Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Mafumu 12:1-33

12  Rehobowamu+ anapita ku Sekemu,+ chifukwa kumeneko n’kumene Aisiraeli onse anasonkhana kuti akamulonge ufumu.  Yerobowamu+ mwana wa Nebati anamva zimenezi akadali ku Iguputo, (pajatu anathawa Mfumu Solomo n’kukakhala ku Iguputo),+  ndipo anthu anatumiza uthenga womuitana. Kenako Yerobowamu ndi mpingo wonse wa Isiraeli anabwera n’kuyamba kulankhula ndi Rehobowamu kuti:+  “Bambo anu anaumitsa goli lathu. Tsopano inuyo mufewetse+ ntchito yowawa ya bambo anu ndi goli lawo lolemera+ limene anatisenzetsa, ndipo tidzakutumikirani.”+  Rehobowamu atamva zimenezi anauza anthuwo kuti: “Pitani kaye kwa masiku atatu, ndipo mukabwerenso kwa ine.”+ Anthuwo anapitadi.  Ndiyeno Mfumu Rehobowamu inafunsira nzeru kwa akulu+ amene anali kutumikira bambo ake Solomo pamene anali moyo. Inawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti anthuwa ndiwayankhe bwanji?”+  Iwo anaiuza kuti: “Ngati lero mukufuna kuti mukhale mtumiki wa anthuwa ndi kuwatumikira,+ muwayankhe ndi mawu abwino,+ ndipo iwo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”+  Koma iye sanamvere malangizo ochokera kwa akulu aja, m’malomwake anayamba kukafunsira malangizo kwa achinyamata amene anakulira naye limodzi,+ omwe anali kumutumikira.+  Iye anawafunsa kuti: “Kodi mungapereke malangizo+ otani kuti tiwayankhe anthuwa amene andipempha kuti, ‘Fewetsani goli limene bambo anu anatisenzetsa’?”+ 10  Achinyamata amene anakulira naye limodziwo anamuuza kuti: “Izi n’zimene mukanene+ kwa anthu awa amene akuuzani kuti, ‘Bambo anu anatisenzetsa goli lolemera, koma inuyo mutipeputsireko.’ Muwauze kuti, ‘Chala changa chaching’ono chidzakhala chachikulu kuposa chiuno cha bambo anga.+ 11  Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera koma ineyo ndiwonjezera goli lanulo.+ Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu koma ineyo ndikukwapulani ndi zikoti zaminga.’”+ 12  Pa tsiku lachitatu, Yerobowamu ndi anthu onse anapita kwa Rehobowamu, monga momwe mfumuyo inanenera kuti: “Mukabwerenso kwa ine pa tsiku lachitatu.”+ 13  Mfumuyo inayamba kuyankha anthuwo mwaukali+ ndipo sinamvere malangizo ochokera kwa akulu amene anailangiza aja.+ 14  Iyo inayamba kulankhula kwa anthuwo motsatira malangizo amene achinyamata aja+ anaipatsa. Inati: “Bambo anga anakusenzetsani goli lolemera, koma ine ndidzawonjezera goli lanulo. Bambo anga anakukwapulani ndi zikwapu, koma ine ndidzakukwapulani ndi zikoti zaminga.”+ 15  Mfumuyo sinamvere anthuwo+ chifukwa zinthu zinatembenuka chonchi mwa kufuna kwa Yehova,+ kuti akwaniritse mawu amene Yehovayo analankhula+ kwa Yerobowamu mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya+ Msilo. 16  Aisiraeli onse ataona kuti mfumuyo sinawamvere, anaiyankha kuti: “Tili ndi gawo lanji mwa Davide?+ Ife tilibe cholowa mwa mwana wa Jese. Pitani kwa milungu yanu+ Aisiraeli. Tsopano iwe Davide,+ uzisamalira nyumba yako yokha.” Aisiraeliwo atatero, anayamba kubwerera kumahema awo. 17  Koma Rehobowamu anapitiriza kulamulira ana a Isiraeli amene anali kukhala m’mizinda ya ku Yuda.