Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1 Akorinto 12:1-31

12  Tsopano abale, ponena za mphatso zauzimu,+ sindikufuna kuti mukhale osadziwa.  Mukudziwa kuti pamene munali a mitundu ina,+ munali kutsogoleredwa m’njira zosiyanasiyana ku mafano+ osalankhula.+  Choncho ndikufuna mudziwe kuti palibe wolankhula mwa mzimu wa Mulungu amene anganene kuti: “Yesu ndi wotembereredwa!”+ Palibenso amene anganene popanda mzimu woyera kuti: “Yesu ndiye Ambuye!”+  Tsopano mphatso zilipo zamitundumitundu,+ koma mzimu ndi umodzi,+  ndipo pali mautumiki osiyanasiyana,+ koma Ambuye ndi mmodzi.+  Palinso ntchito zosiyanasiyana,+ koma Mulungu amene amachita ntchito zonsezo mwa anthu onse+ ndi mmodzi.+  Tsopano ntchito za mzimu zimapatsidwa kwa munthu aliyense pa cholinga chopindulitsa.+  Mwachitsanzo, mwa mzimu wina amapatsidwa mawu anzeru,+ ndipo wina amapatsidwa mawu ozindikira+ mwa mzimu womwewo.  Mwa mzimu womwewonso wina amapatsidwa chikhulupiriro,+ wina mphatso za kuchiritsa.+ 10  Winanso amapatsidwa mphatso yochita ntchito zamphamvu,+ wina kunenera,+ wina kuzindikira+ mawu ouziridwa,+ wina kulankhula malilime osiyanasiyana,+ ndiponso wina kumasulira+ malilime. 11  Koma ntchito zonsezi, mzimu umodzimodziwo+ ndiwo umazichita, pogawira+ aliyense payekha malinga ndi chifuniro cha mzimuwo.+ 12  Pakuti mofanana ndi thupi lomwe ndi limodzi koma lili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonse za thupi, ngakhale ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi,+ ndi mmenenso Khristu alili.+ 13  Pakuti ndi mzimu umodzi, tonsefe tinabatizidwa+ kukhala thupi limodzi, kaya tikhale Ayuda kapena Agiriki, akapolo kapena mfulu, ndipo tonsefe tinamwetsedwa+ mzimu umodzi. 14  Ndithudi, thupi si chiwalo chimodzi, koma zambiri.+ 15  Ngati phazi linganene kuti: “Popeza sindine dzanja, sindili mbali ya thupi,” chimenecho si chifukwa chopangitsa phazi kusakhala mbali ya thupi.+ 16  Ndipo ngati khutu linganene kuti: “Popeza sindine diso, sindili mbali ya thupi,” chimenecho si chifukwa chopangitsa khutu kusakhala mbali ya thupi.+ 17  Thupi lonse likanakhala diso, kodi mphamvu ya kumva ikanakhala kuti? Thupi lonse likanakhala khutu, kodi bwenzi tikumanunkhiza ndi chiyani? 18  Koma Mulungu anaika ziwalo m’thupi, chilichonse m’malo ake, mmene iye anafunira.+ 19  Zonsezo zikanakhala chiwalo chimodzi,+ nanga thupi likanakhala kuti? 20  M’malomwake, ziwalozo n’zambiri,+ koma thupi ndi limodzi. 21  Diso silingauze dzanja kuti: “Ndilibe nawe ntchito,” kapenanso, mutu sungauze mapazi kuti: “Ndilibe nanu ntchito.” 22  Koma ziwalo za thupi zimene zimaoneka ngati zofooka+ ndizo zofunika. 23  Ndipo mbali za thupi zimene timaziona ngati zosalemekezeka kwambiri, n’zimene timazipatsa ulemu wochuluka,+ chotero mbali zathu zosaoneka bwino zimaoneka bwino kwambiri, 24  pamene mbali zathu zooneka bwino kale sizifunikira kalikonse. Ngakhale zili choncho, Mulungu analumikiza bwino thupi lonse, kuika ulemu wochuluka pa mbali imene inalibe ulemuwo, 25  kuti thupi lisakhale logawanika, koma ziwalo zake zisamalirane mofanana.+ 26  Ndipo chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikira nacho limodzi,+ komanso chiwalo chimodzi chikalemekezedwa,+ ziwalo zina zonse zimasangalalira nacho limodzi.+ 27  Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.+ 28  Mulungu waika ziwalo zosiyanasiyana mumpingo.+ Choyamba atumwi,+ chachiwiri aneneri,+ chachitatu aphunzitsi,+ kenako ntchito zamphamvu,+ mphatso za kuchiritsa,+ utumiki wothandiza anthu,+ luso loyendetsa zinthu,+ ndi malilime osiyanasiyana.+ 29  Sikuti onse angakhale atumwi, angatero ngati? Sikuti onse angakhale aneneri, angatero ngati? Sikuti onse angakhale aphunzitsi, angatero ngati? Si onse amachita ntchito zamphamvu, ndi onse ngati? 30  Si onse amene ali ndi mphatso za kuchiritsa, ndi onse ngati? Si onse amalankhula malilime,+ ndi onse ngati? Sikuti onse ndi omasulira,+ ndi onse ngati? 31  M’malomwake, pitirizani kufunafuna mwachangu mphatso zazikulu.+ Komabe, ine ndikuonetsani njira yopambana.+

Mawu a M'munsi