Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

1 Akorinto 1:1-31

1  Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu,+ pamodzi ndi Sositene+ m’bale wathu,  ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto,+ kwa inu amene mwayeretsedwa+ mwa Khristu Yesu, amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera,+ pamodzi ndi onse amene kulikonse akuitana pa dzina+ la Ambuye wathu, Yesu Khristu, Ambuye wawo ndiponso wathu.+  Kukoma mtima kwakukulu+ ndi mtendere+ zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu+ zikhale ndi inu.  Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu,+  kuti mwa iye mwakhala olemera+ m’zinthu zonse, pokhala ndi mphamvu zonse za kulankhula ndi kudziwa zinthu zonse,+  popeza kuti umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati pa inu,  moti palibe mphatso+ imene ikuperewera mwa inu, pamene mukudikira mwachidwi kuululidwa+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.  Mulungu adzakulimbitsani+ mpaka pa mapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani+ m’tsiku+ la Ambuye wathu Yesu Khristu.+  Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale oyanjana+ ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+ 10  Tsopano ndikukudandaulirani+ abale, m’dzina+ la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndi kuti pasakhale magawano+ pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana+ pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ 11  Pakuti a m’banja la Kuloe andiuza+ za inu, abale anga, kuti pali magawano pakati panu. 12  Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu amanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena amati, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso amati “Ine ndine wa Kefa,” pamene ena amati, “Ine ndine wa Khristu.” 13  Choncho Khristu wakhala wogawanika.+ Paulo sanapachikidwe chifukwa cha inu, anatero kodi? Kapena kodi munabatizidwa+ m’dzina la Paulo? 14  Ndikusangalala kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+ 15  moti wina sanganene kuti munabatizidwa m’dzina langa. 16  Inde, ndinabatizanso banja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense. 17  Pakuti Khristu sananditume+ kukabatiza anthu, koma kukalengeza uthenga wabwino, osati mwa nzeru za kulankhula,+ kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda pake. 18  Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo ndi chinthu chopusa+ kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa+ ndi mphamvu ya Mulungu.+ 19  Pakuti Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru zonse za anthu anzeru,+ ndipo ndidzakankhira pambali+ kuchenjera kwa anthu ophunzira.”+ 20  Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi ali kuti?+ Katswiri wa mtsutso+ wa nthawi* ino ali kuti?+ Kodi Mulungu sanapange nzeru za dzikoli kukhala zopusa?+ 21  Pakuti ngakhale kuti dziko mwa nzeru zake+ silinathe kumudziwa Mulungu,+ kunamukomera Mulungu mwa nzeru zake kupulumutsa okhulupirira kudzera mu nkhani yopusayo,+ imene ikulalikidwa. 22  Pakuti Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru,+ 23  koma ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa.+ Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa+ ndipo kwa mitundu ina ndi kupusa.+ 24  Ngakhale zili choncho, kwa amene anaitanidwa, Ayuda ndiponso Agiriki, Khristu ndiye mphamvu+ ya Mulungu ndi nzeru+ za Mulungu. 25  Pakuti chinthu chopusa cha Mulungu ndi chanzeru kuposa anthu, ndipo chinthu chofooka cha Mulungu n’champhamvu kuposa anthu.+ 26  Mukuona mmene anakuitanirani, abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa,+ si ambiri amphamvu+ amene anaitanidwa, si ambiri a m’mabanja achifumu. 27  Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko+ kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi+ zinthu zamphamvu. 28  Mulungu anasankha zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe,+ kuti athetse+ mphamvu zinthu zimene zilipo, 29  kuti pasapezeke munthu wodzitama+ pamaso pa Mulungu. 30  Koma inu muli ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru+ za Mulungu ndiponso chilungamo+ cha Mulungu. Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+ 31  kuti zikhale monga Malemba amanenera kuti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 9.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.