Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 6:1-20

6  Kodi wina wa inu akakhala ndi mlandu+ ndi mnzake, amalimba mtima bwanji kupita kukhoti kwa anthu osalungama,+ osati kwa oyerawo?+  Kapena simukudziwa kuti oyerawo adzaweruza+ dziko?+ Ndipo ngati mudzaweruza dziko, kodi simungathe kuzenga milandu yaing’ono kwambiri+ ngati imeneyo?  Kodi simukudziwa kuti tidzaweruza angelo?+ Ndiye tingalephere bwanji kuweruza nkhani za m’moyo uno?  Chotero, ngati muli ndi nkhani zofuna kuweruza+ m’moyo uno, kodi anthu amene mpingo suwayesa kanthu ndiwo mukuwaika kukhala oweruza?+  Ndikulankhula choncho kuti ndikuchititseni manyazi.+ Kodi zoona palibe wanzeru ndi mmodzi yemwe pakati panu amene angaweruze mlandu pakati pa abale ake?  Kodi m’bale azitengera m’bale wake kukhoti, kwa anthu osakhulupirira?+  Kunena zoona, ndiye kuti mwalephereratu ngati mukutengerana kukhoti. Bwanji osangolola kulakwiridwa?+ Bwanji osalola kuberedwa?+  M’malomwake, inuyo mumachita zolakwa ndiponso mumabera ena, ndipo abale anu ndi amene mumawachitira zimenezi.+  Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu?+ Musasocheretsedwe. Adama,+ opembedza mafano,+ achigololo,+ amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo,+ amuna ogona amuna anzawo,+ 10  akuba, aumbombo,+ zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.+ 11  Ndipo ena mwa inu munali otero.+ Koma mwasambitsidwa kukhala oyera,+ mwapatulidwa,+ mwayesedwa olungama+ m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu,+ komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.+ 12  Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka+ kwa ine, koma sindidzalola kuti chinthu china chizindilamulira.+ 13  Chakudya ndi cha mimba, ndipo mimba ndi ya chakudya,+ koma Mulungu adzawononga mimba ndi chakudya chomwe.+ Choncho thupi silochitira dama koma ndi la Ambuye,+ ndipo Ambuye ndiye mwini thupi.+ 14  Koma Mulungu anaukitsa Ambuye+ kwa akufa+ ndipo adzaukitsanso ife mwa mphamvu yake.+ 15  Kodi simukudziwa kuti matupi anu ndiwo ziwalo+ za Khristu?+ Ndiye kodi ine nditenge ziwalo za Khristu n’kuzisandutsa ziwalo za hule?+ Zosatheka zimenezo! 16  Kodi zoona inu simukudziwa kuti amene wadziphatika kwa hule amakhala thupi limodzi ndi hulelo? Pakuti anati, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.” 17  Koma amene waphatikana ndi Ambuye wakhala mzimu+ umodzi ndi iye.+ 18  Thawani dama. Tchimo lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita dama amachimwira thupi lake.+ 19  Kodi zoona inu simukudziwa kuti thupi lanu ndilo kachisi+ wa mzimu woyera umene uli mwa inu,+ umene munapatsidwa ndi Mulungu? Ndiponso mwiniwake wa inuyo si inu,+ 20  pakuti munagulidwa pa mtengo wokwera.+ Mulimonse mmene zingakhalire, lemekezani Mulungu+ ndi matupi anu.+

Mawu a M'munsi