Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 69

Pitirizani Kulalikira za Ufumu

Pitirizani Kulalikira za Ufumu

(2 Timoteyo 4:5)

  1. 1. Pitani patsogolo ndithu

    Polalikira konse.

    Muthandize anthu ofatsa,

    Akonde choonadi.

    Ndi mwayidi kutumikira;

    Tikonde kulalikira.

    Chitirani umboni M’lungu;

    Ndi dzina lake loyera.

    (KOLASI)

    Pitirizani kulalikira

    padziko lonse.

    Pitirizani kukhala

    okhulupirikabe.

  2. 2. Tipite patsogolo tonse,

    Amuna ndi akazi.

    Odzozedwa ndi nkhosa zina

    Tisasiye cho’nadi.

    Ndi kofunika kuti anthu

    Amve uthenga wabwino.

    Yehova atipatsa mphamvu;

    Ndipo sitiopa kanthu!

    (KOLASI)

    Pitirizani kulalikira

    padziko lonse.

    Pitirizani kukhala

    okhulupirikabe.