Imbirani Yehova—Nyimbo Zatsopano

Sangalalani ndi nyimbo zatsopano zomwe cholinga chake ndi kutamanda komanso kulambira Yehova Mulungu. Pangani dawunilodi nyimbo komanso mawu ake ndipo yesetsani kuti muziphunzire.

NYIMBO 136

Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere

Nyimbo yotamanda Yehova Mulungu chifukwa chodziwa kuti Ufumu wake ukulamulira ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu.

NYIMBO 137

Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima

Imbani nawo nyimboyi, yopempha Yehova kuti atithandize kukhala olimba mtima tikamalalikira za dzina lake.

NYIMBO 138

Inu Ndinu Yehova

Imbani nyimbo ya Ufumuyi potamanda dzina loyera la Yehova.

NYIMBO 139

Athandizeni Kukhala Olimba

Pemphero lopempha Yehova kuti ateteze ophunzira Baibulo komanso awathandize kukhala okhulupirika mpaka mapeto.

NYIMBO NAMBALA 140

Moyo wa Mpainiya

Sonyezani kukhulupirika kwanu kwa Yehova komanso kuti mumasangalala ndi ntchito yolalikira ndipo mumaikonda.

NYIMBO NAMBALA 141

Kufufuza Anthu Okonda Mtendere

Nyimbo yosangalatsa yonena za chikondi chathu pa anthu komanso ntchito yathu yofufuza mwakhama nkhosa zamtengo wapatali za Mulungu.

NYIMBO NAMBALA 142

Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse

Nyimbo yonena za ubwino wa Yehova komanso mbali yathu pothandiza anthu a mitundu yonse kuti akhale mabwenzi a Yehova.

NYIMBO 143

Kuwala M’dziko Lamdima

Uthenga wa Mulungu, wawala ngati dzuwa.

NYIMBO 144

Akamvera Adzapeza Moyo

Tiyenera kulalikira uthenga wa Mulungu nthawi isanathe.

NYIMBO 145

Kukonzekera Kupita Kolalikira

N zosavuta kupitiriza kugona, koma tingapeze mphamvu kuti tisafooke.

NYIMBO 146

Munachitira Ine Amene

Yesu amayamikira chikondi chimene timasonyeza abale ake odzozedwa ndipo amaona kuti tachitiranso iyeyo.

NYIMBO 147

Chuma Chapadera

Yehova amakonda ana ake odzozedwa ndipo iwo amakonda kuchita chifuniro chake.

NYIMBO 148

Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

Tikuthokoza Yehova chifukwa chotipatsa mphatso yamtengo wapatali. Imapatsa anthu onse.

NYIMBO 149

Tikukuthokozani Chifukwa cha Dipo

Mphatso yamtengo wapatali, Yesu analolera kupereka moyo wake monga nsembe, zimatichititsa kuthokoza Yehova mpaka kalekale.

NYIMBO 150

Timadzipereka

Muzisonyeza kuti mumafunitsitsa kutumikira Yehova pogwira ntchito iliyonse yomwe angakupatseni.

NYIMBO 151

Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera

Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yehova adzatenga abale ake a Khristu n’kupita nawo kumwamba kuti adzamenye nkhondo ndi kulandira mphoto limodzi ndi Khristu.

NYIMBO 152

Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

Tikakhala ndi nkhawa, Mulungu akhoza kutilimbikitsa, kutipatsa chiyembekezo komanso chidaliro.

NYIMBO 153

Kodi Mumamva Bwanji?

Kodi mumamva bwanji mukayesetsa kufufuza anthu a mtima wabwino?

NYIMBO 154

Tipirirabe Mpaka Mapeto

Nyimbo yotithandiza kupirira mavuto ndi kutumikira Yehova mokhulupirika mmene tingathere.