Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 8:1-13

8  Tsopano ponena za zakudya zoperekedwa kwa mafano,+ tikudziwa kuti tonse ndife odziwa zinthu.+ Kudziwa zinthu kumachititsa munthu kudzitukumula, koma chikondi chimamangirira.+  Ngati wina akuganiza kuti akudziwa za chinachake,+ sanachidziwebe mokwanira.+  Koma ngati munthu akukonda Mulungu,+ ameneyo amadziwika kwa Mulungu.+  Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+  Pakuti ngakhale ilipo yotchedwa “milungu,”+ kaya kumwamba+ kapena padziko lapansi,+ ndipo n’zoona ilipodi “milungu” yambiri ndi “ambuye” ambiri,+  kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha basi+ amene ndi Atate.+ Iye ndi amene zinthu zonse zinachokera mwa iye, ndipo ifeyo ndife ake.+ Ndipo pali Ambuye+ mmodzi, Yesu Khristu,+ amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo.  Ngakhale zili choncho, si onse amene amadziwa zimenezi.+ Koma ena, pokhala ozolowera mafano enaake mpaka panopo, akamadya chakudya choperekedwa kwa fano amachidya monga choperekedwadi kwa fano,+ ndipo popeza chikumbumtima chawo n’chofooka, chimaipitsidwa.+  Koma chakudya sichingatikometse pamaso pa Mulungu.+ Ngati sitinadye chakudyacho, sikuti tamulakwira, ndiponso ngati tadya, sikuti tamukondweretsa mwapadera.+  Koma muzikhalabe osamala kuti ufulu wanuwo usakhale chopunthwitsa kwa ofooka.+ 10  Pakuti ngati wina angaone iweyo wodziwa zinthuwe ukudya chakudya m’kachisi wa mafano, kodi chikumbumtima cha munthu wofooka uja sichidzamulimbikitsa kudya zakudya zoperekedwa kwa mafano?+ 11  Zikatero, ungawononge munthu wofookayo, yemwe ndi m’bale wako amene Khristu anamufera,+ chifukwa chakuti ukudziwa zinthu. 12  Koma inu mukamachimwira abale anu motero ndi kuvulaza chikumbumtima chawo+ chofookacho, mukuchimwira Khristu. 13  Chotero ngati chakudya chikukhumudwitsa+ m’bale wanga, sindidzadyanso nyama m’pang’ono pomwe, kuti ndisakhumudwitse m’bale wanga.+

Mawu a M'munsi