Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 10:1-33

10  Tsopano sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale, kuti makolo athu akale, onse anali pansi pa mtambo ndipo onse anawoloka nyanja.  Onse anabatizidwa mwa Mose,+ kudzera mwa mtambo ndi mwa nyanja.  Ndiponso, onse anadya chakudya chimodzimodzi chauzimu,  ndipo onse anamwa chakumwa chimodzimodzi chauzimu. Pakuti anali kumwa pathanthwe lauzimu limene linali kuwatsatira, ndipo thanthwelo+ linatanthauza Khristu.+  Ngakhale zinali choncho, ambiri a iwo Mulungu sanakondwere nawo, ndipo anathana nawo m’chipululu.  Tsopano zinthu zimenezi zinakhala zitsanzo kwa ife, kuti ifenso tisakhale anthu olakalaka zinthu zoipa ngati mmene iwo anachitira.  Ndipo tisapembedze mafano, mmene ena mwa iwo anachitira, monga mmene Malemba amanenera kuti: “Anthu anakhala pansi ndi kudya ndiponso kumwa. Kenako anaimirira n’kuyamba kusangalala.”  Tisamachite dama, mmene ena mwa iwo anachitira dama, n’kufa 23,000 tsiku limodzi.  Kapena tisamuyese Yehova, mmene ena mwa iwo anamuyesera, n’kuwonongeka polumidwa ndi njoka. 10  Tisakhalenso ong’ung’udza, mmene ena mwa iwo anang’ung’udzira, wowonongayo n’kuwawononga onsewo. 11  Tsopano zinthu zimenezi zinali kuwagwera monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze+ ifeyo amene mapeto a nthawi* zino atifikira.+ 12  N’chifukwa chake amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.+ 13  Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwera anthu ena.+ Koma Mulungu ndi wokhulupirika+ ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire,+ koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira. 14  Ndiye chifukwa chake, okondedwa anga, thawani+ kupembedza mafano. 15  Ndikulankhula nanu ngati anthu ozindikira.+ Dziwani nokha zimene ndikunena. 16  Kodi kapu+ ya dalitso imene timadalitsa, sitanthauza kugawana magazi a Khristu?+ Kodi mkate umene timanyema,+ sutanthauza kugawana thupi la Khristu? 17  Popeza pali mkate umodzi, ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri,+ ndife thupi limodzi,+ pakuti tonse tikudya nawo mkate umodziwo.+ 18  Taganizirani zochitika za Isiraeli wakuthupi:+ Kodi amene amadyako zoperekedwa nsembe sindiye kuti akugawana ndi guwa lansembe? 19  Ndiye ndinene chiyani? Kuti choperekedwa nsembe kwa fano chili kanthu, kapena kuti fanolo ndi kanthu?+ 20  Ayi, koma ndikunena kuti zinthu zimene mitundu ina imapereka nsembe imazipereka kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti mukhale ogawana ndi ziwanda.+ 21  Sizingatheke kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova*+ komanso za m’kapu ya ziwanda. Sizingatheke kuti muzidya “patebulo la Yehova”+ komanso patebulo la ziwanda. 22  Kapena “kodi tikufuna kuputa nsanje ya Yehova”? Kodi mphamvu zathu zingafanane ndi zake?+ 23  Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka,+ koma si zonse zimene zili zolimbikitsa.+ 24  Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi,+ koma zopindulitsanso wina.+ 25  Chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muzidya+ popanda kufunsa mafunso, poopera chikumbumtima+ chanu, 26  chifukwa “dziko lapansi ndi zonse za mmenemo+ ndi za Yehova.” 27  Ngati wina mwa osakhulupirira wakuitanani ndipo mwapita, kadyeni zonse zimene wakupatsani,+ popanda kufunsa mafunso poopera chikumbumtima chanu.+ 28  Koma wina akakuuzani kuti: “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo poopera amene wakuuzaniyo ndiponso poopera chikumbumtima.+ 29  Sindikunena “chikumbumtima” chako koma cha munthu winayo. N’chifukwa chiyani ufulu wanga ukulamulidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina?+ 30  Ngati ndikudya chakudyacho nditayamika Mulungu, kodi ndinyozedwe pa chinthu chimene ndayamikira?+ 31  Ndiye chifukwa chake, kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.+ 32  Pewani kukhala okhumudwitsa+ kwa Ayuda, ngakhalenso kwa Agiriki, ndi kwa mpingo wa Mulungu, 33  monga mmene ineyo ndikukondweretsera anthu onse m’zinthu zonse.+ Sikuti ndikungofuna zopindulitsa ine ndekha ayi,+ koma zopindulitsa anthu ambiri, kuti apulumutsidwe.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 2.