Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mbiri 14:1-17

14  Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo+ anatumiza amithenga kwa Davide. Anatumizanso matabwa a mkungudza,+ anthu omanga makoma, ndi anthu a ntchito zamatabwa kuti akamangire Davide nyumba.+  Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike+ mu Isiraeli, pakuti ufumu wake unakwezedwa kwambiri chifukwa cha anthu ake Aisiraeli.+  Davide anatenganso akazi ena+ mu Yerusalemu, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+  Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo ndi awa: Samuwa,+ Sobabu,+ Natani,+ Solomo,+  Ibara,+ Elisua, Elipeleti,+  Noga, Nefegi,+ Yafiya,  Elisama,+ Beliyada, ndi Elifeleti.+  Tsopano Afilisiti anamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli yense.+ Choncho Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, anapita kukamenyana nawo.  Afilisitiwo anafika ndi kuyamba kufunkha m’chigwa cha Arefai.+ 10  Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu+ kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwaperekadi m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi m’manja mwako.” 11  Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu,+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero, Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” N’chifukwa chake malowo+ anawatcha Baala-perazimu. 12  Pa nthawiyi Afilisiti anasiya milungu yawo kumeneko.+ Ndiyeno Davide atalamula, milunguyo anaitentha pamoto.+ 13  Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso ndi kuyamba kufunkha m’chigwacho.+ 14  Pamenepo Davide anafunsiranso+ kwa Mulungu ndipo Mulungu woonayo anamuyankha kuti: “Ayi usapite kukakumana nawo. Koma uwazembere ndipo ukawaukire kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 15  Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka,+ ukatuluke n’kumenyana nawo+ chifukwa Mulungu woona adzakhala atatsogola+ kukapha gulu lankhondo la Afilisiti.” 16  Choncho Davide anachitadi monga mmene Mulungu woona anamulamulira,+ moti iwo anapha asilikali a Afilisiti kuchokera ku Gibeoni+ mpaka kukafika ku Gezeri.+ 17  Chotero Davide anatchuka+ mpaka mbiri yake inamveka kumayiko onse. Ndipo Yehova anachititsa kuti mitundu yonse iziopa Davide.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.