Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 2:1-16

2  Chotero abale, pamene ndinafika kwa inu kudzalengeza za chinsinsi chopatulika+ cha Mulungu, sindinafike ndi malankhulidwe+ adzaoneni kapena ndi nzeru zodabwitsa.  Pakuti ndinasankha kuti pamene ndili pakati panu ndisadziwe china chilichonse kupatulapo Yesu Khristu,+ amene anapachikidwa.  Choncho ndinafika kwa inu ndili wofooka, ndipo ndinali kunjenjemera+ ndi mantha.  Polankhula ndi polalikira, mawu anga sanali okopa, oonetsa nzeru, koma oonetsa mzimu ndi mphamvu,+  kuti chikhulupiriro chanu chisazikike pa nzeru za anthu,+ koma pa mphamvu ya Mulungu.+  Tsopano tikulankhula za nzeru kwa anthu okhwima mwauzimu,+ koma osati nzeru+ ya nthawi ino kapena ya olamulira a nthawi* ino+ amene adzawonongedwa.+  Koma tikulankhula za nzeru ya Mulungu imene inaonekera m’chinsinsi chopatulika,+ nzeru yobisika. Mulungu anakonzeratu zochita zimenezi kusanakhale nthawi* zosiyanasiyana,+ kuti tikhale ndi ulemerero.  Palibe wolamulira+ ndi mmodzi yemwe wa nthawi* ino amene anadziwa+ nzeru imeneyi, chifukwa ngati anali kuidziwa sakanapachika+ Ambuye waulemereroyo.  Koma monga mmene Malemba amanenera: “Palibe munthu amene anaonapo kapena kumvapo kapenanso kuganizapo zimene Mulungu wakonzera omukonda.”+ 10  Pakuti mwa mzimu+ wake, Mulungu anaululira+ ifeyo zinthu zimenezi, chifukwa mzimu+ umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama+ za Mulungu. 11  Kodi ndi munthu uti amene angadziwe za munthu kupatulapo mzimu+ umene uli mwa munthuyo? Momwemonso, palibe amene akudziwa zinthu za Mulungu, kupatulapo mzimu+ wa Mulungu. 12  Tsopano sitinalandire mzimu+ wa dziko, koma mzimu+ wochokera kwa Mulungu, kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima.+ 13  Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu,+ koma ndi mawu amene mzimu+ watiphunzitsa, pamene tikuphatikiza zochitika zauzimu ndi mawu auzimu.+ 14  Koma munthu wokonda zinthu za m’dziko* salandira zinthu za mzimu wa Mulungu, chifukwa amaziona ngati zopusa ndipo sangathe kuzidziwa,+ chifukwa zimafuna kuzifufuza mwauzimu. 15  Komano munthu wauzimu+ amafufuza zinthu zonse, koma iye safufuzidwa+ ndi munthu aliyense. 16  Pakuti “ndani akudziwa maganizo a Yehova+ kuti amulangize?”+ Koma ifeyo tili ndi maganizo+ a Khristu.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “munthu wakuthupi.”