Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 15:1-58

15  Tsopano abale, ndikukuuzani uthenga wabwino+ umene ndinaulengeza kwa inu,+ umenenso munaulandira, ndiponso umene mwakhazikikamo.+  Mukupulumutsidwa+ ndi uthenga wabwino umenewo ngati mwaugwiritsitsa. Popanda kutero, ndiye kuti munakhala okhulupirira pachabe,+ malinga ndi mawu amene ndinakuuzani polengeza uthengawo kwa inu.  Mwa zinthu zofunika kwambiri zimene ndinakupatsirani zija, zimenenso ineyo ndinalandira,+ panali zonena kuti, Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba.+  Ndiponso kuti anaikidwa m’manda,+ kenako anaukitsidwa+ tsiku lachitatu,+ mogwirizana ndi Malemba.+  Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa,+ kenako kwa atumwi 12+ aja.  Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero,+ koma ena anagona mu imfa.  Kenako anaonekera kwa Yakobo,+ kenakonso kwa atumwi onse.+  Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine,+ ngati khanda lobadwa masiku asanakwane.  Ineyo ndine wamng’ono kwambiri+ mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza+ mpingo wa Mulungu. 10  Koma mwa kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu, ndili monga ndililimu. Ndipo kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anandisonyeza sikunapite pachabe,+ koma ndinagwira ntchito molimbika kuposa atumwi ena onse.+ Ngakhale zili choncho, si mwa ine ndekha ayi, koma kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumene kuli nane.+ 11  Komabe, kaya ndi ineyo kapena iwowo, zimene tikulalikira ndi zomwezo, zimenenso mwazikhulupirirazo.+ 12  Tsopano ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa,+ bwanji ena mwa inu akunena kuti akufa sadzaukitsidwa?+ 13  Chifukwa ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke.+ 14  Koma ngati Khristu sanauke, kulalikira kwathu n’kopanda pake, ndipo chikhulupiriro chathu n’chopanda pake.+ 15  Ndiponso, ndiye kuti ifenso takhala mboni zonama za Mulungu,+ chifukwa tachita umboni+ wonamizira Mulungu kuti anaukitsa Khristu+ pamene sanamuukitse, ngati akufa sadzaukadi.+ 16  Pakuti ngati akufa sadzauka, Khristunso sanauke. 17  Ndipo ngati Khristu sanauke, chikhulupiriro chanu chilibe ntchito ndipo mukadali m’machimo anu.+ 18  Ndiye kutinso anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu,+ kutha kwawo kunali komweko.+ 19  Ngati tayembekezera Khristu+ m’moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse. 20  Komabe, Khristu anaukitsidwa kwa akufa,+ n’kukhala chipatso choyambirira+ cha amene akugona mu imfa.+ 21  Popeza imfa+ inafika kudzera mwa munthu mmodzi, kuuka+ kwa akufa kunafikanso kudzera mwa munthu mmodzi. 22  Pakuti monga mwa Adamu onse akufa,+ momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa+ moyo. 23  Koma aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira,+ kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake. 24  Ndiyeno pa mapeto pake, adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake, atathetsa maboma onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse.+ 25  Pakuti ayenera kulamulira monga mfumu kufikira Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi+ ake. 26  Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.+ 27  Pakuti Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Koma pamene akunena kuti ‘waika zinthu zonse pansi pake,’+ n’zodziwikiratu kuti sakuphatikizapo amene anaika zinthu zonsezo pansi pa iye.+ 28  Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake,+ Mwanayonso adzadziika pansi pa amene+ anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.+ 29  Apo ayi, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzatani?+ Ngati akufa sadzauka,+ n’chifukwa chiyani anthuwo akubatizidwa+ kuti akhale akufa? 