Nyimbo Zathu

Nyimbo zosangalatsa zosonyeza kuyamikira chuma chathu chauzimu.

Kungomwetulira

Kumwetulira kungatithandize muutumiki komanso pa moyo wathu.

Yehova Wakulandira

Mzimu woyera wa Mulungu ungakuthandizeni kuti mubwerere kwa iye.

Kusangalala ndi Misonkhano

Tikapita ku msonkhano, timasangalala ndi mgwirizano komanso chikondi chomwe abale padziko lonse ali nacho.

Ganizira Nthawiyo

Tikuyembekezera nthawi imene zinthu zonse zidzakhale zabwino.

Tiyendebe

Tipitirizebe kuyenda ndi gulu la Yehova lomwe likupita patsogolo

Madalitso Ophunzira Chinenero China

Kodi mungapeze madalitso otani chifukwa chophunzira chilankhulo china?

Musathamange

Utumiki wathu komanso zinthu zina pamoyo wathu kawirikawiri zimayenda bwino tikamachita zinthu mosapupuluma.

Zimene Timasankha

Ndi nzeru kumaganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire utumiki wathu komanso anthu ena.

Tizikhululukirana

Tiziyesetsa kutsanzira Yehova n’kumakhululukira ena.

Dziko Latsopano Lili Pafupi

Kuyembekezera mwachidwi Paradaiso amene akubwerayu kungatithandize kuti tipirire.

Muziphunzira Kuti Mukhale Olimba

Achinyamata akhoza kukhala olimba mwauzimu ngati atamaphunzira Mawu a Mulungu paokha.

Mawu Anu Adzakhala Mpaka Kalekale

Tiyenera kutamanda Yehova chifukwa choti wasunga Mawu ake kuti anthu aziwagwiritsa ntchito

Zidzatiyendera Tikamapemphera

Kodi tingatani tikakumana ndi mavuto?

Yehova Amandithandiza Kukonza Tsogolo Langa

Tsiku ndi tsiku tizisankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova.

Ndimasunga Malamulo Anu

Zolankhula ndi zochita zathu zizisonyeza kuti timakonda Yehova.

Ndidzadzukanso

Tsanzirani munthu yemwe poyamba anali wakhama potumikira Yehova ndipo akupezanso mphamvu n’kubwerera atakumbukira chikondi chimene mpingo unkamusonyeza.

Ntchito Zanu N’zodabwitsa

Kusangalala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Yehova!

Mwana Wanga Wamkazi Wapadera

Pamene zaka zikudutsa, bambo akuona mwana wake wamkazi akukula ndi kuyamba kuona choonadi kuti ndichakechake.

Tisachedwe

Monga atumiki a Yehova, kuwonjezera zochita mu utumiki wathu m’njira iliyonse kungatibweretsere chimwemwe chochuluka.

Yang’ane

Gwiritsani ntchito bwino nthawi yocheza ndi abale ndi alongo.

Chilengedwe Chanu Chimandidabwitsa

Ntchito za manja a Yehova zimatidabwitsa ndipo zimatichititsa kumuimbira.

Zinthu Zofunika

Tiyenera kumapeza nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri—kupemphera, kuphunzira, ndi kudzipereka kwa Mulungu.

Malo Amene Adzachititsa Kuti Mulemekezedwe

Ndife osangalala kupereka kwa Yehova malo amene adzachititsa kuti dzina lake lalikulu lilemekezedwe.

Ndikukhulupirireni

Kuphunzira mawu a Mulungu ndi kuganizira zimene tikuphunzirazo kungatithandize kupirira mavuto amene tikukumana nawo pa moyo.

Ndikusintha

Kodi mukufunitsitsa kusintha mmene mumachitira zinthu pa utumiki wanu?

Sangandisiye

Yehova Mulungu wathu sangatisiye!

Kukonda Abale

Palibe gulu lina lililonse padzikoli limene lingafanane ndi Mboni za Yehova pa nkhani yothandizana.

Kufufuza

Omwe akufunitsitsa kudziwa Mulungu angafunike kuchita khama pomwe akufufuza za iye.

Mabwenzi Enieni

Kodi tingapeze kuti mabwenzi enieni?

Undidalire

Pamavuto ndi pamtendere, tingadalire mabwenzi enieni.

Ndidzakupatsani Zonse Zomwe Ndingathe

Yehova ndi woyeneradi kumutumikira ndi mtima wathu wonse.

Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima

Yehova angatithandize kuti tipirire molimba mtima mayesero alionse amene tingakumane nawo.