+ 18  Kenako Mfumu Rehobowamu inatumiza Adoramu+ amene anali kuyang’anira anthu ogwira ntchito yokakamiza,+ koma Aisiraeli onse anam’ponya miyala+ n’kumupha. Komabe, Mfumu Rehobowamu inatha kukwera galeta n’kuthawira ku Yerusalemu. 19  Ndipo Aisiraeli anapitiriza kuukira+ nyumba ya Davide mpaka lero.+ 20  Aisiraeli onse atangomva kuti Yerobowamu wabwera, nthawi yomweyo anatumiza uthenga womuitanira kumene anasonkhana, ndipo anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse.+ Palibenso amene ankatsatira nyumba ya Davide kupatula fuko la Yuda lokha.+ 21  Rehobowamu atafika ku Yerusalemu,+ nthawi yomweyo anasonkhanitsa amuna ochita kusankhidwa odziwa kumenya nkhondo okwanira 180,000 a nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini.+ Anawasonkhanitsa kuti akamenyane ndi nyumba ya Isiraeli pofuna kuti ufumu ubwerere kwa Rehobowamu mwana wa Solomo. 22  Kenako mawu a Mulungu woona anafikira Semaya+ munthu wa Mulungu woona,+ kuti: 23  “Kauze Rehobowamu mwana wa Solomo, mfumu ya Yuda, ndi nyumba yonse ya Yuda ndi Benjamini, ndi anthu ena onse kuti, 24  ‘Yehova wati: “Musapite kukamenyana ndi abale anu, ana a Isiraeli.+ Aliyense abwerere kunyumba kwake, chifukwa zimene zachitikazi, zachitika mwa kufuna kwanga.”’”+ Choncho anamvera mawu a Yehova+ n’kubwerera kwawo malinga ndi mawu a Yehova.+ 25  Yerobowamu anamanga mzinda wa Sekemu+ m’dera lamapiri la Efuraimu, n’kuyamba kukhala kumeneko. Kenako anachoka kumeneko n’kupita kukamanga mzinda wa Penueli.+ 26  Ndiyeno Yerobowamu anayamba kunena mumtima mwake kuti:+ “Tsopano ufumuwu ubwerera kunyumba ya Davide.+ 27  Anthu awa akapitiriza kupita kukapereka nsembe kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu,+ mtima wawo ubwerera kwa mbuye wawo Rehobowamu mfumu ya Yuda, ndipo ineyo adzandipha+ n’kubwerera kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.” 28  Choncho mfumuyo inakambirana ndi anthu ena+ n’kupanga ana awiri a ng’ombe agolide.+ Itatero inauza anthuwo kuti: “N’zovuta kwambiri kwa inu kuti muzipita ku Yerusalemu. Nayu Mulungu wanu+ Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+ 29  Ndiyeno chifaniziro cha ng’ombe chimodzi anakachiika ku Beteli,+ china anakachiika ku Dani.+ 30  Chinthu chimenechi chinakhala chochimwitsa anthu.+ Anthuwo anali kukafika mpaka ku Dani kukaima pamaso pa chifaniziro cha mwana wa ng’ombecho. 31  Yerobowamu anayamba kumanga akachisi m’malo okwezeka.+ Ndiyeno anasankha anthu wamba, anthu amene sanali ana a Levi, n’kuwaika kuti akhale ansembe.+ 32  M’mwezi wa 8, pa tsiku la 15 la mweziwo, Yerobowamu anachita chikondwerero chofanana ndi cha ku Yuda.+ Anachita chikondwererochi kuti apereke nsembe kwa ana a ng’ombe amene anawapanga, paguwa lansembe limene analimanga ku Beteli.+ M’malo okwezeka a ku Beteli amene anamanga, anaikako ansembe kuti azitumikira. 33  Yerobowamu anapereka nsembe pa tsiku la 15, m’mwezi wa 8 womwe anausankha yekha.+ Anapereka nsembezo paguwa limene anamanga ku Beteli. Ndipo anakonzera chikondwerero ana a Isiraeli ndi kupereka nsembe zautsi kuti afukize paguwalo.+

Mawu a M'munsi