30  Kodi ifeyo tikuikiranji moyo wathu pachiswe nthawi zonse?+ 31  Tsiku ndi tsiku ndimakhala pa ngozi yoti ndikhoza kufa.+ Ndikukutsimikizirani zimenezi ndili wokondwera nanu,+ abale, kukondwera kumene ndili nako mwa Khristu Yesu Ambuye wathu. 32  Ngati ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso+ monga ena anachitira, ndinapindulapo chiyani? Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”+ 33  Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.+ 34  Dzukani ku tulo tanu+ kuti mukhale olungama ndipo musamachite tchimo, pakuti ena sadziwa Mulungu.+ Ndikulankhula zimenezi kuti muchite manyazi.+ 35  Ngakhale zili choncho, wina anganene kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa motani? Inde, kodi iwo adzauka ndi thupi lotani?”+ 36  Wopusa iwe! Chimene wabzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitafa kaye.+ 37  Ndipo chimene wafesa si mmera umene umakulawo, koma mbewu chabe,+ kaya ya tirigu kapena ina iliyonse. 38  Koma Mulungu amaipatsa thupi+ monga mwa kufuna kwake,+ ndipo mbewu iliyonse amaipatsa thupi lake. 39  Mnofu sukhala wa mtundu umodzi, koma pali mnofu wa munthu, ndipo pali wa nyama, palinso wa mbalame, ndi winanso wa nsomba.+ 40  Palinso matupi akumwamba,+ ndi matupi+ apadziko lapansi, koma ulemerero+ wa matupi akumwamba ndi wina, ndipo ulemerero wa matupi apadziko lapansi ndi winanso. 41  Ulemerero wa dzuwa+ ndi wosiyana ndi ulemerero wa mwezi,+ ndipo ulemerero wa nyenyezi ndi winanso. Ngakhale ulemerero wa nyenyezi+ ina, umasiyana ndi ulemerero wa inzake. 42  Ndi mmenenso zilili ndi kuuka kwa akufa.+ Thupi limafesedwa lili lokhoza kuwonongeka, limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka.+ 43  Limafesedwa lonyozeka,+ limaukitsidwa mu ulemerero.+ Limafesedwa lofooka,+ limaukitsidwa mu mphamvu.+ 44  Limafesedwa thupi lanyama,+ limaukitsidwa thupi lauzimu.+ Ngati pali thupi lanyama, palinso lauzimu. 45  Zinachita kulembedwa kuti: “Munthu woyambirira, Adamu, anakhala munthu wamoyo.”+ Adamu womalizira anakhala mzimu+ wopatsa moyo.+ 46  Ngakhale zili choncho, choyambacho si chauzimu ayi koma chamnofu. Kenako panabwera chauzimu.+ 47  Munthu woyambayo anachokera padziko lapansi ndipo anapangidwa ndi fumbi.+ Wachiwiriyo anachokera kumwamba.+ 48  Mmene wopangidwa ndi fumbiyo alili,+ ndi mmenenso opangidwa ndi fumbiwo alili. Ndipo mmene wakumwambayo alili,+ ndi mmenenso akumwambawo alili.+ 49  Ndiponso, monga tilili m’chifaniziro+ cha wopangidwa ndi fumbi uja, tidzakhalanso m’chifaniziro+ cha wakumwambayo. 50  Koma abale, ndikunenetsa kuti mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu.+ Komanso chowonongeka sichingalandire kusawonongeka.+ 51  Tamverani! Ndikukuuzani chinsinsi chopatulika: Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasandulika,+ 52  m’kamphindi, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza. Pakuti lipengalo+ lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osakhoza kuwonongeka, ndipo tidzasandulika. 53  Pakuti chokhoza kuwonongekachi chidzavala kusawonongeka,+ ndipo chokhoza kufachi+ chidzavala kusafa. 54  Koma chokhoza kuwonongekachi chikadzavala kusawonongeka, ndipo chokhoza kufachi chikadzavala kusafa, pamenepo adzakwaniritsidwa mawu amene analembedwa kuti: “Imfa+ yamezedwa kwamuyaya.”+ 55  “Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?”+ 56  Mphamvu+ imene imabala imfa ndiyo uchimo, koma mphamvu ya uchimo ndi Chilamulo.+ 57  Koma Mulungu ayamikike, pakuti amatithandiza kuti tipambane kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 58  Choncho abale anga okondedwa, khalani olimba,+ osasunthika, okhala ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye,+ podziwa kuti zonse zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 8.