Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Atesalonika 1:1-10

1  Ine Paulo, pamene ndili limodzi ndi Silivano+ ndi Timoteyo,+ ndikulembera mpingo wa Atesalonika wogwirizana+ ndi Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu, kuti: Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere+ zikhale nanu.  Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamatchula za inu nonse m’mapemphero athu.+  Timatero pakuti timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro,+ ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra chifukwa cha chiyembekezo+ chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.  Pakuti tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti Mulunguyo ndiye anakusankhani.+  Chifukwa pamene tinali kulalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unakukhudzani kwambiri, komanso unabwera limodzi ndi mphamvu+ ya mzimu woyera, ndipo unachititsa kuti mukhale otsimikiza+ mtima kwambiri. Ndipo inuyo mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani.+  Choncho munatsanzira+ ifeyo komanso munatsanzira Ambuye,+ pakuti munalandira mawuwo ndi chimwemwe cha mzimu woyera+ ngakhale kuti munali m’masautso+ ambiri,  moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.  Ndipotu, si kuti mawu a Yehova+ ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha ayi, koma kwina kulikonse chikhulupiriro+ chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu.  Pakuti iwo amanena mmene ife tinafikira pakati panu koyamba. Amanenanso mmene inu munatembenukira kwa Mulungu, kusiya mafano+ anu kuti mutumikire Mulungu wamoyo+ ndi woona,+ 10  ndi kuyembekezera+ Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa.+ Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo ukubwerawo.+

Mawu a M'munsi