Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhululukirana

Tizikhululukirana
ONANI

Pangani Dawunilodi:

 1. 1. Munali n’zolinga zabwino.

  Mumafuna kundithandizanso.

  Koma mawu andilasa mtima.

  Komabe n’kaganizira

  Sichinali cholinga.

  (KOLASI)

  Dzuwatu lisanalowe,

  Tiyesetse tikambirane.

  Zomwe talakwirana,

  Tikhululuke.

  Ubale wathu titeteze.

 2. 2. Kumvetsetsanadi ndikovuta.

  Wina ‘nganene zokhumudwitsa.

  Mpofunika kukhululuka,

  Ndipo mudzazindikira;

  Mwachita zofunika.

  (KOLASI)

  Dzuwatu lisanalowe,

  Tiyesetse tikambirane.

  Zomwe talakwirana,

  Tikhululuke.

  Ubale wathu titeteze.

  (VESI LOKOMETSERA)

  Mawu ndi zochita zisasokoneze ubale wathuwu.

  Khululuka, iwala zonse.

  Udzasonyeza chikondi.

  (KOLASI )

  Dzuwatu lisanalowe,

  Tiyesetse tikambirane.

  Zomwe talakwirana,

  Tikhululuke.

  Zichokere mumtimamu.

  Mwachikondi tikhululukirane.