Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mbiri 12:1-40

12  Tsopano nawa anthu amene anapita kwa Davide ku Zikilaga,+ pa nthawi imene iye sanali kuyenda momasuka chifukwa choopa Sauli+ mwana wa Kisi. Iwowa anali ena mwa amuna amphamvu+ amene anamuthandiza pankhondo.  Amuna onyamula mauta amenewa, ankatha kugwiritsa ntchito mkono wamanja ndi wamanzere+ kuponyera miyala+ kapena kuponyera mivi+ pa uta.+ Amenewa anali abale ake a Sauli wa fuko la Benjamini.  Panali Ahiyezeri mtsogoleri wawo ndiponso Yowasi. Amenewa anali ana a Semaa wa ku Gibeya.+ Panalinso Yezieli ndi Peleti, ana a Azimaveti,+ Beraka ndi Yehu wa ku Anatoti,+  Isimaya wa ku Gibeoni,+ mwamuna wamphamvu pa amuna 30+ komanso mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Kenako panali Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera,+  Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harifi.  Komanso panali Elikana, Isiya, Azareli, Yoezeri, ndi Yasobeamu. Amenewa anali mbadwa za Kora.+  Panalinso Yoela ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori.  Ndiyeno panali Agadi ena amene anasankha kupita kumbali ya Davide m’chipululu,+ kumalo ovuta kufikako. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima, asilikali okonzekera nkhondo, amene zishango zawo zazikulu ndi mikondo yawo ing’onoing’ono zinkakhala zokonzeka.+ Nkhope zawo zinali ngati nkhope za mikango,+ ndipo liwiro lawo linali ngati la mbawala m’mapiri.+  Mtsogoleri wawo anali Ezeri, wachiwiri anali Obadiya, wachitatu Eliyabu, 10  wachinayi Misimana, wachisanu Yeremiya, 11  wa 6 Atai, wa 7 Elieli, 12  wa 8 Yohanani, wa 9 Elizabadi, 13  wa 10 Yeremiya, ndipo wa 11 anali Makibanai. 14  Amenewa anali a fuko la Gadi,+ atsogoleri a asilikali. Wamng’ono wa iwo akanatha kulimbana ndi asilikali 100, ndipo wamkulu wa iwo akanatha kulimbana ndi asilikali 1,000.+ 15  Awa ndi amene anawoloka mtsinje wa Yorodano+ m’mwezi woyamba* pamene mtsinjewo unasefukira mbali zake zonse.+ Kenako anathamangitsira kum’mawa ndi kumadzulo anthu onse amene anali kukhala m’zigwa. 16  Amuna ena a fuko la Benjamini ndi la Yuda anayenda mpaka kukafika kwa Davide, kumalo ovuta kufikako.+ 17  Pamenepo Davide anatuluka kukakumana nawo, ndipo anawauza kuti: “Ngati mwabwerera mtendere+ kwa ine kudzandithandiza, mtima wanga ugwirizana nanu.+ Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, pamene sindinalakwe ndi manja anga,+ Mulungu+ wa makolo athu aone zimenezo ndipo aweruze.”+ 18  Poyankha, Amasai mkulu wa asilikali 30 anagwidwa ndi mzimu,+ ndipo anati: “Ifetu ndife anthu anu, inu a Davide, ndipotu tili kumbali yanu,+ inu mwana wa Jese. Mtendere ukhale nanu, ndiponso mtendere ukhale ndi iye amene akukuthandizani, Pakuti Mulungu wanu wakuthandizani.”+ Choncho Davide anawalandira ndi kuwaika pakati pa atsogoleri a asilikali.+ 19  Analiponso ena a fuko la Manase amene anapanduka n’kupita kwa Davide pamene iye anabwera ndi Afilisiti+ kudzamenyana ndi Sauli. Koma Davide sanawathandize Afilisitiwo chifukwa olamulira awo ogwirizana+ atakambirana, anam’bweza chifukwa anati: “Ameneyu akhoza kukatitembenukira n’kugwirizana ndi mbuye wake Sauli, kenako akatidula mitu.”