Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Nyimbo 138

Inu Ndinu Yehova

Inu Ndinu Yehova

(Salimo 83:18)

 1. Mulungu woona

  Wachilengedwe chonse

  Mulungu wamuyaya

  Ndinudi Yehova.

  Ndifetu amwayi

  Kukhala anthu anu

  Tilalika za inu,

  Ku mitundu yonse.

  (KOLASI)

  Yehova, Yehova,

  M’lungu ndinu nokha

  Kumwambako ndi padziko.

  Palibenso wina

  Ndinudi Wamphamvuyonse

  Onsetu adziwe

  Yehova, Yehova,

  M’lungu wathu ndinu nokha.

 2. Tingathe kukhala,

  Chilichonse mwasankha.

  Tigwire ntchito yanu

  Ndinudi Yehova

  Mwatipatsa dzina

  Tikhale Mboni zanu

  Uwu ndi mwayi wathu

  Tikutamandani

  (KOLASI)

  Yehova, Yehova,

  M’lungu ndinu nokha

  Kumwambako ndi padziko.

  Palibenso wina

  Ndinudi Wamphamvuyonse

  Onsetu adziwe

  Yehova, Yehova,

  M’lungu wathu ndinu nokha.