Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Atesalonika 5:1-28

5  Koma tsopano za nthawi ndi nyengo+ abale, simukufunika kukulemberani kanthu.  Pakuti inu eni mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.+  Pamene azidzati:+ “Bata ndi mtendere!”+ chiwonongeko+ chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati,+ ndipo sadzapulumuka.+  Koma inu abale simuli mu mdima ayi,+ kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingachitire kwa mbala.+  Pakuti inu nonse ndinu ana a kuwala+ ndiponso ana a usana.+ Si ife a usiku kapena a mdima ayi.+  Chotero tisapitirize kugona+ ngati mmene enawo akuchitira,+ koma tikhalebe maso+ ndipo tikhalebe oganiza bwino.+  Pakuti ogona+ amagona usiku,+ ndipo amene amaledzera amakonda kuledzera usiku.  Koma ife amene tili a usana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa+ chachikhulupiriro+ ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo chachipulumutso+ monga chisoti,+  chifukwa Mulungu sanatisankhe kuti tidzaone mkwiyo.+ Anatisankha kuti tipeze chipulumutso+ kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 10  Iye anatifera,+ kuti kaya tikhala maso kapena tigona, tikhale ndi moyo limodzi ndi iye.+ 11  Choncho pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana+ monga mmene mukuchitira.+ 12  Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani+ mwa Ambuye ndi kukulangizani. 13  Muwapatse ulemu waukulu mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo.+ Khalani mwamtendere pakati panu.+ 14  Komanso tikukudandaulirani abale kuti, langizani ochita zosalongosoka,+ lankhulani molimbikitsa kwa amtima wachisoni,+ thandizani ofooka, khalani oleza+ mtima kwa onse. 15  Onetsetsani kuti wina asabwezere choipa pa choipa kwa wina aliyense,+ koma nthawi zonse yesetsani kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.+ 16  Muzikhala okondwera nthawi zonse.+ 17  Muzipemphera mosalekeza.+ 18  Muziyamika+ pa chilichonse, pakuti chimenechi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. 19  Musazimitse moto wa mzimu.+ 20  Musanyoze mawu aulosi.+ 21  Tsimikizirani zinthu zonse.+ Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.+ 22  Pewani zoipa zamtundu uliwonse.+ 23  Mulungu wamtendere+ mwiniyo akupatuleni+ kuti muchite utumiki wake. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, ndi thupi lanu, zisungidwe zopanda chilema ndi zopanda cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 24  Amene akukuitanani ndi wokhulupirika, ndipo adzachitadi zimenezi. 25  Abale, pitirizani kutipempherera.+ 26  Perekani moni kwa abale onse ndi kupsompsonana kwaubale.+ 27  Ndikukulamulani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.+ 28  Kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.
Onani Zakumapeto 8.