+ 20  Davide atapita ku Zikilaga,+ anthu ena a fuko la Manase anapita kumbali yake. Anthuwo anali Adinala, Yozabadi, Yediyaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu, ndi Ziletai. Aliyense wa amenewa anali mtsogoleri+ wa asilikali 1,000, a fuko la Manase. 21  Atsogoleriwa anathandiza Davide kulimbana ndi gulu la achifwamba,+ chifukwa atsogoleri onsewa anali amuna amphamvu+ ndi olimba mtima, ndipo anakhala atsogoleri a asilikali. 22  Tsiku ndi tsiku anthu anali kubwera+ kwa Davide kudzamuthandiza, mpaka anachuluka n’kukhala khamu lankhondo lalikulu,+ ngati khamu lankhondo la Mulungu.+ 23  Tsopano nazi ziwerengero za atsogoleri a anthu okonzekera kumenya nkhondo amene anabwera kwa Davide ku Heburoni,+ kudzam’patsa ufumu+ wa Sauli malinga ndi lamulo la Yehova.+ 24  Anthu okonzekera kumenya nkhondo a fuko la Yuda, onyamula zishango zazikulu ndi mikondo ing’onoing’ono, analipo 6,800. 25  Anthu a fuko la Simiyoni, asilikali amphamvu ndi olimba mtima, analipo 7,100. 26  A fuko la Levi analipo 4,600. 27  Yehoyada ndiye anali mtsogoleri+ wa ana a Aroni,+ ndipo anali kuyang’anira anthu 3,700. 28  Panalinso Zadoki+ mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima ndi atsogoleri 22 a m’nyumba ya makolo ake. 29  A fuko la Benjamini,+ abale ake a Sauli,+ analipo 3,000. Kufikira pa nthawiyo, ambiri mwa anthu a fukolo, anali kulondera mosamala nyumba ya Sauli. 30  A fuko la Efuraimu analipo 20,800, amuna amphamvu+ ndi olimba mtima, otchuka m’nyumba ya makolo awo. 31  A hafu ya fuko la Manase,+ amene anatchulidwa mayina kuti adzalonge Davide ufumu, analipo 18,000. 32  A fuko la Isakara,+ amene anali ndi nzeru zotha kudziwa nthawi,+ ndi zimene Aisiraeli ayenera kuchita,+ analipo atsogoleri 200, ndipo iwo anali kulamulira abale awo onse. 33  A fuko la Zebuloni,+ onse oyenerera kupita kunkhondo, kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi zida zawo zonse zankhondo, analipo 50,000. Popita kwa Davide, iwo sanapite ndi mitima iwiri. 34  A fuko la Nafitali+ analipo atsogoleri 1,000. Pamodzi ndi iwowa panali onyamula zishango zazikulu ndi mikondo, okwanira 37,000. 35  A fuko la Dani, okafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo, analipo 28,600. 36  A fuko la Aseri,+ onse oyenerera kupita kunkhondo, kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo, analipo 40,000. 37  Kutsidya lina la Yorodano+ kunachokera a fuko la Rubeni, a fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase okhala ndi zida zonse zankhondo okwanira 120,000. 38  Onsewa anali amuna ankhondo, okhalira limodzi pamzere wa omenya nkhondo. Iwo anapita ndi mtima wathunthu+ ku Heburoni kukalonga Davide kukhala mfumu ya Isiraeli yense. Ndiponso Aisiraeli ena onse otsala anali ndi mtima umodzi wolonga Davide ufumu.+ 39  Anthuwa anakhala kumeneko ndi Davide masiku atatu. Anali kudya ndi kumwa,+ chifukwa abale awo anali atawakonzekera. 40  Ndiponso anthu onse apafupi ndi kumeneko, mpaka kumadera a Isakara,+ Zebuloni,+ ndi Nafitali,+ anali kubweretsa chakudya pa abulu,+ ngamila, nyulu* ndi ng’ombe. Anabweretsa zakudya zophikidwa ndi ufa.+ Anabweretsanso nkhuyu zouma zoumba pamodzi,+ mphesa zouma zoumba pamodzi,+ vinyo,+ mafuta,+ ng’ombe,+ ndi nkhosa.+ Anabweretsa zimenezi zambirimbiri, popeza mu Isiraeli munali chisangalalo+ chachikulu.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda, kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.