsogoleri pa ntchito yonyamula katundu imene oimba+ anali kugwira, anavala malaya akunja odula manja, ansalu yabwino kwambiri. Koma Davide anavalanso efodi+ wansalu. 28  Aisiraeli onse anali kupita ndi likasa la pangano la Yehova akufuula mokondwera,+ ndiponso akuliza nyanga za nkhosa+ ndi malipenga.+ Iwo anali kuimbanso mokweza zinganga,+ zoimbira za zingwe, ndi azeze.+ 29  Ndiyeno likasa la pangano+ la Yehova litafika mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi, ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kusangalala.+ Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Alamoti,” ndi mawu achiheberi a chuni. Mawuwa sadziwika tanthauzo lake, koma mwina ankatanthauza mawu a sapulano a atsikana, kapena mawu okwera kwambiri a anyamata.
“Seminiti,” ndi mawu achiheberi a chuni cha nyimbo, mwina otanthauza mawu oimbidwa motsitsa kapena kuti mwabesi.