NYIMBO 98
Malemba Anauziridwa Ndi Mulungu
-
1. Mawu a M’lungu ndi nyale,
Amatiunikira.
Tikawagwiritsa ntchito
Tizikonda choonadi.
-
2. Mawu ouziridwawa
Amatiphunzitsadi.
Amatha kukonza zinthu
Ndiponso kutilangiza.
-
3. Mawu a Mulungu wathu
Amatitsogolera.
Ngati timawawerenga
Zizitiyendera bwino.
(Onaninso Sal. 119:105; Miy. 4:13.)