Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 5:1-13

5  Mbiri yamvekatu kuti pakuchitika dama*+ pakati panu, ndipo dama lake ndi loti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+  Kodi mukudzitukumula,+ m’malo mwa kumva chisoni,+ kuti munthu amene anachita zimenezi achotsedwe pakati panu?+  Ineyo pandekha, ngakhale kuti mwa thupi sindili kumeneko koma mu mzimu ndili komweko, ndamuweruza kale+ ndithu munthu amene wachita zimenezi, ngati kuti ndinali nanu kumeneko.  Ndaweruza kuti m’dzina la Ambuye wathu Yesu, mukakumana pamodzi, komanso ndi mzimu wanga ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,+  mupereke munthu ameneyu kwa Satana+ kuti thupilo liwonongedwe, n’cholinga choti mzimuwo+ upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye.+  Chimene mukudzitamira+ si chabwino ayi. Kodi simukudziwa kuti chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa+ mtanda wonse?+  Chotsani chofufumitsa chakalecho, kuti mukhale mtanda watsopano,+ popeza ndinu opanda chofufumitsa. Pakuti Khristu+ waperekedwa+ monga nsembe yathu ya pasika.+  Chotero tiyeni tichite chikondwererochi,+ osati ndi chofufumitsa chakale,+ kapena chofufumitsa+ choimira zoipa ndi uchimo,+ koma ndi mikate yopanda chofufumitsa yoimira kuona mtima ndi choonadi.+  M’kalata yanga ndinakulemberani kuti muleke kuyanjana ndi anthu adama. 10  Sindikutanthauza kuti muzipeweratu adama+ a m’dzikoli,+ kapena aumbombo ndi olanda, kapena opembedza mafano ayi. Kuti muchite zimenezo, ndiye mungafunikire kutuluka m’dzikomo.+ 11  Koma tsopano ndikukulemberani kuti muleke kuyanjana+ ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo,+ kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa,+ kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi. 12  Nanga kuweruza anthu amene ali kunja*+ ndi ntchito yanga ngati? Kodi inu si paja mumaweruza amene ali mkati,+ 13  ndipo Mulungu amaweruza amene ali kunja?+ “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wachikhristu.